Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Marko 10:23 - Buku Lopatulika

23 Ndipo Yesu anaunguzaunguza, nanena ndi ophunzira ake, Okhala nacho chuma adzalowa mu Ufumu wa Mulungu ndi kuvuta nanga!

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

23 Ndipo Yesu anaunguzaunguza, nanena ndi ophunzira ake, Okhala nacho chuma adzalowa mu Ufumu wa Mulungu ndi kuvuta nanga!

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

23 Yesu adayang'ana ophunzira ake amene adaamzungulira naŵauza kuti, “Nkwapatali kwambiri kwa anthu achuma kuti akaloŵe mu Ufumu wa Mulungu.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

23 Yesu anayangʼanayangʼana ndipo anati kwa ophunzira ake, “Nʼkovutadi kuti achuma akalowe mu ufumu wa Mulungu!”

Onani mutuwo Koperani




Marko 10:23
13 Mawu Ofanana  

Ngati ndayesa golide chiyembekezo changa, ndi kunena ndi golide woyengetsa, ndiwe chikhazikitso changa;


nati, Indetu ndinena kwa inu, Ngati simutembenuka, nimukhala monga tianato, simudzalowa konse mu Ufumu wa Kumwamba.


Ndithu ndinena ndi inu, Munthu aliyense wosalandira Ufumu wa Mulungu ngati kamwana, sadzalowamo konse.


Koma nkhope yake inagwa pa mau awa, ndipo anachoka iye wachisoni; pakuti anali mwini chuma chambiri.


Ndipo m'mene anawaunguza ndi mkwiyo, ndi kumva chisoni chifukwa cha kuuma kwa mitima yao, ananena kwa munthuyo, Tambasula dzanja lako. Ndipo analitambasula; ndipo linachira dzanja lake.


Ndipo Iye anaunguzaunguza kumuona iye amene adachita ichi.


Ndipo Yesu pomuona iye anati, Ha! Nkuvutika nanga kwa anthu eni chuma kulowa Ufumu wa Mulungu!


Yesu anayankha, Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, Ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi Mzimu, sangathe kulowa ufumu wa Mulungu.


Pakuti penyani maitanidwe anu, abale, kuti saitanidwa ambiri anzeru, monga mwa thupi; ambiri amphamvu, mfulu zambiri, iai;


Mverani, abale anga okondedwa; kodi Mulungu sanasankhe osauka a dziko lapansi akhale olemera ndi chikhulupiriro, ndi olowa nyumba a ufumu umene adaulonjeza kwa iwo akumkonda Iye?


Akazi achigololo inu, kodi simudziwa kuti ubwenzi wa dziko lapansi uli udani ndi Mulungu? Potero, iye amene afuna kukhala bwenzi la dziko lapansi adziika mdani wa Mulungu.


pakuti kotero kudzaonjezedwa kwa inu kolemerera khomo lakulowa ufumu wosatha wa Ambuye wathu ndi Mpulumutsi Yesu Khristu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa