Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 19:24 - Buku Lopatulika

24 Ndiponso ndinena kwa inu, Nkwapafupi kuti ngamira ipyole diso la singano, koposa mwini chuma kulowa Ufumu wa Kumwamba.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

24 Ndiponso ndinena kwa inu, Nkwapafupi kuti ngamira ipyole diso la singano, koposa mwini chuma kulowa Ufumu wa Kumwamba.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

24 Ndipo ndikunenetsanso kuti nkwapafupi kuti ngamira idzere pa kachiboo ka zingano, kupambana kuti munthu wolemera akaloŵe mu Ufumu wa Mulungu.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

24 Komanso ndikuwuzani kuti, nʼkwapafupi kuti ngamira idzere pa kabowo ka zingano kusiyana ndi kuti wolemera akalowe mu ufumu wa Mulungu.”

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 19:24
9 Mawu Ofanana  

Kodi angathe Mkusi kusanduliza khungu lake, kapena nyalugwe mawanga ake? Pamenepo mungathe inunso kuchita zabwino, inu amene muzolowera kuchita zoipa.


Ndipo ophunzira, pamene anamva, anazizwa kwambiri, nanena, Ngati nkutero angapulumuke ndani?


Ndipo Yesu anawayang'ana, nati kwa iwo, Ichi sichitheka ndi anthu, koma zinthu zonse zitheka ndi Mulungu.


Atsogoleri akhungu inu, akukuntha udzudzu, koma mumeza ngamira.


Pakuti nkwapafupi kwa ngamira ipyole diso la singano koma kwa munthu mwini chuma, kulowa Ufumu wa Mulungu nkwapatali.


Yesu anayankha nati kwa iye, Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, Ngati munthu sabadwa mwatsopano, sangathe kuona Ufumu wa Mulungu.


Yesu anayankha, Indetu, indetu, ndinena ndi iwe, Ngati munthu sabadwa mwa madzi ndi Mzimu, sangathe kulowa ufumu wa Mulungu.


Mungathe inu bwanji kukhulupirira, popeza mulandira ulemu wina kwa mnzake ndipo ulemu wakuchokera kwa Mulungu yekha simuufuna?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa