Mlaliki 4:8 - Buku Lopatulika8 Pali mmodzi palibe wachiwiri; inde, alibe mwana ngakhale mbale; koma ntchito yake yonse ilibe chitsiriziro, ngakhale diso lake silikhuta chuma. Samati, Ndigwira ntchito ndi kumana moyo wanga zabwino chifukwa cha yani? Ichinso ndi chabe, inde, vuto lalikulu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20148 Pali mmodzi palibe wachiwiri; inde, alibe mwana ngakhale mbale; koma ntchito yake yonse ilibe chitsiriziro, ngakhale diso lake silikhuta chuma. Samati, Ndigwira ntchito ndi kumana moyo wanga zabwino chifukwa cha yani? Ichinso ndi chabe, inde, vuto lalikulu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa8 Panali munthu amene anali yekha, wopanda mwana kapena mbale, komabe ntchito yake yolemetsa sinkatha. Maso ake sankakhutitsidwa nacho chuma chake. Motero sankadzifunsa konse kuti, “Kodi ntchito yolemetsa ndikuigwirayi ndiponso mavuto a kudzimana zokondweretsaŵa, ndikuchitira yani?” Zimenezi nzopanda phindu ndiponso nzosakondweretsa. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero8 Panali munthu amene anali yekhayekha; analibe mwana kapena mʼbale. Ntchito yake yolemetsa sinkatha, ndipo maso ake sankakhutitsidwa ndi chuma chake. Iye anadzifunsa kuti, “Kodi ntchito yosautsayi ndikuyigwirira yani? Nanga nʼchifukwa chiyani ndikudzimana chisangalalo?” Izinso ndi zopandapake, zosasangalatsa! Onani mutuwo |