Yeremiya 8:10 - Buku Lopatulika10 Chifukwa chake ndidzapereka akazi ao kwa ena, ndi minda yao kwa iwo adzalowamo; pakuti onse kuyambira wamng'ono kufikira wamkulu asirirasirira; kuyambira mneneri kufikira wansembe onse achita zonyenga. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201410 Chifukwa chake ndidzapereka akazi ao kwa ena, ndi minda yao kwa iwo adzalowamo; pakuti onse kuyambira wamng'ono kufikira wamkulu asirirasirira; kuyambira mneneri kufikira wansembe onse achita zonyenga. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa10 Nchifukwa chake akazi ao ndidzaŵapatsa kwa anthu ena, minda yao ndidzaipereka kwa amene aŵagonjetsa. Ndithudi, kuyambira ana ndi akulu omwe, onsewo ali ndi khwinthi la phindu lopeza monyenga. Aneneri ndi ansembe omwe, onsewo ndi onyenga. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero10 Nʼchifukwa chake akazi awo ndidzawapereka kwa amuna ena ndipo minda yawo ndidzayipereka kwa amene adzawagonjetse. Kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu, onse ali ndi khalidwe lofuna kupeza chuma mwakuba. Aneneri pamodzi ndi ansembe omwe, onse amachita zachinyengo. Onani mutuwo |