Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 125:3 - Buku Lopatulika

3 Pakuti ndodo yachifumu ya choipa siidzapumula pa gawo la olungama; kuti olungama asatulutse dzanja lao kuchita chosalungama.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Pakuti ndodo yachifumu ya choipa siidzapumula pa gawo la olungama; kuti olungama asatulutse dzanja lao kuchita chosalungama.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Mafumu oipa sadzalamulira nthaŵi yonse dziko limene lapatsidwa kwa anthu ake, kuti nawonso anthu olungamawo angachite zoipa.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Ndodo yaufumu ya anthu oyipa sidzakhala pa dziko limene lapatsidwa kwa anthu olungama, kuti anthu olungamawo angachite nawonso zoyipa.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 125:3
11 Mawu Ofanana  

Popeza adziwa mapangidwe athu; akumbukira kuti ife ndife fumbi.


Sadzatsutsana nao nthawi zonse; ndipo sadzasunga mkwiyo wake kosatha.


Anatulutsa manja ake awagwire iwo akuyanjana naye, anaipsa pangano lake.


Mdani sadzamuumira mtima; ndi mwana wa chisalungamo sadzamzunza.


Wofesa zosalungama adzakolola tsoka; ndipo nthyole ya mkwiyo wake idzalephera.


Iwe Asiriya chibonga cha mkwiyo wanga, ndodo m'dzanja lake muli ukali wanga!


Munalimbana naye pang'ono, pamene munamchotsa; wamchotsa iye kuomba kwake kolimba tsiku la mphepo yamlumbanyanja.


Sichinakugwerani inu chiyeso koma cha umunthu; koma Mulungu ali wokhulupirika, amene sadzalola inu kuyesedwa koposa kumene mukhoza; koma pamodzi ndi chiyeso adzaikanso populumukirapo, kuti mudzakhoze kupirirako.


Usaope zimene uti udzamve kuwawa; taona, mdierekezi adzaponya ena a inu m'nyumba yandende, kuti mukayesedwe; ndipo mudzakhala nacho chisautso masiku khumi. Khala wokhulupirika kufikira imfa, ndipo ndidzakupatsa iwe korona wa moyo.


Onani, lero lomwe maso anu anapenya kuti Yehova anakuperekani inu lero m'dzanja langa m'phangamo, ndipo ena anandiuza ndikupheni; koma ndinakulekani, ndi kuti, sindidzatukulira mbuye wanga dzanja langa; chifukwa iye ndiye wodzozedwa wa Yehova.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa