Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Afilipi 4:5 - Buku Lopatulika

5 Kufatsa kwanu kuzindikirike ndi anthu onse. Ambuye ali pafupi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Kufatsa kwanu kuzindikirike ndi anthu onse. Ambuye ali pafupi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Kufatsa kwanu kuziwoneka pamaso pa anthu onse. Ambuyetu ali pafupi.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Kufatsa kwanu kuzioneka pamaso pa anthu onse. Ambuye anu ali pafupi.

Onani mutuwo Koperani




Afilipi 4:5
25 Mawu Ofanana  

Chifukwa chake ndinena kwa inu, Musadere nkhawa moyo wanu, chimene mudzadya ndi chimene mudzamwa; kapena thupi lanu, chimene mudzavala. Kodi moyo suli woposa chakudya, ndi thupi loposa chovala?


Chifukwa chake musadere nkhawa za mawa; pakuti mawa adzadzidera nkhawa iwo okha. Zikwanire tsiku zovuta zake.


Koma mudziyang'anire nokha, kuti kapena mitima yanu ingalemetsedwe ndi madyaidya ndi kuledzera, ndi zosamalira za moyo uno, ndi kuti tsiku ilo lingafikire inu modzidzimutsa ngati msampha;


Ngati wina sakonda Ambuye, akhale wotembereredwa. Akudza Ambuye.


Koma pamenepo pali chosowa konsekonse mwa inu, kuti muli nayo milandu wina ndi mnzake. Chifukwa ninji simusankhula kulola kuipsidwa? Simusankhula chifukwa ninji kulola kunyengedwa?


Chifukwa chake, ngati chakudya chikhumudwitsa mbale wanga, sindidzadya nyama kunthawi yonse, kuti ndingakhumudwitse mbale wanga.


Koma yense wakuyesetsana adzikanizira zonse. Ndipo iwowa atero kuti alandire korona wakuvunda; koma ife wosavunda.


Koma ine ndekha Paulo, ndidandaulira inu mwa kufatsa ndi ulere wa Khristu, ine amene pamaso panu ndikhala wodzichepetsa pakati pa inu, koma pokhala kwina ine ndilimbika mtima kwa inu;


kuti musamagwedezeka mtima msanga ndi kutaya maganizo anu, kapena kuopsedwa, mwa mzimu kapena mwa mau; kapena mwa kalata, monga wolembedwa ndi ife, monga ngati tsiku la Ambuye lafika;


asachitire mwano munthu aliyense, asakhale andeu, akhale aulere, naonetsere chifatso chonse pa anthu onse.


osaleka kusonkhana kwathu pamodzi, monga amachita ena, komatu tidandaulirane, ndiko koposa monga momwe muona tsiku lilikuyandika.


Pakuti katsala kanthawi kakang'onong'ono, ndipo wakudzayo adzafika, wosachedwa.


ndi kusanthula nthawi yiti, kapena nthawi yanji Mzimu wa Khristu wokhala mwa iwo analozera, pakuchitiratu umboni wa masautso a Khristu, ndi ulemerero wotsatana nao.


Koma chitsiriziro cha zinthu zonse chili pafupi; chifukwa chake khalani anzeru, ndipo dikirani m'mapemphero;


Iye wakuchitira umboni izi, anena, Indetu; ndidza msanga. Amen; idzani, Ambuye Yesu.


Ndipo taonani, ndidza msanga. Wodala iye amene asunga mau a chinenero cha buku ili.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa