Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


116 Mau a m'Baibulo Okhudza Kuipa

116 Mau a m'Baibulo Okhudza Kuipa

Mawu a Mulungu m’Masalimo 5:4 amati, “Pakuti Inu simuli Mulungu wokondwera ndi zoipa; woipa sadzakhala nanu pamodzi.” Ndipo ndikukulimbikitsani kuti muzindikire kufunika koŵerenga ndi kusinkhasinkha Mawu a Mulungu, chifukwa ndiwo chitsogozo chathu cha tsiku ndi tsiku. Ngati tikufuna moyo wabwino, tiyenera kutsatira malamulo ndi mawu amene Ambuye anatipatsa m’Baibulo.

Choncho, tisiye zoipa zonse zimene sizikondweretsa Mulungu. Tiwongolere mapazi athu ndikutsatira mawu ake kuti atitsogolere ku choonadi chake. Popeza iye amadana ndi zoipa, tiyesetse ndi mtima wonse kuti tichotse njira yachinyengo mwa ife. Tibwerere kwa Mulungu ndikulapa machimo athu.

Chifundo chake chikufuna kutipulumutsa, kutiyeretse, ndikutibwezeretsa kuti tikakhale ndi moyo wabwino, wonga fungo lokoma pamaso pake.




Masalimo 5:4

Pakuti Inu sindinu Mulungu wakukondwera nacho choipa mphulupulu siikhala ndi Inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 4:14

Usalowe m'mayendedwe ochimwa, usayende m'njira ya oipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 6:16-19

Zilipo zinthu zisanu ndi chimodzi Yehova azida; ngakhale zisanu ndi ziwiri zimnyansa: Maso akunyada, lilime lonama, ndi manja akupha anthu osachimwa; mtima woganizira ziwembu zoipa, mapazi akuthamangira mphulupulu m'mangum'mangu; mboni yonama yonong'ona mabodza, ndi wopikisanitsa abale.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 7:9

Ithe mphulupulu ya anthu oipa, ndikupemphani, koma wolungamayo mumkhazikitse. Pakuti woyesa mitima ndi impso ndiye Mulungu wolungama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 4:14-15

Usalowe m'mayendedwe ochimwa, usayende m'njira ya oipa. Pewapo, osapitamo; patukapo, nupitirire.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mika 2:1

Tsoka iwo akulingirira chinyengo, ndi kukonza choipa pakama pao! Kutacha m'mawa achichita, popeza chikhozeka m'manja mwao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 5:20

Tsoka kwa iwo amene ayesa zoipa zabwino, ndi zabwino zoipa; amene aika mdima m'malo mwa kuyera, ndi kuyera m'malo mwa mdima; amene aika zowawa m'malo mwa zotsekemera, ndi zotsekemera m'malo mwa zowawa!

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:21

Musagonje kwa choipa, koma ndi chabwino gonjetsani choipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 64:2

Ndibiseni pa upo wachinsinsi wa ochita zoipa; pa phokoso la ochita zopanda pake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 4:17

Pakuti amadya chakudya cha uchimo, namwa vinyo wa chifwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 5:4-5

Pakuti Inu sindinu Mulungu wakukondwera nacho choipa mphulupulu siikhala ndi Inu. Opusa sadzakhazikika pamaso panu, mudana nao onse akuchita zopanda pake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Zekariya 5:8

Ndipo anati, Uyu ndi uchimo; namgwetsa m'kati mwa efa; naponya ntovu wolemerawo pakamwa pake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 15:19-20

Pakuti mumtima muchokera maganizo oipa, zakupha, zachigololo, zachiwerewere, zakuba, za umboni wonama, zamwano; Ophunzira anu alumphiranji miyambo ya makolo? Pakuti sasamba manja pakudya. izi ndizo ziipitsa munthu, koma kudya osasamba manja sikuipitsa munthu ai.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 10:15

Thyolani mkono wa woipa; ndipo wochimwa, mutsate choipa chake kufikira simuchipezanso china.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 1:29-32

anadzala ndi zosalungama zonse, kuipa, kusirira, dumbo; odzala ndi kaduka, mbanda, ndeu, chinyengo, udani; wakunena za Mwana wake, amene anabadwa, wa mbeu ya Davide, monga mwa thupi, akazitape, osinjirira, akumuda Mulungu, achipongwe, odzitama, amatukutuku, oyamba zoipa, osamvera akulu ao, opanda nzeru, osasunga mapangano, opanda chikondi cha chibadwidwe, opanda chifundo; amene ngakhale adziwa kuweruza kwake kwa Mulungu, kuti iwo amene achita zotere ayenera imfa, azichita iwo okha, ndiponso avomerezana ndi iwo akuzichita.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 34:21

Mphulupulu idzamupha woipa; ndipo adzawatsutsa kumlandu iwo akudana naye wolungama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 10:29-30

Njira ya Yehova ndi linga kwa woongoka mtima; koma akuchita zoipa adzaonongeka. Yehova samvetsa njala moyo wa wolungama; koma amainga chifuniro cha wochimwa. Wolungama sadzachotsedwa konse; koma oipa sadzakhalabe m'dziko.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yobu 35:8

Choipa chanu chikhoza kuipira munthu wonga inu, ndi chilungamo chanu chikhoza kukomera wobadwa ndi munthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 94:23

Ndipo anawabwezera zopanda pake zao, nadzawaononga m'choipa chao; Yehova Mulungu wathu adzawaononga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 25:5

Chotsera woipa pamaso pa mfumu, mpando wake udzakhazikika m'chilungamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 48:22

Kulibe mtendere, ati Yehova, kwa oipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 37:1-2

Usavutike mtima chifukwa cha ochita zoipa, usachite nsanje chifukwa cha ochita chosalungama. Katsala kanthawi ndipo woipa adzatha psiti; inde, udzayang'anira mbuto yake, nudzapeza palibe. Koma ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nao mtendere wochuluka. Woipa apangira chiwembu wolungama, namkukutira mano. Ambuye adzamseka, popeza apenya kuti tsiku lake likudza. Oipa anasolola lupanga, nakoka uta wao; alikhe ozunzika ndi aumphawi, aphe amene ali oongoka m'njira. Lupanga lao lidzalowa m'mtima mwao momwe, ndipo mauta ao adzathyoledwa. Zochepa zake za wolungama zikoma koposa kuchuluka kwao kwa oipa ambiri. Pakuti manja a oipa adzathyoledwa, koma Yehova achirikiza olungama. Yehova adziwa masiku a anthu angwiro; ndipo cholowa chao chidzakhala chosatha. Sadzachita manyazi m'nyengo yoipa, ndipo m'masiku a njala adzakhuta. Pakuti adzawamweta msanga monga udzu, ndipo adzafota monga msipu wauwisi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 15:21

Ndipo ndidzakulanditsa iwe m'dzanja la oipa, ndipo ndidzakuombola iwe m'dzanja la oopsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 3:19

Koma ukachenjeza woipa, osabwerera iye kuleka choipa chake kapena njira yake yoipa, adzafa mu mphulupulu yake; koma iwe walanditsa moyo wako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 59:2-4

koma zoipa zanu zakulekanitsani inu ndi Mulungu wanu; ndipo machimo anu abisa nkhope yake kwa inu, kuti Iye sakumva. Ndipo Mombolo adzafika ku Ziyoni, ndi kwa iwo amene atembenuka kusiya kulakwa mwa Yakobo, ati Yehova. Ndipo kunena za Ine, ili ndi pangano langa ndi iwo, ati Yehova; mzimu wanga umene uli pa iwe, ndi mau anga amene ndaika m'kamwa mwako sadzachoka m'kamwa mwako, pena m'kamwa mwa ana ako, pena m'kamwa mwa mbeu ya mbeu yako, ati Yehova, kuyambira tsopano ndi kunthawi zonse. Pakuti manja anu adetsedwa ndi mwazi, ndi zala zanu ndi mphulupulu, milomo yanu yanena zonama, lilime lanu lilankhula moipa. Palibe wotulutsa mlandu molungama, ndipo palibe wonena zoona; iwo akhulupirira mwachabe, nanena zonama; iwo atenga kusaweruzika ndi kubala mphulupulu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 5:11

ndipo musayanjane nazo ntchito za mdima zosabala kanthu, koma makamakanso muzitsutse;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Genesis 6:5

Ndipo anaona Yehova kuti kuipa kwa anthu kunali kwakukulu padziko lapansi, ndiponso kuti ndingaliro zonse za maganizo a mitima yao zinali zoipabe zokhazokha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:19-21

Ndipo ntchito za thupi zionekera, ndizo dama, chodetsa, kukhumba zonyansa, Taonani, ine Paulo ndinena ndi inu, kuti, ngati mulola akuduleni, Khristu simudzapindula naye kanthu. kupembedza mafano, nyanga, madano, ndeu, kaduka, zopsa mtima, zotetana, magawano, mipatuko, njiru, kuledzera, mchezo, ndi zina zotere; zimene ndikuchenjezani nazo, monga ndachita, kuti iwo akuchitachita zotere sadzalowa Ufumu wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 4:16

Pakuti akapanda kuchita zoipa, samagona; ndipo akapanda kukhumudwitsa wina, tulo tao tiwachokera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 6:18

mtima woganizira ziwembu zoipa, mapazi akuthamangira mphulupulu m'mangum'mangu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 3:1-5

Koma zindikira ichi, kuti masiku otsiriza zidzafika nthawi zowawitsa. Koma iwe watsatatsata chiphunzitso changa, mayendedwe, chitsimikizo mtima, chikhulupiriro, kuleza mtima, chikondi, chipiriro, mazunzo, kumva zowawa; zotere zonga anandichitira mu Antiokeya, mu Ikonio, mu Listara, mazunzo otere onga ndawamva; ndipo m'zonsezi Ambuye anandilanditsa. Ndipo onse akufuna kukhala opembedza m'moyo mwa Khristu Yesu, adzamva mazunzo. Koma anthu oipa ndi onyenga, adzaipa chiipire, kusokeretsa ndi kusokeretsedwa. Koma ukhalebe iwe mu izi zimene waziphunzira, nutsimikizika mtima nazo, podziwa amene adakuphunzitsa; ndi kuti kuyambira ukhanda wako wadziwa malembo opatulika, okhoza kukupatsa nzeru kufikira chipulumutso, mwa chikhulupiriro cha mwa Khristu Yesu. Lemba lililonse adaliuzira Mulungu, ndipo lipindulitsa pa chiphunzitso, chitsutsano, chikonzero, chilangizo cha m'chilungamo: kuti munthu wa Mulungu akhale woyenera, wokonzeka kuchita ntchito iliyonse yabwino. Pakuti anthu adzakhala odzikonda okha, okonda ndalama, odzitamandira, odzikuza, amwano, osamvera akuwabala, osayamika, osayera mtima, opanda chikondi chachibadwidwe, osayanjanitsika, akudierekeza, osakhoza kudziletsa, aukali, osakonda abwino, achiwembu, aliuma olimbirira, otukumuka mtima, okonda zokondweretsa munthu, osati okonda Mulungu; akukhala nao maonekedwe a chipembedzo, koma mphamvu yake adaikana; kwa iwonso udzipatule.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 3:12

Pakuti maso a Ambuye ali pa olungama, ndi makutu ake akumva pembedzo lao; koma nkhope ya Ambuye ili pa ochita zoipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 17:9

Mtima ndiwo wonyenga koposa, ndi wosachiritsika, ndani angathe kuudziwa?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 94:16-17

Adzandiukira ndani kutsutsana nao ochita zoipa? Adzandilimbikira ndani kutsutsana nao ochita zopanda pake? Akadapanda kukhala thandizo langa Yehova, moyo wanga ukadakhala kuli chete.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 13:12

Usiku wapita, ndi mbandakucha wayandikira; chifukwa chake tivule ntchito za mdima, ndipo tivale zida za kuunika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 11:21

Zoonadi, wochimwa sadzapulumuka chilango; koma mbeu ya olungama idzalanditsidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 3:8

iye wochita tchimo ali wochokera mwa mdierekezi, chifukwa mdierekezi amachimwa kuyambira pachiyambi. Kukachita ichi Mwana wa Mulungu adaonekera, ndiko kuti akaononge ntchito za mdierekezi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 9:17

Oipawo adzabwerera kumanda, inde amitundu onse akuiwala Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 21:10

Wamphulupulu mtima wake umkhumba zoipa; sakomera mtima mnzake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 11:5

Yehova ayesa wolungama mtima, koma moyo wake umuda woipa ndi iye wakukonda chiwawa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:17-18

Chomwecho mtengo wabwino uliwonse upatsa zipatso zokoma; koma mtengo wamphuchi upatsa zipatso zoipa. Sungathe mtengo wabwino kupatsa zipatso zoipa, kapena mtengo wamphuchi kupatsa zipatso zokoma.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:29

Yehova atalikira oipa; koma pemphero la olungama alimvera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 13:11

Ndipo ndidzalanga dziko lapansi, chifukwa cha kuipa kwao, ndi oipa chifukwa cha mphulupulu zao; ndipo ndidzaletsa kudzikuza kwa onyada, ndidzagwetsa kudzikweza kwa oopsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 24:19-20

Usavutike mtima chifukwa cha ochita zoipa; ngakhale kuchitira nsanje amphulupulu. pakuti mtima wao ulingalira za chionongeko; milomo yao ilankhula za mphulupulu. Pakuti woipayo sadzalandira mphotho; nyali ya amphulupulu idzazima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 1:5-6

Chifukwa chake oipa sadzaimirira pa mlanduwo, kapena ochimwa mu msonkhano wa olungama. Pakuti Yehova adziwa mayendedwe a olungama; koma mayendedwe a oipa adzatayika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 12:21

Palibe vuto lidzagwera wolungama; koma amphulupulu adzadzazidwa ndi zoipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 55:7

woipa asiye njira yake, ndi munthu wosalungama asiye maganizo ake, nabwere kwa Yehova; ndipo Yehova adzamchitira chifundo; ndi kwa Mulungu wathu, pakuti Iye adzakhululukira koposa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:31

Chiwawo chonse, ndi kupsa mtima, ndi mkwiyo, ndi chiwawa, ndi mwano zichotsedwe kwa inu, ndiponso choipa chonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 10:6

Madalitso ali pamutu pa wolungama; koma m'kamwa mwa oipa mubisa chiwawa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 13:41-42

Mwana wa Munthu adzatuma angelo ake, ndipo iwo adzasonkhanitsa pamodzi, ndi kuchotsa mu Ufumu wake zokhumudwitsa zonse, ndi anthu akuchita kusaweruzika, ndipo adzawataya iwo m'ng'anjo yamoto; kumeneko kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 6:12-15

Munthu wopanda pake, mwamuna wamphulupulu; amayenda ndi m'kamwa mokhota. Amatsinzinira ndi maso ake, napalasira ndi mapazi ake, amalankhula ndi zala zake; zopotoka zili m'mtima mwake, amaganizira zoipa osaleka; amapikisanitsa anthu. Chifukwa chake tsoka lake lidzadza modzidzimuka; adzasweka msangamsanga, palibe chompulumutsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 14:1-3

Wauchitsiru amati mumtima mwake, Kulibe Mulungu. Achita zovunda, achita ntchito zonyansa; kulibe wakuchita bwino. Yehova mu Mwamba anaweramira pa ana a anthu, kuti aone ngati aliko wanzeru, wakufuna Mulungu. Anapatuka onse; pamodzi anavunda mtima; palibe wakuchita bwino ndi mmodzi yense.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 34:16

Nkhope ya Yehova itsutsana nao akuchita zoipa, kudula chikumbukiro chao padziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 32:6

Pakuti wopusa adzanena zopusa, ndi mtima wake udzachita mphulupulu, kuchita zoipitsa, ndi kunena za Yehova molakwira, kusowetsa konse mtima wanjala, ndi kulepheretsa chakumwa cha waludzu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:29

Munthu wa chiwawa akopa mnzake, namuyendetsa m'njira yosakhala bwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 16:17-18

Ndipo ndikudandaulirani, abale, yang'anirani iwo akuchita zopatutsana ndi zophunthwitsa, kosalingana ndi chiphunzitsocho munachiphunzira inu; ndipo potolokani pa iwo. Pakuti otere satumikira Ambuye wathu Khristu, koma mimba yao; ndipo ndi mau osalaza ndi osyasyalika asocheretsa mitima ya osalakwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:6

Mphulupulu iomboledwa ndi chifundo ndi ntheradi; apatuka pa zoipa poopa Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yobu 8:20-22

Taona, Mulungu sakana munthu wangwiro; kapena kugwiriziza ochita zoipa. Koma adzadzaza m'kamwa mwako ndi kuseka, ndi milomo yako kufuula. Iwo akudana nawe adzavala manyazi; ndi hema wa oipa adzakhala kuli zii.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 140:1-2

Ndilanditseni, Yehova, kwa munthu woipa; ndisungeni kwa munthu wachiwawa; Makala amoto awagwere; aponyedwe kumoto; m'maenje ozama, kuti asaukenso. Munthu wamlomo sadzakhazikika padziko lapansi; choipa chidzamsaka munthu wachiwawa kuti chimgwetse. Ndidziwa kuti Yehova adzanenera wozunzika mlandu, ndi kuweruzira aumphawi. Indedi, olungama adzayamika dzina lanu; oongoka mtima adzakhala pamaso panu. amene adzipanga zoipa mumtima mwao; masiku onse amemeza nkhondo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 12:20

Chinyengo chili m'mitima ya oganizira zoipa; koma aphungu a mtendere amakondwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 59:7-8

Mapazi ao athamangira koipa, ndipo iwo afulumira kukhetsa mwazi wosachimwa; maganizo ao ali maganizo oipa; bwinja ndi chipasuko zili m'njira mwao. Njira ya mtendere saidziwa, ndipo palibe chiweruziro m'mayendedwe mwao; akhotetsa njira zao; aliyense ayenda m'menemo sadziwa mtendere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 24:1-2

Usachitire nsanje anthu oipa, ngakhale kufuna kukhala nao; Ukalefuka tsiku la tsoka mphamvu yako ichepa. Omwe atengedwa kuti akafe, uwapulumutse; omwe ati aphedwe, usaleke kuwalanditsa. Ukanena, Taonani, sitinadziwe chimenechi; kodi woyesa mitima sachizindikira ichi? Ndi wosunga moyo wako kodi sachidziwa? Ndipo kodi sabwezera munthu yense monga mwa machitidwe ake? Mwananga, idya uchi pakuti ngwabwino, ndi chisa chake chitsekemera m'kamwa mwako. Potero udzadziwa kuti nzeru ili yotero m'moyo wako; ngati waipeza padzakhala mphotho, ndipo chiyembekezo chako sichidzalephereka. Usabisalire, woipa iwe, pomanga wolungama; usapasule popuma iyepo. Pakuti wolungama amagwa kasanu ndi kawiri, nanyamukanso; koma oipa akhumudwa pomfikira tsoka. Usakondwere pakugwa mdani wako; mtima wako usasekere pokhumudwa iye; kuti Yehova angaone kukondwa kwako, ndi kukuyesa koipa, ndi kuleka kumkwiyira. Usavutike mtima chifukwa cha ochita zoipa; ngakhale kuchitira nsanje amphulupulu. pakuti mtima wao ulingalira za chionongeko; milomo yao ilankhula za mphulupulu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 36:1-4

Cholakwa cha woipayo chimati m'kati mwa mtima wanga, palibe kuopa Mulungu pamaso pake. Tanimphitsani chifundo chanu pa iwo akudziwa Inu; ndi chilungamo chanu pa oongoka mtima. Phazi la akudzikuza lisandifikire ine, ndi dzanja la oipa lisandichotse. Pomwepo padagwera ochita zopanda pake. Anawalikha, ndipo sadzatha kuukanso. Pakuti adzidyoletsa yekha m'kuona kwake, kuti anthu sadzachipeza choipa chake ndi kukwiya nacho. Mau a pakamwa pake ndiwo opanda pake ndi onyenga, waleka kuzindikira ndi kuchita bwino. Alingirira zopanda pake pakama pake; adziika panjira posati pabwino; choipa saipidwa nacho.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 26:24-26

Wakuda mnzake amanyenga ndi milomo yake; koma akundika chinyengo m'kati mwake. Pamene akometsa mau ake usamkhulupirire; pakuti m'mtima mwake muli zonyansa zisanu ndi ziwiri. Angakhale abisa udani wake pochenjera, koma udyo wake udzavumbulutsidwa posonkhana anthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 101:3-4

Sindidzaika chinthu choipa pamaso panga; chochita iwo akupatuka padera chindiipira; sichidzandimamatira. Mtima wopulukira udzandichokera; sindidzadziwana naye woipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 1:16-17

Sambani, dziyeretseni; chotsani machitidwe anu oipa pamaso panga; lekani kuchita zoipa; phunzirani kuchita zabwino; funani chiweruzo; thandizani osautsidwa, weruzirani ana amasiye, munenere akazi amasiye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 6:12

Chifukwa kuti kulimbana kwathu sitilimbana nao mwazi ndi thupi, komatu nao maukulu, ndi maulamuliro, ndi akuchita zolimbika a dziko lapansi a mdima uno, ndi auzimu a choipa m'zakumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 11:5

Chilungamo cha wangwiro chimaongola njira yake; koma woipa adzagwa ndi zoipa zake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 5:8

Khalani odzisungira, dikirani; mdani wanu mdierekezi, monga mkango wobuma, ayendayenda ndi kufunafuna wina akamlikwire:

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 139:23-24

Mundisanthule, Mulungu, nimudziwe mtima wanga; mundiyese nimudziwe zolingalira zanga. Ndipo mupenye ngati ndili nao mayendedwe oipa, nimunditsogolere panjira yosatha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 21:15

Kuchita chiweruzo kukondweretsa wolungama; koma kuwaononga akuchita mphulupulu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 3:11

Tsoka kwa woipa! Kudzamuipira; chifukwa kuti mphotho ya manja ake idzapatsidwa kwa iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 7:24

Koma sanamvere, sanatchere khutu, koma anayenda mu upo ndi m'kuuma kwa mtima wao woipa, nabwerera chambuyo osayenda m'tsogolo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 125:5

Koma iwo akupatula kutsata njira zao zokhotakhota, Yehova adzawachotsa pamodzi ndi ochita zopanda pake. Mtendere ukhale pa Israele.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 34:15

Maso a Yehova ali pa olungama mtima, ndipo makutu ake atchereza kulira kwao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mika 2:1-2

Tsoka iwo akulingirira chinyengo, ndi kukonza choipa pakama pao! Kutacha m'mawa achichita, popeza chikhozeka m'manja mwao. Nyamukani, chokani, pakuti popumula panu si pano ai; chifukwa cha udyo wakuononga ndi chionongeko chachikulu. Munthu akayenda ndi mtima wachinyengo ndi kunama, ndi kuti, Ndidzanenera kwa iwe za vinyo ndi chakumwa chakuledzeretsa; iye ndiye mneneri wa anthu ake. Ndidzakumemezani ndithu, Yakobo, inu nonse; ndidzasonkhanitsa ndithu otsala a Israele; ndidzawaika pamodzi ngati nkhosa za ku Bozira; ngati zoweta pakati pa busa pao adzachita phokoso chifukwa cha kuchuluka anthu. Wothyola wakwera pamaso pao; iwo anathyola, napita kuchipata, natuluka pomwepo; ndi mfumu yao yapita pamaso pao, ndipo Yehova awatsogolera. Ndipo akhumbira minda, nailanda; ngakhale nyumba, nazichotsa; asautsa mwamuna ndi nyumba yake, inde munthu ndi cholowa chake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 1:13-15

Munthu poyesedwa, asanena, Ndiyesedwa ndi Mulungu; pakuti Mulungu sangathe kuyesedwa ndi zoipa, ndipo Iye mwini sayesa munthu: koma munthu aliyense ayesedwa pamene chilakolako chake cha iye mwini chimkokera, ndikumnyenga. Pamenepo chilakolakocho chitaima, chibala uchimo; ndipo uchimo, utakula msinkhu, ubala imfa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 2:12-15

kukupulumutsa kunjira yoipa, kwa anthu onena zokhota; akusiya mayendedwe olungama, akayende m'njira za mdima; omwe asangalala pochita zoipa, nakondwera ndi zokhota zoipa; amene apotoza njira zao, nakhotetsa mayendedwe ao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:44

koma Ine ndinena kwa inu, Kondanani nao adani anu, ndi kupempherera iwo akuzunza inu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:26

Ziwembu zoipa zinyansa Yehova; koma oyera mtima alankhula mau okondweretsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 8:7-8

Chifukwa chisamaliro cha thupi chidana ndi Mulungu; pakuti sichigonja ku chilamulo cha Mulungu, pakuti sichikhoza kutero. Ndipo iwo amene ali m'thupi sangathe kukondweretsa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 6:27-28

Ndakuyesa iwe nsanja ndi linga mwa anthu anga, kuti udziwe ndi kuyesa njira yao. Onse ali opikisana ndithu, ayendayenda ndi maugogodi; ndiwo mkuwa ndi chitsulo; onsewa achita movunda;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 33:15-16

Iye amene ayenda molungama, nanena molunjika; iye amene anyoza phindu lonyenga, nasansa manja ake kusalandira zokometsera milandu, amene atseka makutu ake kusamva za mwazi, natsinzina maso ake kusayang'ana choipa; iye adzakhala pamsanje; malo ake ochinjikiza adzakhala malinga amiyala; chakudya chake chidzapatsidwa kwa iye; madzi ake adzakhala chikhalire.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 6:12-13

Chifukwa chake musamalola uchimo uchite ufumu m'thupi lanu la imfa kumvera zofuna zake: ndipo musapereke ziwalo zanu kuuchimo, zikhale zida za chosalungama; koma mudzipereke inu nokha kwa Mulungu, monga amoyo atatuluka mwa akufa, ndi ziwalo zanu kwa Mulungu zikhale zida za chilungamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 140:4-5

Ndilindireni Yehova, ndisalowe m'manja mwa woipa; ndisungeni kwa munthu wachiwawa; kwa iwo akuti akankhe mapazi anga. Odzikuza ananditchera msampha, nandibisira zingwe; anatcha ukonde m'mphepete mwa njira; ananditchera makwekwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 4:19

Njira ya oipa ikunga mdima; sadziwa chimene chiwaphunthwitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Atesalonika 3:3

Koma Ambuye ali wokhulupirika amene adzakukhazikitsani inu, nadzakudikirirani kuletsa woipayo;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 3:10-12

monga kwalembedwa, Palibe mmodzi wolungama, inde palibe mmodzi; palibe mmodzi wakudziwitsa, palibe mmodzi wakulondola Mulungu; onsewa apatuka, pamodzi akhala opanda pake; palibe mmodzi wakuchita zabwino, inde, palibe mmodzi ndithu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 13:6

Chilungamo chitchinjiriza woongoka m'njira; koma udyo ugwetsa wochimwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:13

Ndipo musatitengere kokatiyesa, koma mutipulumutse kwa woipayo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 73:27

Pakuti, taonani, iwo okhala patali ndi Inu adzaonongeka; muononga onse akupembedza kwina, kosiyana ndi Inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:4-5

Zonse Yehova anazipanga zili ndi zifukwa zao; ngakhale amphulupulu kuti aone tsiku loipa. Yense wonyada mtima anyansa Yehova; zoonadi sadzapulumuka chilango.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:21-23

Si yense wakunena kwa Ine, Ambuye, Ambuye, adzalowa mu Ufumu wa Kumwamba; koma wakuchitayo chifuniro cha Atate wanga wa Kumwamba. Ambiri adzati kwa Ine tsiku lomwelo, Ambuye, Ambuye, kodi sitinanenere mau m'dzina lanu, ndi m'dzina lanunso kutulutsa ziwanda, ndi kuchita m'dzina lanunso zamphamvu zambiri? Ndipo pamenepo ndidzafukulira iwo, Sindinakudziweni inu nthawi zonse; chokani kwa Ine, inu akuchita kusaweruzika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 29:27

Munthu woipa anyansa olungama; ndipo woongoka m'njira anyansa wochimwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 91:3

Pakuti adzakuonjola kumsampha wa msodzi, kumliri wosakaza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 5:19

Tidziwa kuti tili ife ochokera mwa Mulungu, ndipo dziko lonse lapansi ligona mwa woipayo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 97:10

Inu okonda Yehova, danani nacho choipa: Iye asunga moyo wa okondedwa ake; awalanditsa m'manja mwa oipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:9

Chikondano chikhale chopanda chinyengo. Dana nacho choipa; gwirizana nacho chabwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 3:19-20

Koma chiweruziro ndi ichi, kuti kuunika kunadza kudziko lapansi, ndipo anthu anakonda mdima koposa kuunika; pakuti ntchito zao zinali zoipa. Iyeyu anadza kwa Yesu usiku, nati kwa Iye, Rabi, tidziwa kuti Inu ndinu mphunzitsi wochokera kwa Mulungu; pakuti palibe munthu akhoza kuchita zizindikiro zimene Inu muchita, ngati Mulungu sakhala naye. Pakuti yense wakuchita zoipa adana nako kuunika, ndipo sakudza kwa kuunika, kuti zingatsutsidwe ntchito zake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 24:8-9

Wolingalira zakuchita zoipa anthu adzamtcha wachiwembu. Maganizo opusa ndiwo tchimo; wonyoza anyansa anthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 31:17-18

Yehova, musandichititse manyazi; pakuti ndafuulira kwa Inu, oipa achite manyazi, atonthole m'manda. Ikhale yosalankhula milomo ya mabodza, imene imalankhula mwachipongwe pa olungama mtima, ndi kudzikuza ndi kunyoza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 13:4

pakuti ndiye mtumiki wa Mulungu, kuchitira iwe zabwino. Koma ngati uchita choipa, opatu, pakuti iye sagwira lupanga kwachabe; pakuti ndiye mtumiki wa Mulungu wakukwiyira ndi kubwezera chilango wochita zoipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 21:7

Chiwawa cha amphulupulu chidzawakokolola; chifukwa akana kuchita chiweruzo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 13:49-50

Padzatero pa chimaliziro cha nthawi ya pansi pano: angelo adzatuluka, nadzawasankhula oipa pakati pa abwino, Koma zina zinagwa pamiyala, pamene panalibe dothi lambiri; ndipo pomwepo zinamera, pakuti sizinakhale nalo dothi lakuya. nadzawataya m'ng'anjo yamoto; komweko kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 5:23-24

amene alungamitsa woipa pa chokometsera mlandu, nachotsera wolungama chilungamo chake! Chifukwa chake monga ngati lilime la moto likutha chiputu, ndi monga udzu wouma ugwa pansi m'malawi, momwemo muzu wao udzakhala monga wovunda, maluwa ao adzauluka m'mwamba ngati fumbi; chifukwa kuti iwo akana chilamulo cha Yehova wa makamu, nanyoza mau a Woyera wa Israele.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 3:10-11

Pakuti, Iye wofuna kukonda moyo, ndi kuona masiku abwino, aletse lilime lake lisanene choipa, ndi milomo yake isalankhule chinyengo; ndipo apatuke pachoipa, nachite chabwino; afunefune mtendere ndi kuulondola.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:27

ndiponso musampatse malo mdierekezi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 10:29

Njira ya Yehova ndi linga kwa woongoka mtima; koma akuchita zoipa adzaonongeka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 101:4

Mtima wopulukira udzandichokera; sindidzadziwana naye woipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 36:12

Pomwepo padagwera ochita zopanda pake. Anawalikha, ndipo sadzatha kuukanso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:18-19

Kunyada kutsogolera kuonongeka; mtima wodzikuza ndi kutsogolera kuphunthwa. Kufatsa mtima ndi osauka kuposa kugawana zofunkha ndi onyada.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 91:10

palibe choipa chidzakugwera, ndipo cholanga sichidzayandikiza hema wako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye Mulungu, ndipangeni mtima woyera, ndipo mukonzenso mzimu wowongoka mkati mwanga. Atate wanga wakumwamba wokondedwa, ndidzichepetsa pamaso panu chifukwa ndikukusowani. Lero ndabwera kudzapempha chikhululukiro pa zoipa zanga zonse. Mundikhululukire chifukwa ndayenda m'njira yoipa ndipo mtima wanga wachita zoyipa pamaso panu. Ndikupemphani kuti mundisambitse ndi magazi anu Yesu, chifukwa ndikufuna kuti musinthe munthu wamkati wanga kukhala m'chifaniziro chanu. Mundidzaze tsiku lililonse ndi kukhalapo kwanu kotero kuti ndikhale m'chiyero chanu. Wongolereni mapazi anga ndipo mundiphunzitse chifuniro chanu chomwe chili chabwino, chokondweretsa, komanso changwiro. Ndithandizeni kuti ndisapatuke ku mawu anu nthawi iliyonse, koma kuti nthawi zonse ndizikhala kuti nditsatire malamulo ndi malangizo anu. Musandilole kutsata zilakolako za thupi langa kapena kuipa kwa mtima wanga. Khalani mwa ine Mzimu Woyera ndipo chikondi chanu chilamulire munthu wanga wonse kuti nthawi zonse ndizikhala ndi inu komanso chifukwa cha inu. M'dzina la Yesu, Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa