Ndikakhala ndi mtendere wa Mulungu mumtima mwanga, palibe malo a maganizo oipa. Ukali uli ndi mphamvu yowononga kulankhulana, kusokoneza ubale, komanso kusokoneza chimwemwe ndi thanzi la anthu ambiri.
N’zomvetsa chisoni kuti nthawi zambiri anthufe timapeza zifukwa zotsimikizira ukali wathu m’malo motenga udindo. Komabe, tingathe kuugonjetsa ukaliwu motsatira mfundo za m’Baibulo, poona Mulungu pakati pa mayesero, kupemphera nthawi zonse, ndi kudzipereka kwa Iye.
Mawu a Mulungu amatilimbikitsa kuti tione mayesero osiyanasiyana ngati chifukwa chachikulu cha chimwemwe, podziwa kuti mayesero a chikhulupiriro chathu amabala chipiriro. Ndipo chipirirocho chizigwira ntchito yake yonse mwa ife, kuti tikule bwino m’zonse, osasowa kanthu kalili konse (Yakobo 1:2-4).
Kwiyani, koma musachimwe; dzuwa lisalowe muli chikwiyire, ndiponso musampatse malo mdierekezi.
Chiwawo chonse, ndi kupsa mtima, ndi mkwiyo, ndi chiwawa, ndi mwano zichotsedwe kwa inu, ndiponso choipa chonse.
Chiwawo chonse, ndi kupsa mtima, ndi mkwiyo, ndi chiwawa, ndi mwano zichotsedwe kwa inu, ndiponso choipa chonse. Koma mukhalirane okoma wina ndi mnzake, a mtima wachifundo, akukhululukirana nokha, monganso Mulungu mwa Khristu anakhululukira inu.
Mudziwa, abale anga okondedwa, kuti munthu aliyense akhale wotchera khutu, wodekha polankhula, wodekha pakupsa mtima. Muchiyese chimwemwe chokha, abale anga, m'mene mukugwa m'mayesero a mitundumitundu; Pakuti mkwiyo wa munthu suchita chilungamo cha Mulungu.
Chifukwa chake chotsani zopweteka m'mtima mwako, nulekanitse zoipa ndi thupi lako; pakuti ubwana ndi unyamata ngwa chabe.
Koma mafunso opusa ndi opanda malango upewe, podziwa kuti abala ndeu. Ndipo kapolo wa Ambuye sayenera kuchita ndeu, komatu akhale woyenera, waulere pa onse, wodziwa kuphunzitsa, woleza,
Kulingalira kwa munthu kuchedwetsa mkwiyo; ulemerero wake uli wakuti akhululukire cholakwa.
Usayanjane ndi munthu wokwiya msanga; ngakhale kupita ndi mwamuna waukali; kuti ungaphunzire mayendedwe ake, ndi kutengera moyo wako msampha.
koma Ine ndinena kwa inu, kuti yense wokwiyira mbale wake wopanda chifukwa adzakhala wopalamula mlandu; ndipo amene adzanena ndi mbale wake, Wopanda pake iwe, adzakhala wopalamula mlandu wa akulu: koma amene adzati, Chitsiru iwe: adzakhala wopalamula Gehena wamoto.
Pakuti ngati mukhululukira anthu zolakwa zao adzakhululukira inunso Atate wanu wa Kumwamba. Koma ngati simukhululukira anthu zolakwa zao, Atate wanunso sadzakhululukira zolakwa zanu.
Chifukwa chake zinthu zilizonse mukafuna kuti anthu achitire inu, inunso muwachitire iwo zotero; pakuti icho ndicho chilamulo ndi aneneri.
Pamenepo Petro anadza, nati kwa Iye, Ambuye, mbale wanga adzandilakwira kangati, ndipo ine ndidzamkhululukira iye? Kufikira kasanu ndi kawiri kodi? Yesu ananena kwa iye, Sindinena kwa iwe kufikira kasanu ndi kawiri, koma kufikira makumi asanu ndi awiri kubwerezedwa kasanu ndi kawiri.
Ndipo pamene muimirira ndi kupemphera, khululukirani, ngati munthu wakulakwirani kanthu; kuti Atate wanunso ali Kumwamba akhululukire inu zolakwa zanu.
Koma ndinena kwa inu akumva, Kondanani nao adani anu; chitirani zabwino iwo akuda inu, dalitsani iwo akutemberera inu, pemphererani iwo akuchitira inu chipongwe.
Musabwezere munthu aliyense choipa chosinthana ndi choipa. Ganiziranitu zinthu za ulemu pamaso pa anthu onse. Ngati nkutheka, monga momwe mukhoza, khalani ndi mtendere ndi anthu onse. Musabwezere choipa, okondedwa, koma patukani pamkwiyo; pakuti kwalembedwa, Kubwezera kuli kwanga, Ine ndidzabwezera, ati Ambuye.
Chikondi chikhala chilezere, chili chokoma mtima; chikondi sichidukidwa; chikondi sichidziwa kudzitamanda, sichidzikuza, sichichita zosayenera, sichitsata za mwini yekha, sichipsa mtima, sichilingirira zoipa;
Pakuti pakuyendayenda m'thupi, sitichita nkhondo monga mwa thupi, (pakuti zida za nkhondo yathu sizili za thupi, koma zamphamvu mwa Mulungu zakupasula malinga); ndi kugwetsa matsutsano, ndi chokwezeka chonse chimene chidzikweza pokana chidziwitso cha Mulungu, ndi kugonjetsa ganizo lonse kukumvera kwa Khristu;
Ndipo ntchito za thupi zionekera, ndizo dama, chodetsa, kukhumba zonyansa, Taonani, ine Paulo ndinena ndi inu, kuti, ngati mulola akuduleni, Khristu simudzapindula naye kanthu. kupembedza mafano, nyanga, madano, ndeu, kaduka, zopsa mtima, zotetana, magawano, mipatuko, njiru, kuledzera, mchezo, ndi zina zotere; zimene ndikuchenjezani nazo, monga ndachita, kuti iwo akuchitachita zotere sadzalowa Ufumu wa Mulungu.
Koma chipatso cha Mzimu ndicho chikondi, chimwemwe, mtendere, kuleza mtima, chifundo, kukoma mtima, chikhulupiriro, chifatso, chiletso; pokana zimenezi palibe lamulo.
Koma mukhalirane okoma wina ndi mnzake, a mtima wachifundo, akukhululukirana nokha, monganso Mulungu mwa Khristu anakhululukira inu.
Chifukwa chake khalani akutsanza a Mulungu, monga ana okondedwa; kuyesera chokondweretsa Ambuye nchiyani; ndipo musayanjane nazo ntchito za mdima zosabala kanthu, koma makamakanso muzitsutse; pakuti zochitidwa nao m'tseri, kungakhale kuzinena kuchititsa manyazi. Koma zinthu zonse potsutsika ndi kuunika, zionekera; pakuti chonse chakuonetsa chili kuunika. Mwa ichi anena, Khala maso wogona iwe, nuuke kwa akufa, ndipo Khristu adzawala pa iwe. Potero, penyani bwino umo muyendera, si monga opanda nzeru, koma monga anzeru; akuchita machawi, popeza masiku ali oipa. Chifukwa chake musakhale opusa, koma dziwitsani chifuniro cha Ambuye nchiyani. Ndipo musaledzere naye vinyo, m'mene muli chitayiko; komatu mudzale naye Mzimu, ndi kudzilankhulira nokha ndi masalimo, ndi mayamiko, ndi nyimbo zauzimu, kuimbira ndi kuimba m'malimba Ambuye mumtima mwanu; ndipo yendani m'chikondi monganso Khristu anakukondani inu, nadzipereka yekha m'malo mwathu, chopereka ndi nsembe kwa Mulungu, ikhale fungo lonunkhira bwino.
musachite kanthu monga mwa chotetana, kapena monga mwa ulemerero wopanda pake, komatu ndi kudzichepetsa mtima, yense ayese anzake omposa iye mwini; pakuti chifukwa cha ntchito ya Khristu anafikira pafupi imfa, wosasamalira moyo wake, kuti akakwaniritse chiperewero cha utumiki wanu wa kwa ine. munthu yense asapenyerere zake za iye yekha, koma yense apenyererenso za mnzake.
Koma tsopano tayani inunso zonsezi: mkwiyo, kupsa mtima, dumbo, mwano, zonyansa zotuluka m'kamwa mwanu:
Chifukwa chake valani, monga osankhika a Mulungu, oyera mtima ndi okondedwa, mtima wachifundo, kukoma mtima, kudzichepetsa, chifatso, kuleza mtima; kulolerana wina ndi mnzake, ndi kukhululukirana eni okha, ngati wina ali nacho chifukwa pa mnzake; monganso Ambuye anakhululukira inu, teroni inunso;
Ndipo mtendere wa Khristu uchite ufumu m'mitima yanu, kulingakonso munaitanidwa m'thupi limodzi; ndipo khalani akuyamika.
Penyani kuti wina asabwezere choipa womchitira choipa; komatu nthawi zonse mutsatire chokoma, kwa anzanu, ndi kwa onse.
Chifukwa chake ndifuna kuti amunawo apemphere pamalo ponse, ndi kukweza manja oyera, opanda mkwiyo ndi makani.
Ndipo kapolo wa Ambuye sayenera kuchita ndeu, komatu akhale woyenera, waulere pa onse, wodziwa kuphunzitsa, woleza, wolangiza iwo akutsutsana mofatsa; ngati kapena Mulungu awapatse iwo chitembenuziro, kukazindikira choonadi,
asachitire mwano munthu aliyense, asakhale andeu, akhale aulere, naonetsere chifatso chonse pa anthu onse.
pakuti timdziwa Iye amene anati, Kubwezera chilango nkwanga, Ine ndidzabwezera. Ndiponso, Ambuye adzaweruza anthu ake.
Londolani mtendere ndi anthu onse, ndi chiyeretso chimene, akapanda ichi, palibe mmodzi adzaona Ambuye:
Koma nzeru yochokera kumwamba iyamba kukhala yoyera, nikhalanso yamtendere, yaulere, yomvera bwino, yodzala chifundo ndi zipatso zabwino, yopanda tsankho, yosadzikometsera pamaso. Ndipo chipatso cha chilungamo chifesedwa mumtendere kwa iwo akuchita mtendere.
Momwemo pakutaya choipa chonse, ndi chinyengo chonse, ndi maonekedwe onyenga, ndi kaduka, ndi masinjiriro onse,
amene pochitidwa chipongwe sanabwezere chipongwe, pakumva zowawa, sanaopse, koma anapereka mlandu kwa Iye woweruza kolungama;
osabwezera choipa ndi choipa, kapena chipongwe ndi chipongwe, koma penatu madalitso; pakuti kudzatsata ichi mwaitanidwa, kuti mukalandire dalitso.
koposa zonse mukhale nacho chikondano chenicheni mwa inu nokha; pakuti chikondano chikwiriritsa unyinji wa machimo;
Iye amene anena kuti ali m'kuunika, namuda mbale wake, ali mumdima kufikira tsopano lino.
Koma iye wakumuda mbale wake ali mumdima, nayenda mumdima, ndipo sadziwa kumene amukako, pakuti mdima wamdetsa maso ake.
Yense wakudana ndi mbale wake ali wakupha munthu; ndipo mudziwa kuti wakupha munthu aliyense alibe moyo wosatha wakukhala mwa iye.
Okondedwa, tikondane wina ndi mnzake: chifukwa kuti chikondi chichokera kwa Mulungu, ndipo yense amene akonda, abadwa kuchokera kwa Mulungu, namzindikira Mulungu. Iye wosakonda sazindikira Mulungu; chifukwa Mulungu ndiye chikondi.
Munthu akati, kuti, Ndikonda Mulungu, nadana naye mbale wake, ali wabodza: pakuti iye wosakonda mbale wake amene wamuona, sangathe kukonda Mulungu amene sanamuone.
Wina akaona mbale wake alikuchimwa tchimo losati la kuimfa, apemphere Mulungu, ndipo Iye adzampatsira moyo wa iwo akuchita machimo osati a kuimfa. Pali tchimo la kuimfa: za ililo sindinena kuti mupemphere.
Chiyambi cha ndeu chifanana ndi kutsegulira madzi; tsono kupikisana kusanayambe tasiya makani.
Chitani chinthenthe, ndipo musachimwe. Nenani mumtima mwanu pakama panu, ndipo mukhale chete.
Yehova ndiye wa nsoni zokoma ndi wachisomo, wosakwiya msanga, ndi wa chifundo chochuluka. Sadzatsutsana nao nthawi zonse; ndipo sadzasunga mkwiyo wake kosatha.
Kadzichenjerani nokha; akachimwa mbale wako umdzudzule, akalapa, umkhululukire. momwemo kudzakhala tsiku lakuvumbuluka Mwana wa Munthu. Tsikulo iye amene adzakhala pamwamba pa tsindwi, ndi akatundu ake m'nyumba, asatsike kuwatenga; ndipo iye amene ali m'munda modzimodzi asabwere ku zake za m'mbuyo. Kumbukirani mkazi wa Loti. Iye aliyense akafuna kusunga moyo wake adzautaya, koma iye aliyense akautaya, adzausunga. Ndinena ndi inu, usiku womwewo adzakhala awiri pa kama mmodzi; mmodzi adzatengedwa, ndi wina adzasiyidwa. Padzakhala akazi awiri akupera pamodzi, mmodzi adzatengedwa, ndi wina adzasiyidwa. Ndipo anayankha nanena kwa Iye, Kuti, Ambuye? Ndipo anati kwa iwo, Pamene pali mtembo, pomweponso miimba idzasonkhanidwa. Ndipo akakuchimwira kasanu ndi kawiri pa tsiku lake, nakakutembenukira kasanu ndi kawiri ndi kunena, Ndalapa ine; uzimkhululukira.
Ndipo si chotero chokha, komanso tikondwera m'zisautso; podziwa ife kuti chisautso chichita chipiriro; ndi chipiriro chichita chizolowezi; ndi chizolowezi chichita chiyembekezo:
Ndipo tidziwa kuti amene akonda Mulungu zinthu zonse zithandizana kuwachitira ubwino, ndiwo amene aitanidwa monga mwa kutsimikiza kwa mtima wake.
Chifukwa chake tilondole zinthu za mtendere, ndi zinthu zakulimbikitsana wina ndi mnzake.
Koma zinthu zonse zichokera kwa Mulungu amene anatiyanjanitsa kwa Iye yekha mwa Khristu, natipatsa utumiki wa chiyanjanitso; ndiko kunena kuti Mulungu anali mwa Khristu, alinkuyanjanitsa dziko lapansi kwa Iye yekha, osawawerengera zolakwa zao; ndipo anaikiza kwa ife mau a chiyanjanitso.
Abale, ngatinso munthu agwidwa nako kulakwa kwakuti, inu auzimu, mubweze wotereyo mu mzimu wa chifatso; ndi kudzipenyerera wekha, ungayesedwe nawenso.
Ndipo mtendere wa Mulungu wakupambana chidziwitso chonse, udzasunga mitima yanu ndi maganizo anu mwa Khristu Yesu.
ndi kuyang'anira kuti pangakhale wina wakuperewera chisomo cha Mulungu, kuti ungapuke muzu wina wa kuwawa mtima ungavute inu, ndipo aunyinji angadetsedwe nao;
Pakuti maganizo anga sali maganizo anu, ngakhale njira zanu sizili njira zanga, ati Yehova. Pakuti monga kumwamba kuli kutali ndi dziko lapansi, momwemo njira zanga zili zazitali kupambana njira zanu, ndi maganizo anga kupambana maganizo anu.
Pakuti iwo amene ali monga mwa thupi asamalira zinthu za thupi; koma iwo amene ali monga mwa mzimu, asamalira zinthu za mzimu: pakuti chisamaliro cha thupi chili imfa; koma chisamaliro cha mzimu chili moyo ndi mtendere.
chikwirira zinthu zonse, chikhulupirira zinthu zonse, chiyembekeza zinthu zonse, chipirira zinthu zonse.
Chifukwa kuti kulimbana kwathu sitilimbana nao mwazi ndi thupi, komatu nao maukulu, ndi maulamuliro, ndi akuchita zolimbika a dziko lapansi a mdima uno, ndi auzimu a choipa m'zakumwamba.
ndipo tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino,
Ndani ali wanzeru, ndi waluso mwa inu? Aonetsere ndi mayendedwe ake abwino ntchito zake mu nzeru yofatsa. Koma mukakhala nako kaduka kowawa, ndi chotetana m'mtima mwanu, musadzitamandira, ndipo musamanama potsutsana nacho choonadi.
Ndipo ngati mbale wako akuchimwira iwe, pita, numlangize pa nokha iwe ndi iye; ngati akumvera iwe, wambweza mbale wako.
Khalani inu achifundo monga Atate wanu ali wachifundo. Ndipo musamaweruza, ndipo simudzaweruzidwa. Ndipo musawatsutsa, ndipo simudzamatsutsidwa. Khululukani, ndipo mudzakhululukidwa.
Ndipo Mulungu wa chipiriro ndi wa chitonthozo apatse inu kuti mukhale ndi mtima umodzi wina ndi mnzake, monga mwa Khristu Yesu;
koma ndi kuchita zoona mwa chikondi tikakule m'zinthu zonse, kufikira Iye amene ali mutu ndiye Khristu;
Mau a Khristu akhalitse mwa inu chichulukire mu nzeru yonse, ndi kuphunzitsa ndi kuyambirirana eni okha ndi masalimo, ndi mayamiko ndi nyimbo zauzimu, ndi kuimbira Mulungu ndi chisomo mumtima mwanu.
Munthu asapeputse ubwana wako; komatu khala chitsanzo kwa iwo okhulupirira, m'mau, m'mayendedwe, m'chikondi, m'chikhulupiriro, m'kuyera mtima.
tigwiritse chivomerezo chosagwedera cha chiyembekezo chathu, pakuti wolonjezayo ali wokhulupirika; ndipo tiganizirane wina ndi mnzake kuti tifulumizane ku chikondano ndi ntchito zabwino,
Momwemonso, anyamata inu, mverani akulu. Koma nonsenu muvale kudzichepetsa kuti mutumikirane; pakuti Mulungu akaniza odzikuza, koma apatsa chisomo kwa odzichepetsa. Potero dzichepetseni pansi padzanja la mphamvu la Mulungu, kuti panthawi yake akakukwezeni;
Mulibe mantha m'chikondi; koma chikondi changwiro chitaya kunja mantha, popeza mantha ali nacho chilango, ndipo wamanthayo sakhala wangwiro m'chikondi.
ndipo adzawapukutira misozi yonse kuichotsa pamaso pao; ndipo sipadzakhalanso imfa; ndipo sipadzakhalanso maliro, kapena kulira, kapena chowawitsa; zoyambazo zapita.
ndi kuonetsera kudzichepetsa konse, ndi chifatso, ndi kuonetsera chipiriro, ndi kulolerana wina ndi mnzake, mwa chikondi;