Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




1 Yohane 2:11 - Buku Lopatulika

11 Koma iye wakumuda mbale wake ali mumdima, nayenda mumdima, ndipo sadziwa kumene amukako, pakuti mdima wamdetsa maso ake.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Koma iye wakumuda mbale wake ali mumdima, nayenda mumdima, ndipo sadziwa kumene amukako, pakuti mdima wamdetsa maso ake.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Munthu wodana ndi mnzake, ali mu mdima, ndipo akuyenda mu mdima. Sadziŵa kumene akupita, chifukwa mdima wamudetsa m'maso.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Koma aliyense wodana ndi mʼbale wake ali mu mdima ndipo akuyenda mu mdima. Iyeyo sakudziwa kumene akupita, chifukwa mdima wamudetsa mʼmaso mwake.

Onani mutuwo Koperani




1 Yohane 2:11
16 Mawu Ofanana  

Ndipo Abisalomu sanalankhule ndi Aminoni chabwino kapena choipa, pakuti Abisalomu anamuda Aminoni popeza adachepetsa mlongo wake Tamara.


Njira ya oipa ikunga mdima; sadziwa chimene chiwaphunthwitsa.


Wanzeru maso ake ali m'mutu wake, koma chitsiru chiyenda mumdima; ndipo nanenso ndinazindikira kuti chomwe chiwagwera onsewo ndi chimodzi.


Usamamuda mbale wako mumtima mwako; umdzudzule munthu mnzako ndithu, usadzitengera uchimo chifukwa cha iye.


Pamenepo Yesu anati kwa iwo, Katsala kanthawi kakang'ono ndipo kuunika kuli mwa inu. Yendani pokhala muli nako kuunika, kuti mdima sungakupezeni; ndipo woyenda mumdima sadziwa kumene amukako.


Wadetsa maso ao, naumitsa mtima wao; kuti angaone ndi maso, angazindikire ndi mtima, nangatembenuke, ndipo ndingawachiritse.


koma mitima yao inaumitsidwa; pakuti kufikira lero lomwe lino, pa kuwerenga kwa pangano lakale chophimba chomwechi chikhalabe chosavundukuka, chimene chilikuchotsedwa mwa Khristu.


mwa amene mulungu wa nthawi ino ya pansi pano anachititsa khungu maganizo ao a osakhulupirira, kuti chiwalitsiro cha Uthenga Wabwino wa ulemerero wa Khristu, amene ali chithunzithunzi cha Mulungu, chisawawalire.


Pakuti kale ifenso tinali opusa, osamvera, onyengeka, akuchitira ukapolo zilakolako ndi zokondweretsa za mitundumitundu, okhala m'dumbo ndi njiru, odanidwa, odana wina ndi mnzake.


Pakuti iye wakusowa izi ali wakhungu, wa chimbuuzi, woiwala matsukidwe ake potaya zoipa zake zakale.


Tikati kuti tiyanjana ndi Iye, ndipo tiyenda mumdima, tinama, ndipo sitichita choonadi;


Iye amene akonda mbale wake akhala m'kuunika, ndipo mwa iye mulibe chokhumudwitsa.


Iye amene anena kuti ali m'kuunika, namuda mbale wake, ali mumdima kufikira tsopano lino.


Yense wakudana ndi mbale wake ali wakupha munthu; ndipo mudziwa kuti wakupha munthu aliyense alibe moyo wosatha wakukhala mwa iye.


Munthu akati, kuti, Ndikonda Mulungu, nadana naye mbale wake, ali wabodza: pakuti iye wosakonda mbale wake amene wamuona, sangathe kukonda Mulungu amene sanamuone.


Chifukwa unena kuti ine ndine wolemera, ndipo chuma ndili nacho, osasowa kanthu; ndipo sudziwa kuti ndiwe watsoka, ndi wochititsa chifundo, ndi wosauka, ndi wakhungu, ndi wausiwa;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa