Miyambo 2 - Buku LopatulikaUkoma ndi phindu lake la Nzeru 1 Mwananga, ukalandira mau anga, ndi kusunga malamulo anga; 2 kutcherera makutu ako kunzeru, kulozetsa mtima wako kukuzindikira; 3 ukaitananso luntha, ndi kufuulira kuti ukazindikire; 4 ukaifunafuna ngati siliva, ndi kuipwaira ngati chuma chobisika; 5 pompo udzazindikira kuopa Yehova ndi kumdziwadi Mulungu. 6 Pakuti Yehova apatsa nzeru; kudziwa ndi kuzindikira kutuluka m'kamwa mwake. 7 Iye asungira oongoka mtima nzeru yeniyeni; ndiye chikopa cha oyenda molunjika; 8 kuti atchinjirize njira za chiweruzo, nadikire khwalala la opatulidwa ake. 9 Pamenepo udzazindikira chilungamo ndi chiweruzo, zolunjika ndi mayendedwe onse abwino. 10 Pakuti nzeru idzalowa m'mtima mwako, moyo wako udzakondwera ndi kudziwa, 11 kulingalira kudzakudikira, kuzindikira kudzakutchinjiriza; 12 kukupulumutsa kunjira yoipa, kwa anthu onena zokhota; 13 akusiya mayendedwe olungama, akayende m'njira za mdima; 14 omwe asangalala pochita zoipa, nakondwera ndi zokhota zoipa; 15 amene apotoza njira zao, nakhotetsa mayendedwe ao. 16 Nzeru idzakupulumutsa kwa mkazi wachiwerewere, kwa mkazi wachilendo wosyasyalika ndi mau ake; 17 wosiya bwenzi la ubwana wake, naiwala chipangano cha Mulungu wake. 18 Nyumba yake itsikira kuimfa, ndi mayendedwe ake kwa akufa; 19 onse akunka kwa iye sabweranso, safika kunjira za moyo; 20 nzeru idzakuyendetsa m'njira ya anthu abwino, kuti usunge mayendedwe a olungama. 21 Pakuti oongoka mtima adzakhala m'dziko, angwiro nadzatsalamo. 22 Koma oipa adzalikhidwa m'dziko, achiwembu adzazulidwamo. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi