Masalimo 125 - Buku LopatulikaOkhulupirira Yehova akhazikika mtima Nyimbo yokwerera. 1 Iwo akukhulupirira Yehova akunga phiri la Ziyoni, losasunthika, likhazikika kosatha. 2 Monga mapiri azinga Yerusalemu, momwemo Yehova azinga anthu ake, kuyambira tsopano kufikira nthawi zonse. 3 Pakuti ndodo yachifumu ya choipa siidzapumula pa gawo la olungama; kuti olungama asatulutse dzanja lao kuchita chosalungama. 4 Chitirani chokoma, Yehova, iwo okhala okoma; iwo okhala oongoka mumtima mwao. 5 Koma iwo akupatula kutsata njira zao zokhotakhota, Yehova adzawachotsa pamodzi ndi ochita zopanda pake. Mtendere ukhale pa Israele. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi