Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


104 Mau a m'Baibulo Okhudza Umbiri

104 Mau a m'Baibulo Okhudza Umbiri

Mtima wanga, uyenera kuugonjetsa nthawi zonse ku chifuniro cha Mulungu osati zilakolako ndi zokhumba zanga, chifukwa malingaliro amasinthasintha ndipo mzimu ungakhale wonyansa. Ndi bwino kuti Mzimu Woyera utsogolere mapazi anga onse.

Kupereka zolinga ndi mapulani anga kwa Mulungu ndiyo chinsinsi chachikulu cha chipambano changa, chifukwa Iye amadziwa tsogolo langa ndipo amadziwa chomwe chilidi chabwino kwa moyo wanga. Choncho, ndikofunikira kwambiri kusadalira nzeru zanga, koma kufunafuna chitsogozo Chake nthawi zonse, chifukwa, chifukwa cha uchimo wanga, nthawi zonse ndimakhala ndi chizolowezi chochita zinthu molakwika.

Nthawi ngati zimenezi, ndikofunikira kudzisamalira ku zinthu zonse zomwe sizikondweretsa Mulungu ndikupempha kuti andipatse mtima woyera pamaso pake. Ndikofunikiranso kupewa umbombo, chifukwa ndi tchimo pamaso pa Mulungu, ndipo pamapeto pake, umatitsogolera ku chiwonongeko, osatipindulitsa konse.

Umbombo ungawoneke wokongola poyamba, koma m'kupita kwa nthawi umasanduka chinthu chowawa chomwe tingafune kuti sitidayesepo. Choncho, ndi bwino kupempha Atate kuti afufuze mtima wanga nandipange kukhala munthu wangwiro, wolungama, ndi woyera, m'maganizo anga ndi zolinga zanga, kuti ndisangalale ndi moyo wanga wonse padziko lapansi.

Luka 12.15 amatikumbutsa kuti: "Ndipo anati kwa iwo, Samalani, mudzisunge ku umbombo; pakuti moyo wa munthu sukhala m'kuchuluka kwa chuma chake.”




Ahebri 13:5

Mtima wanu ukhale wosakonda chuma; zimene muli nazo zikukwanireni; pakuti Iye anati, Sindidzakusiya konse, kungakhale kukutaya, sindidzakutaya ndithu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 6:10

Pakuti muzu wa zoipa zonse ndiwo chikondi cha pa ndalama; chimene ena pochikhumba, anasochera, nataya chikhulupiriro, nadzipyoza ndi zowawa zambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:36

Lingitsani mtima wanga kumboni zanu, si ku chisiriro ai.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 12:15

Ndipo Iye anati kwa iwo, Yang'anirani, mudzisungire kupewa msiriro uliwonse; chifukwa moyo wake wa munthu sulingana ndi kuchuluka kwa zinthu zake ali nazo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:5

Chifukwa chake fetsani ziwalozo zili padziko; dama, chidetso, chifunitso chamanyazi, chilakolako choipa, ndi chisiriro, chimene chili kupembedza mafano;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 5:3

Koma dama ndi chidetso chonse, kapena chisiriro, zisatchulidwe ndi kutchulidwa komwe mwa inu, monga kuyenera oyera mtima;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:24

Palibe munthu angathe kukhala kapolo wa ambuye awiri: pakuti pena adzamuda mmodziyo, ndi kukonda winayo; pena adzakangamira kwa mmodzi, nadzanyoza wina. Simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa Chuma.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Petro 2:3

Ndipo m'chisiriro adzakuyesani malonda ndi mau onyenga; amene chiweruzo chao sichinachedwe ndi kale lomwe, ndipo chitayiko chao sichiodzera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 5:2

Wetani gulu la Mulungu lili mwa inu, ndi kuliyang'anira, osati mokakamiza, koma mwaufulu, kwa Mulungu; osatsata phindu lonyansa, koma mwachangu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 5:5

Pakuti ichi muchidziwe kuti wadama yense, kapena wachidetso, kapena wosirira, amene apembedza mafano, alibe cholowa mu ufumu wa Khristu ndi Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 28:6

Waumphawi woyenda mwangwiro apambana ndi yemwe akhotetsa njira zake, angakhale alemera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 5:10

Wokonda siliva sadzakhuta siliva; ngakhale wokonda chuma sadzakhuta phindu; ichinso ndi chabe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:27

Wopindula monyenga avuta nyumba yake; koma wakuda mitulo adzakhala ndi moyo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 8:10

Chifukwa chake ndidzapereka akazi ao kwa ena, ndi minda yao kwa iwo adzalowamo; pakuti onse kuyambira wamng'ono kufikira wamkulu asirirasirira; kuyambira mneneri kufikira wansembe onse achita zonyenga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 16:13

Palibe mnyamata wa m'nyumba akhoza kukhala kapolo wa ambuye awiri; pakuti kapena adzamuda wina, nadzakonda winayo; kapena adzatsata wina, nadzapeputsa winayo. Simungathe kukhala kapolo wa Mulungu ndi wa Chuma.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 28:22

Mwini diso lankhwenzule akangaza kulemera, osadziwa kuti umphawi udzamfikira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Petro 2:14

okhala nao maso odzala ndi chigololo, osakhoza kuleka uchimo, kunyengerera iwo a moyo wosakhazikika; okhala nao mtima wozolowera kusirira; ana a temberero;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 20:17

Usasirire nyumba yake ya mnzako, usasirire mkazi wake wa mnzako, kapena wantchito wake wa mwamuna, kapena wantchito wake wamkazi, kapena ng'ombe yake, kapena bulu wake, kapena kanthu kalikonse ka mnzako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 19:24

Ndiponso ndinena kwa inu, Nkwapafupi kuti ngamira ipyole diso la singano, koposa mwini chuma kulowa Ufumu wa Kumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 8:36

Pakuti munthu apindulanji akadzilemezera dziko lonse, natayapo moyo wake?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 11:24-25

Alipo wogawira, nangolemerabe; aliponso womana chomwe ayenera kupatsa nangosauka. Mtima wa mataya udzalemera; wothirira madzi nayenso adzathiriridwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 23:4

Usadzitopetse kuti ulemere; leka nzeru yakoyako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 21:6

Kupata chuma ndi lilime lonama ndiko nkhungu yoyendayenda, ngakhale misampha ya imfa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 6:10

kapena ambala, kapena osirira, kapena oledzera, kapena olalatira, kapena olanda, sadzalowa Ufumu wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 16:14-15

Koma Afarisi, ndiwo okonda ndalama, anamva izi zonse; ndipo anamseka. Ndipo anati kwa iwo, Inu ndinu odziyesera nokha olungama pamaso pa anthu; koma Mulungu azindikira mitima yanu; chifukwa ichi chimene chikuzika mwa anthu chili chonyansa pamaso pa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 10:3

Pakuti woipa adzitamira chifuniro cha moyo wake, adalitsa wosirira, koma anyoza Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mika 2:2

Ndipo akhumbira minda, nailanda; ngakhale nyumba, nazichotsa; asautsa mwamuna ndi nyumba yake, inde munthu ndi cholowa chake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 23:4-5

Usadzitopetse kuti ulemere; leka nzeru yakoyako. Kodi upenyeranji chimene kulibe? Pakuti chuma chimera mapiko, ngati mphungu youluka mumlengalenga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 6:13

Pakuti kuyambira wamng'ono kufikira wamkulu onse akhala akusirira; ndiponso kuyambira mneneri kufikira wansembe onse achita monyenga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 12:21

Atero iye wakudziunjikira chuma mwini yekha wosakhala nacho chuma cha kwa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 28:25

Wodukidwa mtima aputa makangano; koma wokhulupirira Yehova adzakula.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 2:16

Pakuti chilichonse cha m'dziko lapansi, chilakolako cha thupi ndi chilakolako cha maso, matamandidwe a moyo, sizichokera kwa Atate, koma kudziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 56:11

Inde agalu ali osusuka, sakhuta konse; amenewa ali abusa osazindikira; iwo onse atembenukira kunjira zao, yense kutsata phindu lake m'dera lake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 33:31

Ndipo akudzera monga amadzera anthu, nakhala pansi pamaso pako ngati anthu anga, namva mau ako, koma osawachita; pakuti pakamwa pao anena mwachikondi, koma mtima wao utsata phindu lao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 21:26

Ena asirira modukidwa tsiku lonse; koma wolungama amapatsa osamana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 4:8

Pali mmodzi palibe wachiwiri; inde, alibe mwana ngakhale mbale; koma ntchito yake yonse ilibe chitsiriziro, ngakhale diso lake silikhuta chuma. Samati, Ndigwira ntchito ndi kumana moyo wanga zabwino chifukwa cha yani? Ichinso ndi chabe, inde, vuto lalikulu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:19-21

Musadzikundikire nokha chuma padziko lapansi, pamene njenjete ndi dzimbiri ziononga; ndi pamene mbala ziboola ndi kuba: Chifukwa chake pamene paliponse upatsa mphatso zachifundo, usamaomba lipenga patsogolo pako, monga amachita onyenga m'masunagoge, ndi m'makwalala, kotero kuti atamandidwe ndi anthu. Indetu ndinena kwa inu, Iwo alandiriratu mphotho zao. koma mudzikundikire nokha chuma mu Mwamba, pamene njenjete kapena dzimbiri siziononga, ndipo mbala siziboola ndi kuba; pakuti kumene kuli chuma chako, komwe udzakhala mtima wakonso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 12:33-34

Gulitsani zinthu muli nazo, nimupatse mphatso zachifundo; mudzikonzere matumba a ndalama amene sakutha, chuma chosatha mu Mwamba, kumene mbala siziyandikira, ndipo njenjete siziononga. Pakuti kumene kuli chuma chanu, komweko kudzakhalanso mtima wanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:16

Wotsendereza waumphawi kuti achulukitse chuma chake, ndi wopatsa wolemera kanthu, angosauka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:11-12

Si kuti ndinena monga mwa chiperewero, pakuti ndaphunzira ine, kuti zindikwanire zilizonse ndili nazo. Ndadziwa ngakhale kupeputsidwa, ndadziwanso kusefukira; konseko ndi m'zinthu zonse ndalowa mwambo wakukhuta, ndiponso wakumva njala; wakusefukira, ndiponso wakusowa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 13:22

Ndipo iye amene afesedwa kuminga, uyu ndiye wakumva mau; ndipo kulabadira kwa dziko lapansi, ndi chinyengo cha chuma chitsamwitsa mau, ndipo akhala wopanda chipatso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 20:33-35

Sindinasirira siliva, kapena golide, kapena chovala cha munthu aliyense. Mudziwa inu nokha kuti manja anga awa anatumikira zosowa zanga, ndi za iwo akukhala ndi ine. M'zinthu zonse ndinakupatsani chitsanzo, chakuti pogwiritsa ntchito, kotero muyenera kuthandiza ofooka ndi kukumbuka mau a Ambuye Yesu, kuti anati yekha, Kupatsa kutidalitsa koposa kulandira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 3:2

Pakuti anthu adzakhala odzikonda okha, okonda ndalama, odzitamandira, odzikuza, amwano, osamvera akuwabala, osayamika,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 57:17

Chifukwa cha kuipa kwa kusirira kwake ndinakwiya ndi kummenya iye; ndinabisa nkhope yanga, ndipo ndinakwiya; ndipo iye anankabe mokhota m'njira ya mtima wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 11:28

Wokhulupirira chuma chake adzagwa; koma olungama adzaphuka ngati tsamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mlaliki 5:15

Monga anatuluka m'mimba ya amake, adzabweranso kupita wamaliseche, monga anadza osatenga kanthu pa ntchito zake, kakunyamula m'dzanja lake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:33

Koma muyambe mwafuna Ufumu wake ndi chilungamo chake, ndipo zonse zimenezo zidzaonjezedwa kwa inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 6:24

Koma tsoka inu eni chuma! Chifukwa mwalandira chisangalatso chanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 5:1-3

Nanga tsono achuma inu, lirani ndi kuchema chifukwa cha masautso anu akudza pa inu. Tengani, abale, chitsanzo cha kumva zowawa ndi kuleza mtima, aneneri amene analankhula m'dzina la Ambuye. Taonani tiwayesera odala opirirawo; mudamva za chipiriro cha Yobu, ndipo mwaona chitsiriziro cha Ambuye, kuti Ambuye ali wodzala chikondi, ndi wachifundo. Koma makamaka, abale anga, musalumbire, kungakhale kutchula kumwamba kapena dziko, kapena lumbiro lina lililonse; koma inde wanu akhale inde, ndi iai wanu akhale iai; kuti mungagwe m'chiweruziro. Kodi wina wa inu akumva zowawa? Apemphere. Kodi wina asekera? Aimbire. Pali wina kodi adwala mwa inu? Adziitanire akulu a Mpingo, ndipo apemphere pa iye, atamdzoza ndi mafuta m'dzina la Ambuye: ndipo pemphero la chikhulupiriro lidzapulumutsa wodwalayo, ndipo Ambuye adzamuukitsa; ndipo ngati adachita machimo adzakhululukidwa kwa iye. Chifukwa chake muvomerezane wina ndi mnzake machimo anu, ndipo mupempherere wina kwa mnzake kuti muchiritsidwe. Pemphero la munthu wolungama likhoza kwakukulu m'machitidwe ake. Eliya anali munthu wakumva zomwezi tizimva ife, ndipo anapemphera chipempherere kuti isavumbe mvula; ndipo siinagwe mvula padziko zaka zitatu kudza miyezi isanu ndi umodzi. Ndipo anapempheranso; ndipo m'mwamba munatsika mvula, ndi dziko lidabala zipatso zake. Abale anga, ngati wina wa inu asochera posiyana ndi choonadi, ndipo ambweza iye mnzake; Chuma chanu chaola ndi zovala zanu zajiwa ndi njenjete. azindikire, kuti iye amene abweza wochimwa kunjira yake yosochera adzapulumutsa munthu kwa imfa, ndipo adzavundikira machimo aunyinji. Golide wanu ndi siliva wanu zachita dzimbiri, ndipo dzimbiri lake lidzachita mboni zoneneza inu, ndipo zidzadya nyama yanu ngati moto. Mwadzikundikira chuma masiku otsiriza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 5:8

Tsoka kwa iwo amene aphatikiza nyumba ndi nyumba, amene alumikiza munda ndi munda, kufikira padzapanda malo, ndipo inu mudzasiyidwa nokha pakati padziko!

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 17:11

Monga nkhwali iumatira pa mazira amene sinaikire, momwemo iye amene asonkhanitsa chuma, koma mosalungama; pakati pa masiku ake chidzamsiya iye, ndipo pa chitsirizo adzakhala wopusa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 13:11

Chuma cholandiridwa mokangaza chidzachepa; koma wokundika ndi dzanja adzaona zochuluka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 18:24-25

Ndipo Yesu pomuona iye anati, Ha! Nkuvutika nanga kwa anthu eni chuma kulowa Ufumu wa Mulungu! Pakuti nkwapafupi kwa ngamira ipyole diso la singano koma kwa munthu mwini chuma, kulowa Ufumu wa Mulungu nkwapatali.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:25

Chifukwa chake ndinena kwa inu, Musadere nkhawa moyo wanu, chimene mudzadya ndi chimene mudzamwa; kapena thupi lanu, chimene mudzavala. Kodi moyo suli woposa chakudya, ndi thupi loposa chovala?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 2:3-4

musachite kanthu monga mwa chotetana, kapena monga mwa ulemerero wopanda pake, komatu ndi kudzichepetsa mtima, yense ayese anzake omposa iye mwini; pakuti chifukwa cha ntchito ya Khristu anafikira pafupi imfa, wosasamalira moyo wake, kuti akakwaniritse chiperewero cha utumiki wanu wa kwa ine. munthu yense asapenyerere zake za iye yekha, koma yense apenyererenso za mnzake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 10:34

Pakuti munamva chifundo ndi iwo a m'ndende, ndiponso mudalola mokondwera kulandidwa kwa chuma chanu, pozindikira kuti muli nacho nokha chuma choposa chachikhalire.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 9:7

Yense achite monga anatsimikiza mtima, si mwa chisoni kapena mokakamiza, pakuti Mulungu akonda wopereka mokondwerera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 14:31

Wotsendereza aumphawi atonza Mlengi wake; koma wochitira wosauka chifundo amlemekeza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 3:3

wosati woledzera, kapena womenyana ndeu; komatu wofatsa, wopanda ndeu, wosakhumba chuma;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 5:10-11

si konsekonse ndi achigololo a dziko lino lapansi, kapena ndi osirira, ndi okwatula, kapena ndi opembedza mafano; pakuti nkutero mukatuluke m'dziko lapansi; koma tsopano ndalembera inu kuti musayanjane naye, ngati wina wotchedwa mbale ali wachigololo, kapena wosirira, kapena wopembedza mafano, kapena wolalatira, kapena woledzera, kapena wolanda, kungakhale kukadya naye wotere, iai.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 1:29

anadzala ndi zosalungama zonse, kuipa, kusirira, dumbo; odzala ndi kaduka, mbanda, ndeu, chinyengo, udani;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:42

Kwa iye wopempha iwe umpatse, ndipo kwa iye wofuna kukukongola usampotolokere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 62:10

Musakhulupirire kusautsa, ndipo musatama chifwamba; chikachuluka chuma musakhazikepo mitima yanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 3:14

Ndipo asilikali omwe anamfunsa iye, nati, Nanga ife tizichita chiyani? Ndipo iye anati kwa iwo, Musaopse, musanamize munthu aliyense; khalani okhuta ndi kulipira kwanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 21:2-4

Ndipo Ahabu analankhula ndi Naboti, nati, Ndipatse munda wako wampesa ukhale munda wanga wa ndiwo, popeza uli pafupi ndi nyumba yanga; ndipo m'malo mwake ndidzakupatsa munda wampesa wokoma woposa uwu; kapena kukakukomera ndidzakupatsa ndalama za pa mtengo wake. Ndipo Ahabu anati kwa Eliya, Wandipeza kodi, mdani wangawe? Nayankha, Ndakupeza; pokhala wadzigulitsa kuchita choipacho pamaso pa Yehova. Taona, ndidzakufikitsira choipa, ndi kuchotsa mbumba yako psiti; ndipo ndidzalikhira Ahabu mwana wamwamuna yense, ndi yense womangika ndi womasuka mu Israele; ndipo ndidzalinganiza nyumba yako ndi nyumba ya Yerobowamu mwana wa Nebati, ndi ya Baasa mwana wa Ahiya; chifukwa cha kuputa kumene unaputa nako mkwiyo wanga, ndi kuchimwitsa Israele. Ndipo za Yezebele yemwe Yehova ananena, nati, Agalu adzadya Yezebele ku linga la Yezireele. Mwana aliyense wa Ahabu amene adzafera m'mzinda, agalu adzamudya; ndipo iye amene adzafera kuthengo, mbalame za m'mlengalenga zidzamudya. Koma panalibe wina ngati Ahabu wakudzigulitsa kuchita choipa pamaso pa Yehova, amene Yezebele mkazi wake anamfulumiza. Ndipo anachita moipitsitsa kutsata mafano, monga mwa zonse amazichita Aamori, amene Yehova adawapirikitsa pamaso pa ana a Israele. Ndipo kunali, pakumva Ahabu mau amenewa, anang'amba zovala zake, navala chiguduli pathupi pake, nasala kudya, nagona pachiguduli, nayenda nyang'anyang'a. Pamenepo mau a Yehova anadza kwa Eliya wa ku Tisibe, nati, Waona umo wadzichepetsera Ahabu pamaso panga? Popeza adzichepetsa pamaso panga, sindidzafikitsa choipa chimenechi akali moyo iye; koma m'masiku a mwana wake ndidzachifikitsa pa nyumba yake. Ndipo Naboti anati kwa Ahabu, Pali Yehova, ndi pang'ono ponse ai, kuti ndikupatseni cholowa cha makolo anga. Ndipo Ahabu analowa m'nyumba mwake wamsunamo ndi wokwiya, chifukwa cha mau amene Naboti wa ku Yezireele adalankhula naye; popeza adati, Sindikupatsani cholowa cha makolo anga. M'mwemo anagona pa kama wake, nayang'ana kumbali, nakana kudya mkate.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 22:12

Analandira mphotho mwa iwe kukhetsa mwazi, walandira phindu loonjezerapo, wanyengerera anansi ako ndi kuwazunza, ndipo wandiiwala Ine, ati Ambuye Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 9:25

Pakuti munthu apindulanji, akadzilemezera dziko lonse lapansi nadzitayapo, kapena kulipapo moyo wake?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 2:2-4

Pakuti akalowa m'sunagoge mwanu munthu wovala mphete yagolide, ndi chovala chokometsetsa, ndipo akalowanso munthu wosauka ndi chovala chodetsa; Koma ufuna kuzindikira kodi, munthu wopanda pake iwe, kuti chikhulupiriro chopanda ntchito chili chabe? Abrahamu kholo lathu, sanayesedwe wolungama ndi ntchito kodi, paja adapereka mwana wake Isaki nsembe paguwa la nsembe? Upenya kuti chikhulupiriro chidachita pamodzi ndi ntchito zake, ndipo motuluka mwa ntchito chikhulupiriro chidayesedwa changwiro; ndipo anakwaniridwa malembo onenawa, Ndipo Abrahamu anakhulupirira Mulungu, ndipo kudawerengedwa kwa iye chilungamo; ndipo anatchedwa bwenzi la Mulungu. Mupenya kuti munthu ayesedwa wolungama ndi ntchito yake, osati ndi chikhulupiriro chokha. Ndipo momwemonso sanayesedwe wolungama Rahabu mkazi wa damayo ndi ntchito kodi, popeza adalandira amithenga, nawatulutsa adzere njira ina? Pakuti monga thupi lopanda mzimu lili lakufa, koteronso chikhulupiriro chopanda ntchito chili chakufa. ndipo mukapenyerera iye wovala chokometsetsa, nimukati naye, Inu mukhale apa pabwino; ndipo mukati kwa wosaukayo, Iwe, imauko, kapena, khala pansi pa mpando wa mapazi anga; kodi simunasiyanitse mwa inu nokha, ndi kukhala oweruza oganizira zoipa?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 22:7

Wolemera alamulira osauka; ndipo wokongola ndiye kapolo wa womkongoletsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yobu 20:20-21

Popeza sanadziwe kupumula m'kati mwake, sadzalanditsa kanthu ka zofunika zake. Sikunatsalira kanthu kosadya iye, chifukwa chake zokoma zake sizidzakhalitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 5:21

Usasirire mkazi wake wa mnzako; usakhumbe nyumba yake ya mnzako, munda wake, kapena wantchito wake wamwamuna, kapena wantchito wake wamkazi, ng'ombe yake, kapena bulu wake, kapena kanthu kalikonse ka mnzako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 2:5

Pakuti sitinayende nao mau osyasyalika nthawi iliyonse monga mudziwa, kapena kupsinjika msiriro, mboni ndi Mulungu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:8

Zapang'ono, pokhala chilungamo, ziposa phindu lalikulu lopanda chiweruzo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 10:24

Munthu asafune zake za iye yekha, koma za mnzake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 49:6-7

Iwo akutama kulemera kwao; nadzitamandira pa kuchuluka kwa chuma chao; kuombola mbale sangadzamuombole, kapena kumperekera dipo kwa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mafumu 5:20-27

Koma Gehazi, mnyamata wa Elisa, munthu wa Mulungu, anati, Taona, mbuye wanga analekera Naamani uyu wa ku Aramu osalandira m'manja ake chimene anabwera nacho; pali Yehova, ndidzathamangira ndi kulandira kanthu kwa iye. Motero Gehazi anatsata Naamani. Ndipo pamene Naamani anaona wina alikumthamangira, anatsika pagaleta kukomana naye, nati, Nkwabwino kodi? Nati, Kuli bwino. Mbuye wanga wandituma, ndi kuti, Taonani, andifikira tsopano apa anyamata awiri a ana a aneneri, ochokera ku mapiri a Efuremu; muwapatse talente wa siliva, ndi zovala zosintha ziwiri. Nati Naamani, Ulole ulandire matalente awiri. Namkakamiza namanga matalente awiri a siliva m'matumba awiri, ndi zovala zosintha ziwiri, nasenzetsa anyamata ake awiri; iwo anatsogola atazisenza. Ndipo pamene anafika kumsanje anazilandira m'manja mwao, naziika m'nyumba; nauza anthuwo amuke, iwo nachoka. Pamenepo analowa, naima kwa mbuye wake. Ndipo Elisa ananena naye, Ufuma kuti Gehazi? Nati, Ngati mnyamata wanu wayenda konse? Ndipo anati kwa iye, Mtima wanga sunakuperekeze kodi, umo munthuyo anatembenuka pa galeta wake kukomana ndi iwe? Kodi nyengo ino ndiyo yakulandira siliva, ndi kulandira zovala, ndi minda ya azitona, ndi yampesa, ndi nkhosa, ndi ng'ombe, ndi akapolo, ndi adzakazi? Chifukwa chake khate la Naamani lidzakumamatira iwe ndi mbumba yako chikhalire. Ndipo anatuluka pamaso pake wakhate wa mbuu ngati chipale chofewa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 14:28-30

Pakuti ndani wa inu amene akafuna kumanga nsanja yaitali, sayamba wakhala pansi, nawerengera mtengo wake, aone ngati ali nazo zakuimaliza? Kuti kungachitike, pamene atakhazika pansi miyala ya kumaziko ake, osakhoza kuimaliza anthu onse akuyang'ana adzayamba kumseka iye, Ndipo Yesu anayankha nati kwa achilamulo ndi Afarisi, nanena, Kodi nkuloledwa tsiku la Sabata kuchiritsa, kapena iai? ndi kunena kuti, Munthu uyu anayamba kumanga, koma sanathe kumaliza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 1:19

Mayendedwe a yense wopindula chuma monyenga ngotere; chilanda moyo wa eni ake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 19:21-22

Yesu ananena naye, Ngati ufuna kukhala wangwiro, pita, kagulitse zomwe uli nazo, nupatse aumphawi, ndipo udzakhala ndi chuma Kumwamba; ndipo ukadze kuno, unditsate. Koma mnyamatayo m'mene anamva chonenacho, anamuka wachisoni; pakuti anali nacho chuma chambiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 4:2-3

Mulakalaka, ndipo zikusowani; mukupha, nimuchita kaduka, ndipo simungathe kupeza; mulimbana, nimuchita nkhondo; mulibe kanthu, chifukwa simupempha. Mupempha, ndipo simulandira, popeza mupempha koipa, kuti mukachimwaze pochita zikhumbitso zanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:16

Zapang'ono, ulikuopa Yehova, zipambana ndi katundu wambiri pokhala phokoso.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 10:40-42

Koma Marita anatekeseka ndi kutumikira kwambiri; ndipo anadzako nati, Ambuye, kodi simusamala kuti mbale wanga anandisiya nditumikire ndekha? Mumuuze tsono kuti andithandize. Koma Ambuye anayankha nati kwa iye, Marita, Marita, uda nkhawa nuvutika ndi zinthu zambiri; koma chisoweka chinthu chimodzi, pakuti Maria anasankha dera lokoma limene silidzachotsedwa kwa iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 7:19

Adzataya siliva wao kumakwalala, nadzayesa golide wao chinthu chodetsedwa; siliva wao ndi golide wao sadzakhoza kuwalanditsa tsiku la mkwiyo wa Yehova, sadzakwaniritsa moyo wao, kapena kudzaza matumbo ao; pakuti izi ndi chokhumudwitsa cha mphulupulu zao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 5:1-10

Koma munthu wina dzina lake Ananiya pamodzi ndi Safira mkazi wake, Ndipo anagwa pansi pomwepo pa mapazi ake, namwalira; ndipo analowa anyamatawo, nampeza iye wafa, ndipo anamnyamula kutuluka naye, namuika kwa mwamuna wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 30:7-9

Zinthu ziwiri ndakupemphani, musandimane izo ndisanamwalire: Mundichotsere kutali zachabe ndi mabodza; musandipatse umphawi, ngakhale chuma, mundidyetse zakudya zondiyenera; ndingakhute ndi kukukanani, ndi kuti, Yehova ndani? Kapena ndingasauke ndi kuba, ndi kutchula dzina la Mulungu wanga pachabe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 8:12

Pakuti ngati chivomerezocho chili pomwepo, munthu alandiridwa monga momwe ali nacho, si monga chimsowa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yobu 31:24-25

Ngati ndayesa golide chiyembekezo changa, ndi kunena ndi golide woyengetsa, ndiwe chikhazikitso changa; ngati ndinakondwera popeza chuma changa nchachikulu, ndi dzanja langa lapeza zochuluka;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:16

Mukhale ndi mtima umodzi wina ndi mnzake. Musasamalire zinthu zazikulu, koma phatikanani nao odzichepetsa. Musadziyesere anzeru mwa inu nokha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 22:21

Nanena iwo, Cha Kaisara. Pomwepo Iye anati kwa iwo, Chifukwa chake patsani kwa Kaisara zake za Kaisara, ndi kwa Mulungu zake za Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 21:17

Wokonda zoseketsa adzasauka; wokonda vinyo ndi mafuta sadzalemera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 11:39-41

Koma Ambuye anati kwa iye, Tsopano inu Afarisi muyeretsa kunja kwake kwa chikho ndi mbale, koma m'kati mwanu mudzala zolanda ndi zoipa. Ndipo mutikhululukire ife machimo athu; pakuti ifenso tikhululukira munthu yense wa mangawa athu. Ndipo musatitengere ife kokatiyesa. Opusa inu, kodi Iye wopanga kunja kwake sanapangenso m'kati mwake? Koma patsani mphatso yachifundo za m'katimo; ndipo onani, zonse zili zoyera kwa inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 18:21

Koma iwe, dzisankhire mwa anthu ako onse, amuna anzeru, akuopa Mulungu, amuna oona, akudana nalo phindu la chinyengo; nuwaikire iwo oterewa, akulu a pa zikwi, akulu a pa mazana, akulu a pa makumi asanu, akulu a pa makumi;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 19:22

Chotikondetsa munthu ndicho kukoma mtima kwake; ndipo wosauka apambana munthu wonama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 6:10

monga akumva chisoni, koma akukondwera nthawi zonse; monga aumphawi, koma akulemeretsa ambiri; monga okhala opanda kanthu, ndipo akhala nazo zinthu zonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 4:19

Koma Mulungu wanga adzakwaniritsa chosowa chanu chilichonse monga mwa chuma chake mu ulemerero mwa Khristu Yesu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 3:11-13

Ndipo Mulungu anati kwa iye, Popeza wapempha chimenechi, osadzipemphera masiku ambiri, osadzipempheranso chuma, osadzipempheranso moyo wa adani ako, koma wadzipemphera nzeru zakumvera milandu; taona, ndachita monga mwa mau ako; taona ndakupatsa mtima wanzeru ndi wakuzindikira, kotero kuti panalibe wina wolingana ndi iwe kale, ndipo sadzakhalanso wina wolingana ndi iwe utamuka. Ndiponso zimene sunazipemphe adakupatsa, ndipo chuma ndi ulemu, kuti pakati pa mafumu sipadzakhala ina yolingana ndi iwe masiku ako onse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:3

Odala ali osauka mumzimu; chifukwa uli wao Ufumu wa Kumwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 10:2

Chuma cha uchimo sichithangata; koma chilungamo chipulumutsa kuimfa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 8:18-20

Koma pakuona Simoni kuti mwa kuika manja a atumwi anapatsidwa Mzimu Woyera, anawatengera ndalama, nanena, Ndipatseni inenso ulamuliro umene, kuti aliyense amene ndikaika manja pa iye, alandire Mzimu Woyera. Ndipo anamuika Stefano anthu opembedza, namlira maliro aakulu. Koma Petro anati kwa iye, Ndalama yako itayike nawe, chifukwa unalingirira kulandira mphatso ya Mulungu ndi ndalama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 4:5-8

Ndipo m'mene anamtsogolera anakwera naye, namuonetsa Iye maufumu onse a dziko lokhalamo anthu, m'kamphindi kakang'ono. Ndipo mdierekezi anati kwa Iye, Ine ndidzapatsa Inu ulamuliro wonse umenewu ndi ulemerero wao: chifukwa unaperekedwa kwa ine; ndipo ndiupatsa kwa iye amene ndifuna. Chifukwa chake ngati Inu mudzagwadira pamaso panga, wonsewo udzakhala wanu. Ndipo Yesu anayankha, nati kwa iye, Kwalembedwa, kuti, Ambuye Mulungu wako uzimgwadira, ndipo Iye yekhayekha uzimtumikira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mbiri 1:11-12

Ndipo Mulungu anati kwa Solomoni, Popeza chinali mumtima mwako ichi, osapempha chuma, akatundu, kapena ulemu, kapena moyo wa iwo akudana nawe, osapemphanso masiku ambiri; koma wadzipemphera nzeru ndi chidziwitso, kuti uweruze anthu anga amene ndakuika ukhale mfumu yao, nzeru ndi chidziwitso zipatsidwa kwa iwe, ndidzakupatsanso chuma, ndi akatundu, ndi ulemu, zotere zonga sanakhale nazo mafumu akale usanakhale iwe, ndi akudza pambuyo pako sadzakhala nazo zotero.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 3:17-18

Koma iye amene ali nacho chuma cha dziko lapansi, naona mbale wake ali wosowa ndi kutsekereza chifundo chake pommana iye, nanga chikondi cha Mulungu chikhala mwa iye bwanji? Tiana, tisakonde ndi mau, kapena ndi lilime, komatu ndi kuchita ndi m'choonadi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 25:14-30

Pakuti monga munthu, wakunka ulendo, aitana akapolo ake, napereka kwa iwo chuma chake. Ndipo mmodzi anampatsa ndalama za matalente zisanu, ndi wina ziwiri, ndi wina imodzi; kwa iwo onse monga nzeru zao; namuka iye. Pomwepo uyo amene analandira matalente asanu, anapita kugula nazo malonda, napindulapo matalente ena asanu. Chimodzimodzi uyo wa awiriwo, anapindulapo ena awiri. Koma uyo amene analandira imodziyo anamuka, nakumba pansi, naibisa talente ya mbuye wake. Ndipo itapita nthawi yaikulu, anabwera mbuye wa akapolo awo, nawerengera nao pamodzi. Ndipo asanu a iwo anali opusa, ndi asanu anali ochenjera. Ndipo uyo amene adalandira matalente asanu anadza, ali nawo matalente ena asanu, nanena, Mbuye, munandipatsa matalente asanu, onani ndapindulapo matalente ena asanu. Mbuye wake anati kwa iye, Chabwino, kapolo iwe wabwino ndi wokhulupirika; unali wokhulupirika pa zinthu zazing'ono, ndidzakhazika iwe pa zinthu zambiri; lowa iwe m'chikondwerero cha mbuye wako. Ndipo wa matalente awiriwo anadzanso, nati, Mbuye, munandipatsa ine matalente awiri; onani, ndapindulapo matalente ena awiri. Mbuye wake anati kwa iye, Chabwino, kapolo iwe wabwino ndi wokhulupirika; unali wokhulupirika pa zinthu zazing'ono, ndidzakhazika iwe pa zinthu zambiri; lowa iwe m'chikondwerero cha mbuye wako. Ndipo uyonso amene analandira talente imodzi, anadza, nati, Mbuye, ndinakudziwani inu kuti ndinu munthu wouma mtima, wakututa kumene simunafese, ndi wakusonkhanitsa kumene simunawaze; ndinaopa ine, ndinapita, ndinabisa pansi talente yanu: onani, siyi talente yanuyo. Koma mbuye wake anayankha, nati kwa iye, Kapolo iwe woipa ndi waulesi, unadziwa kuti ndimatuta kumene sindinafese, ndi kusonkhanitsa kumene sindinawaze; chifukwa chake ukadapereka ndalama zanga kwa okongola ndalama, ndipo ine pobwera ndikadatenga zanga ndi phindu lake. Chifukwa chake chotsani kwa iye ndalamayo, muipatse kwa amene ali nazo ndalama khumi. Pakuti kwa yense amene ali nazo, kudzapatsidwa, ndipo iye adzakhala nazo zochuluka: koma kwa iye amene alibe, kudzachotsedwa, chingakhale chimene anali nacho. Pakuti opusawo, m'mene anatenga nyali zao, sanadzitengerenso mafuta; Ndipo ponyani kapoloyo wopanda pake kumdima wakunja; kumene kudzakhala kulira ndi kukukuta mano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Mulungu ndi woyera, ndi wamuyaya, woyenera ulemerero wonse. Kwa Inu Ambuye Yesu ulemu ukhale kosatha, chifukwa chachikulu chandikomera ine. Mwandionetsa kukoma mtima kwanu kosatha ndi chikondi chanu. Zikomo chifukwa chokhala nane nthawi zonse ndi kundithandiza. Ndimakulambirani chifukwa ndinu mphamvu yanga, mtendere wanga, ndi malo anga obisalira. Mzimu Woyera, ndidzipereka pamaso panu, ndipo ndikubweretsa zolakwa zanga zonse pamaso panu. Ndikudziwa kuti ndili ndi zofooka zambiri, ndipo chifukwa chake ndikukupemphani kuti mukhale olimba mwa ine. Mundilanditse ku mayesero onse, musalole mapazi anga kutsata umbombo. Yeretsani mtima wanga ku chilakolako chilichonse chomwe sichichokera kwa Inu, chifukwa ndikufuna kuchita chifuniro chanu changwiro nthawi zonse. Ndidzipereka kudikira mawu anu, osati kuchita mwamsanga chilichonse chomwe sichili m'cholinga chanu pa ine. Ndikupereka moyo wanga ndi mtima wanga kwa Inu. Ndili m'manja mwanu Yesu, mundipange monga momwe mukufunira, ndipo mundisinthe kukhala munthu watsopano. M'dzina la Yesu, Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa