Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Ahebri 12:15 - Buku Lopatulika

15 ndi kuyang'anira kuti pangakhale wina wakuperewera chisomo cha Mulungu, kuti ungapuke muzu wina wa kuwawa mtima ungavute inu, ndipo aunyinji angadetsedwe nao;

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

15 ndi kuyang'anira kuti pangakhale wina wakuperewera chisomo cha Mulungu, kuti ungapuke muzu wina wa kuwawa mtima ungavute inu, ndipo aunyinji angadetsedwe nao;

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

15 Chenjerani kuti wina aliyense asabwerere m'mbuyo nkutaya madalitso a Mulungu. Chenjerani kuti wina aliyense asakhale ngati muzu woŵaŵa, umene umaphuka nkuvuta ena ambiri ndi ululu wake.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

15 Yangʼanitsitsani kuti wina aliyense asachiphonye chisomo cha Mulungu ndiponso kuti pasaphuke muzu wamkwiyo umene udzabweretsa mavuto ndi kudetsa ambiri.

Onani mutuwo Koperani




Ahebri 12:15
41 Mawu Ofanana  

Ndipo adzapereka Aisraele chifukwa cha machimo a Yerobowamu anachimwawo, nachimwitsa nao Aisraele.


Ndipo Mose anati kwa Aroni, Anthu awa anakuchitiranji, kuti iwe watengera iwo kulakwa kwakukulu kotere?


Chinjiriza mtima wako koposa zonse uzisunga; pakuti magwero a moyo atulukamo.


Ndikanachitanso chiyani ndi munda wanga wampesa, chimene sindinachite m'menemo; muja ndinayembekeza kuti udzabala mphesa, wabaliranji mphesa zosadya?


Chifukwa kuti munda wampesa wa Yehova wa makamu ndiwo banja la Israele, ndi anthu a Yuda, mtengo wake womkondweretsa; Iye nayembekeza chiweruziro, koma onani kuphana; nayembekeza chilungamo, koma onani kufuula.


Ndipo Ine ndinakuoka mpesa wangwiro, mbeu yoona; kodi bwanji wandisandukira Ine mbeu yopanda pake, ya mpesa wachilendo?


koma ndinakupempherera kuti chikhulupiriro chako chingazime; ndipo iwe, pamene watembenuka ukhazikitse abale ako.


Chifukwa chake iye wakuyesa kuti ali chilili, ayang'anire kuti angagwe.


Chikondi sichitha nthawi zonse, koma kapena zonenera zidzakhala chabe, kapena malilime adzaleka, kapena nzeru idzakhala chabe.


Musanyengedwe; mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma.


Kudzitamanda kwanu sikuli bwino. Kodi simudziwa kuti chotupitsa pang'ono chitupitsa mtanda wonse?


Dziyeseni nokha, ngati muli m'chikhulupiriro, dzitsimikizeni nokha. Kapena simuzindikira kodi za inu nokha kuti Yesu Khristu ali mwa inu? Mukapanda kukhala osatsimikizidwa.


Ndipo ochita naye pamodzi tidandauliranso kuti musalandire chisomo cha Mulungu kwachabe inu,


Ndipo Ayuda otsala anawagwiranso m'maso pamodzi naye; kotero kuti Barnabasinso anatengedwa ndi kugwira m'maso kwao.


Mulibe kanthu ndi Khristu, inu amene muyesedwa olungama ndi lamulo; mudagwa posiyana nacho chisomo.


Koma dama ndi chidetso chonse, kapena chisiriro, zisatchulidwe ndi kutchulidwa komwe mwa inu, monga kuyenera oyera mtima;


kuti angakhale pakati pa inu mwamuna, kapena mkazi, kapena banja, kapena fuko, mtima wao watembenuka kusiyana naye Yehova Mulungu wathu lero lino, kuti apite ndi kutumikira milungu ya amitundu aja; kuti ungakhale pakati pa inu muzu wakubala ndulu ndi chowawa.


Pakuti mpesa wao ndiwo wa ku Sodomu, ndi wa m'minda ya ku Gomora; mphesa zao ndizo mphesa zandulu, matsangwi ao ngowawa.


Chokhachi, dzichenjerani nokha, ndi kusunga moyo wanu mwachangu, kuti mungaiwale zinthuzi adaziona maso anu, ndi kuti zisachoke kumtima kwanu masiku onse a moyo wanu; koma muzidziwitsa ana anu ndi zidzukulu zanu.


Chifukwa chake fetsani ziwalozo zili padziko; dama, chidetso, chifunitso chamanyazi, chilakolako choipa, ndi chisiriro, chimene chili kupembedza mafano;


Zonse ziyera kwa iwo amene ayera mtima; koma kwa iwo odetsedwa ndi osakhulupirira kulibe kanthu koyera; komatu zadetsedwa nzeru zao ndi chikumbumtima chao.


Tapenyani, abale, kuti kapena ukakhale mwa wina wa inu mtima woipa wosakhulupirira, wakulekana ndi Mulungu wamoyo;


Chifukwa chake tiope kuti kapena likatsala lonjezano lakulowa mpumulo wake, wina wa inu angaoneke ngati adaliperewera.


Chifukwa chake tichite changu cha kulowa mpumulowo, kuti wina angagwe m'chitsanzo chomwe cha kusamvera.


Koma tikhumba kuti yense wa inu aonetsere changu chomwechi cholinga kuchiyembekezo chokwanira kufikira chitsiriziro;


Ndipo inu, musakhudze choperekedwacho, mungadziononge konse, potapa choperekedwacho; ndi kuononga konse chigono cha Israele ndi kuchisautsa.


Momwemo abale, onjezani kuchita changu kukhazikitsa maitanidwe ndi masankhulidwe anu; pakuti mukachita izi, simudzakhumudwa nthawi zonse;


Pakuti polankhula mau otukumuka opanda pake, anyengerera pa zilakolako za thupi, ndi zonyansa, anthu amene adayamba kupulumuka kwa iwo a mayendedwe olakwa;


Popeza izi zonse zidzakanganuka kotero, muyenera inu kukhala anthu otani nanga, m'mayendedwe opatulika ndi m'chipembedzo,


Momwemo, okondedwa, popeza muyembekeza izi, chitani changu kuti mupezedwe ndi Iye mumtendere, opanda banga ndi opanda chilema.


Mudzipenyerere nokha, kuti mungataye zimene tazichita, koma kuti mulandire mphotho yokwanira.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa