Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 125:2 - Buku Lopatulika

2 Monga mapiri azinga Yerusalemu, momwemo Yehova azinga anthu ake, kuyambira tsopano kufikira nthawi zonse.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Monga mapiri azinga Yerusalemu, momwemo Yehova azinga anthu ake, kuyambira tsopano kufikira nthawi zonse.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Monga momwe mapiri amazingira Yerusalemu, momwemonso Chauta akuzinga anthu ake kuyambira tsopano mpaka muyaya.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Monga mapiri azungulira Yerusalemu, momwemonso Yehova azungulira anthu ake kuyambira tsopano mpaka muyaya.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 125:2
8 Mawu Ofanana  

Ndipo Elisa anapemphera, nati, Yehova, mumtsegulire maso ake kuti aone. Pamenepo Yehova anamtsegulira maso mnyamatayo, napenya iye, ndipo taonani, paphiripo panadzala ndi akavalo ndi magaleta amoto akumzinga Elisa.


Yehova adzasungira kutuluka kwako ndi kulowa kwako, kuyambira tsopano kufikira nthawi zonse.


Mngelo wa Yehova azinga kuwatchinjiriza iwo akuopa Iye, nawalanditsa iwo.


Ndipo Yehova adzalenga pokhala ponse paphiri la Ziyoni, ndi pa misonkhano yake, mtambo ndi utsi usana, ndi kung'azimira kwa malawi a moto usiku; chifukwa kuti pa ulemerero wonse padzayalidwa chophimba.


Mafumu a dziko lapansi sanakhulupirire, ngakhale onse okhala kunja kuno, kuti adani ndi amaliwongo adzalowadi m'zipata za Yerusalemu.


Pakuti Ine, ati Yehova, ndidzakhala kwa iye linga lamoto pozungulira pake, ndipo ndidzakhala ulemerero m'kati mwake.


Mulungu wamuyaya ndiye mokhaliramo mwako; ndi pansipo pali manja osatha. Ndipo aingitsa mdani pamaso pako, nati, Ononga.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa