Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Aefeso 6:12 - Buku Lopatulika

12 Chifukwa kuti kulimbana kwathu sitilimbana nao mwazi ndi thupi, komatu nao maukulu, ndi maulamuliro, ndi akuchita zolimbika a dziko lapansi a mdima uno, ndi auzimu a choipa m'zakumwamba.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Chifukwa kuti kulimbana kwathu sitilimbana nao mwazi ndi thupi, komatu nao maukulu, ndi maulamuliro, ndi akuchita zolimbika a dziko lapansi a mdima uno, ndi auzimu a choipa m'zakumwamba.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Paja sitikulimbana ndi anthu chabetu ai. Tikulimbana ndi maufumu, aulamuliro ndi mphamvu za dziko lino lapansi lamdima, ndiponso ndi mizimu yoipa yamumlengalenga.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Pakuti sitikulimbana ndi thupi ndi magazi, koma tikulimbana ndi maufumu, maulamuliro, mphamvu za dziko la mdima, ndi mphamvu zoyipa kwambiri zauzimu zamlengalenga.

Onani mutuwo Koperani




Aefeso 6:12
25 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehova anati kwa Satana, Ufuma kuti? Nayankha Satana, nati kwa Yehova, Kupitapita m'dziko, ndi kuyendayenda m'mwemo.


Ndipo Yesu anayankha iye, nati, Ndiwe wodala, Simoni Bara-Yona: pakuti thupi ndi mwazi sizinakuululire ichi, koma Atate wanga wa Kumwamba.


ndipo malabadiro a dziko lapansi, ndi chinyengo cha chuma, ndi kulakalaka kwa zinthu zina, zilowamo, zitsamwitsa mau, ndipo akhala opanda chipatso.


Yesetsani kulowa pa khomo lopapatiza; chifukwa anthu ambiri, ndikuuzani, adzafunafuna kulowamo, koma sadzakhoza.


Masiku onse, pamene ndinali ndi inu mu Kachisi, simunatanse manja anu kundigwira: koma nyengo ino ndi yanu, ndipo ulamuliro wa mdima ndi wanu.


Tsopano pali kuweruza kwa dziko ili lapansi; mkulu wa dziko ili lapansi adzatayidwa kunja tsopano.


Sindidzalankhulanso zambiri ndi inu, pakuti mkulu wa dziko lapansi adza; ndipo alibe kanthu mwa Ine;


za chiweruzo, chifukwa mkulu wa dziko ili lapansi waweruzidwa.


kukawatsegulira maso ao, kuti atembenuke kuchokera kumdima, kulinga kukuunika, ndi kuchokera ulamuliro wa Satana kulinga kwa Mulungu, kuti alandire iwo chikhululukiro cha machimo, ndi cholowa mwa iwo akuyeretsedwa ndi chikhulupiriro cha mwa Ine.


Pakuti ndakopeka mtima kuti ngakhale imfa, ngakhale moyo, ngakhale angelo, ngakhale maufumu, ngakhale zinthu zilipo, ngakhale zinthu zilinkudza, ngakhale zimphamvu,


Koma ndinena ichi, abale, kuti thupi ndi mwazi sizingathe kulowa Ufumu wa Mulungu; kapena chivundi sichilowa chisavundi.


Ndipo kulibe kudabwa; pakuti Satana yemwe adzionetsa ngati mngelo wa kuunika.


mwa amene mulungu wa nthawi ino ya pansi pano anachititsa khungu maganizo ao a osakhulupirira, kuti chiwalitsiro cha Uthenga Wabwino wa ulemerero wa Khristu, amene ali chithunzithunzi cha Mulungu, chisawawalire.


kuti avumbulutse Mwana wake mwa ine, kuti ndimlalikire Iye mwa amitundu; pomwepo sindinafunsane ndi thupi ndi mwazi:


pamwamba pa ukulu wonse, ndi ulamuliro, ndi mphamvu, ndi ufumu, ndi dzina lililonse lotchedwa, si m'nyengo ino ya pansi pano yokha, komanso mwa iyo ikudza;


Wolemekezeka Mulungu ndi Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu, amene anatidalitsa ife ndi dalitso lonse la mzimu m'zakumwamba mwa Khristu;


zimene munayendamo kale, monga mwa mayendedwe a dziko lapansi lino, monga mwa mkulu wa ulamuliro wa mlengalenga, wa mzimu wakuchita tsopano mwa ana a kusamvera;


kuti mu Mpingo azindikiritse tsopano kwa akulu ndi maulamuliro m'zakumwamba nzeru ya mitundumitundu ya Mulungu,


amene anatilanditsa ife kuulamuliro wa mdima, natisunthitsa kutilowetsa mu ufumu wa Mwana wa chikondi chake;


atavula maukulu ndi maulamuliro, anawaonetsera poyera, nawagonjetsera nako.


Koma ngatinso wina ayesana nao m'makani amasewero, samveka korona ngati sanayesane monga adapangana.


Chifukwa chake ifenso, popeza tizingidwa nao mtambo waukulu wotere wa mboni, titaye cholemetsa chilichonse, ndi tchimoli limangotizinga, ndipo tithamange mwachipiriro makaniwo adatiikira, ndi kupenyerera woyambira ndi womaliza wa chikhulupiriro chathu,


Simunakana kufikira mwazi pogwirana nalo tchimo;


amene akhala padzanja lamanja la Mulungu, atalowa mu Mwamba; pali angelo, ndi maulamuliro, ndi zimphamvu, zonse zimgonjera.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa