Mwambi 17:15 umati: “Wokhululukira woipa ndi wotsutsa wolungama, onse awiri ndi onyansa kwa Ambuye.” Mulungu amadana ndi onse okhululukira ochimwa ndi otsutsa olungama ndipo amatiwonetsa kuti chilungamo chake sichikhala ndi tsankho kapena ziphuphu, koma chimafuna nthawi zonse chilungamo ndi chiweruzo choyenera, chifukwa Iye ndi wolungama m'njira zake zonse.
Mu buku la Yesaya 1:17, Mulungu akutiitana kuti tichite motsutsana ndi chisalungamo: “Phunzirani kuchita zabwino; funani chiweruzo; tsimikizirani woponderezedwa; weruzani mlandu wa mwana wamasiye; tetezani mkazi wamasiye.” Mawu awa akutilimbikitsa kukhala anthu osintha zinthu ndi kulimbana ndi chisalungamo m'njira zonse, osati m'mawu okha, komanso m'machitidwe athu. Chisalungamo ndi vuto lomwe limakhudza anthu ambiri padziko lonse lapansi, motero tiyenera kupemphera kwa Mulungu kuti atichotse ku machimo onse ndi chisalungamo.
Mu buku la Mika 6:8, tikukumbutsidwa kuti: “Iye wakudziwitsa, iwe munthu, chokoma; ndipo Yehova afunanji ndi iwe, koma kuchita chilungamo, ndi kukonda chifundo, ndi kuyenda modzichepetsa ndi Mulungu wako?” Monga Akhristu, ndi udindo wathu kutsatira chitsanzo cha Yesu ndi kudzipereka kukhala zida za chilungamo m'dziko lomwe nthawi zambiri limasowa chilungamo.
Ndikofunika kukumbukira kuti chilungamo sichili m'manja mwathu, koma m'manja mwa Mulungu. Tiyenera kudalira ulamuliro wake ndi kufunafuna chitsogozo chake polimbana ndi chisalungamo.
Ambuye adziwa kupulumutsa opembedza poyesedwa iwo, ndi kusunga osalungama kufikira tsiku loweruza akalangidwe;
Wokometsa mlandu wa wamphulupulu, ndi wotsutsa wolungama, onse awiriwa amnyansa Yehova.
Iye anakuuza, munthuwe, chomwe chili chokoma; ndipo Yehova afunanji nawe koma kuti uchite cholungama, ndi kukonda chifundo ndi kuyenda modzichepetsa ndi Mulungu wako.
Musamachita chisalungamo poweruza mlandu, poyesa utali wake, kulemera kwake, kapena kuchuluka kwake.
phunzirani kuchita zabwino; funani chiweruzo; thandizani osautsidwa, weruzirani ana amasiye, munenere akazi amasiye.
Tsoka kwa iwo amene alamulira malamulo osalungama, ndi kwa alembi olemba mphulupulu; Popeza dzanja langa lapeza maufumu a mafano, mafano ao osema anapambana ndi iwo a ku Yerusalemu ndi ku Samariya; monga ndachitira Samariya ndi mafano ake, momwemo kodi sindidzachitira Yerusalemu ndi mafano ake? Chifukwa chake padzaoneka, kuti pamene Ambuye atatha ntchito yake yonse paphiri la Ziyoni ndi pa Yerusalemu, ndidzalanga zipatso za mtima wolimba wa mfumu ya Asiriya, ndi ulemerero wa maso ake okwezedwa. Popeza anati, Mwa mphamvu ya dzanja langa ndachita ichi, ndi mwa nzeru yanga; pakuti ine ndili wochenjera; ndachotsa malekezero a anthu, ndalanda chuma chao, ndagwetsa monga munthu wolimba mtima iwo okhala pa mipando yachifumu; dzanja langa lapeza monga chisa, chuma cha mitundu ya anthu, ndipo monga munthu asonkhanitsa mazira osiyidwa, ine ndasonkhanitsa dziko lonse lapansi, ndipo panalibe chogwedeza phiko, kapena chotsegula pakamwa, kapena cholira pyepye. Kodi nkhwangwa idzadzikweza yokha, pa iye amene adula nayo? Kodi chochekera chidzadzikweza chokha pa iye amene achigwedeza, ngati chibonga ingamgwedeze iye amene ainyamula, ngati ndodo inganyamule kanthu popeza ili mtengo. Chifukwa chake Ambuye, Yehova wa makamu, adzatumiza kuonda mwa onenepa ake; ndipo pansi pa ulemerero wake padzayaka kutentha, konga ngati kutentha kwa moto. Ndipo kuwala kwa Israele kudzakhala moto, ndi Woyera wake adzakhala lawi; ndipo lidzatentha ndi kuthetsa minga yake ndi lunguzi wake tsiku limodzi. Ndipo adzanyeketsa ulemerero wa m'nkhalango yake, ndi wa m'munda wake wopatsa bwino, moyo ndi thupi; ndipo padzakhala monga ngati pokomoka wonyamula mbendera. Ndipo mitengo yotsala ya m'nkhalango yake idzakhala yowerengeka, kuti mwana ailembera. kuwapatulira osowa kuchiweruziro, ndi kuchotsera anthu anga aumphawi zoyenera zao, kuti alande za akazi amasiye, nafunkhire ana amasiye!
Zilipo zinthu zisanu ndi chimodzi Yehova azida; ngakhale zisanu ndi ziwiri zimnyansa: Maso akunyada, lilime lonama, ndi manja akupha anthu osachimwa; mtima woganizira ziwembu zoipa, mapazi akuthamangira mphulupulu m'mangum'mangu; mboni yonama yonong'ona mabodza, ndi wopikisanitsa abale.
Weruzani osauka ndi amasiye; weruzani molungama ozunzika ndi osowa. Pulumutsani osauka ndi aumphawi; alanditseni m'dzanja la oipa.
Mundiweruzire, Mulungu, ndipo mundinenere mlandu kwa anthu opanda chifundo. Mundilanditse kwa munthu wonyenga ndi wosalungama.
Imvani, Mulungu wathu, popeza tanyozeka ife; muwabwezere chitonzo chao pamtu pao, ndi kuwapereka akhale chofunkhidwa m'dziko la ndende; ndipo musakwirira mphulupulu yao, ndi kulakwa kwao kusafafanizike pamaso panu; pakuti anautsa mkwiyo wanu pamaso pa omanga linga.
Siyana nacho choipa, nuchite chokoma, nukhale nthawi zonse. Pakuti Yehova akonda chiweruzo, ndipo sataya okondedwa ake. Asungika kosatha, koma adzadula mbumba za oipa. Olungama adzalandira dziko lapansi, nadzakhala momwemo kosatha.
Chifukwa cha kupasuka kwa ozunzika, chifukwa cha kuusa moyo kwa aumphawi, ndiuka tsopano, ati Yehova; ndidzamlonga mosungika muja alakalakamo.
Tsegula pakamwa pako, ukanenere wosalankhula, ndi mlandu wa amasiye onse. Tsegula pakamwa pako nuweruze molungama, nunenere osauka ndi aumphawi.
popeza nkolungama kwa Mulungu kubwezera chisautso kwa iwo akuchitira inu chisautso, ndi kwa inu akumva chisautso mpumulo pamodzi ndi ife, pa vumbulutso la Ambuye Yesu wochokera Kumwamba pamodzi ndi angelo a mphamvu yake,
Kondwera pa iye, m'mwamba iwe, ndi oyera mtima, ndi atumwi, ndi aneneri inu; chifukwa Mulungu anauweruzira kuweruzidwa kwanu.
Aleksandro wosula mkuwa anandichitira zoipa zambiri: adzambwezera iye Ambuye monga mwa ntchito zake;
Musamapotoza chiweruzo, musamasamalira munthu, kapena kulandira chokometsera mlandu; popeza chokometsera mlandu chidetsa maso a anzeru, ndi kuipisa mau a olungama.
Pakuti Ine Yehova ndikonda chiweruziro, ndida chifwamba ndi choipa; ndipo ndidzawapatsa mphotho yao m'zoonadi; ndipo ndidzapangana nao pangano losatha.
Yehova atero: Chitani chiweruzo ndi chilungamo, landitsani ofunkhidwa m'dzanja la wosautsa; musachite choipa, musamchitire mlendo chiwawa, kapena ana amasiye, kapena akazi amasiye, musakhetse mwazi wosachimwa pamalo pano.
Popeza tsono mupondereza aumphawi, ndi kumsonkhetsa tirigu; mwamanga nyumba za miyala yosema, koma simudzakhala m'mwemo; mwaoka minda ya mipesa yokonda, koma simudzamwa vinyo wake. Pakuti ndidziwa kuti zolakwa zanu nzochuluka, ndi machimo anu ndi olimba, inu akusautsa olungama, akulandira chokometsera mlandu, akukankha osowa kuchipata.
Yehova, mwamva chikhumbo cha ozunzika, mudzakhazikitsa mtima wao, mudzatchereza khutu lanu; kuti muweruze mlandu wa amasiye ndi wokhalira mphanthi, kuti munthu wa padziko lapansi angaonjeze kuopsa.
Usavutike mtima chifukwa cha ochita zoipa, usachite nsanje chifukwa cha ochita chosalungama. Katsala kanthawi ndipo woipa adzatha psiti; inde, udzayang'anira mbuto yake, nudzapeza palibe. Koma ofatsa adzalandira dziko lapansi; nadzakondwera nao mtendere wochuluka. Woipa apangira chiwembu wolungama, namkukutira mano. Ambuye adzamseka, popeza apenya kuti tsiku lake likudza. Oipa anasolola lupanga, nakoka uta wao; alikhe ozunzika ndi aumphawi, aphe amene ali oongoka m'njira. Lupanga lao lidzalowa m'mtima mwao momwe, ndipo mauta ao adzathyoledwa. Zochepa zake za wolungama zikoma koposa kuchuluka kwao kwa oipa ambiri. Pakuti manja a oipa adzathyoledwa, koma Yehova achirikiza olungama. Yehova adziwa masiku a anthu angwiro; ndipo cholowa chao chidzakhala chosatha. Sadzachita manyazi m'nyengo yoipa, ndipo m'masiku a njala adzakhuta. Pakuti adzawamweta msanga monga udzu, ndipo adzafota monga msipu wauwisi.
Chilungamo, chilungamo ndicho muzichitsata, kuti mukhale ndi moyo ndi kulandira dziko limene Yehova Mulungu wanu akupatsani.
asapitirireko munthu, nanyenge mbale wake m'menemo, chifukwa Ambuye ndiye wobwezera wa izi zonse, monganso tinakuuziranitu, ndipo tinachitapo umboni.
Ungayanje woipa, koma sadzaphunzira chilungamo; m'dziko la machitidwe oongoka, iye adzangochimwa, sadzaona chifumu cha Yehova. Yehova, dzanja lanu litukulidwa, koma iwo saona; koma iwo adzaona changu chanu cha kwa anthu, nadzakhala ndi manyazi; inde moto udzamaliza adani anu.
Usakhotetsa mlandu wa mnzako waumphawi. Uzikhala kutali ndi mlandu wonama; ndipo usapha munthu wosachimwa ndi wolungama; pakuti sindidzayesa wolungama munthu woipa.
Ndipo usasautsa mlendo kapena kumpsinja; pakuti munali alendo m'dziko la Ejipito. Musazunza mkazi wamasiye, kapena mwana wamasiye aliyense.
Ndiponso ndinaona kunja kuno malo akuweruza, komweko kuli zoipa; ndi malo a chilungamo, komweko kuli zoipa. Ndinati mumtima wanga, Mulungu adzaweruza wolungama ndi woipa; pakuti pamenepo pali mphindi ya zofuna zonse ndi ntchito zonse.
Wakuneneza mnzake m'tseri ndidzamdula; wa maso odzikuza ndi mtima wodzitama sindidzamlola.
Atero Yehova, Chifukwa cha zolakwa zitatu za Israele, kapena zinai, sindidzabweza kulanga kwake; popeza agulitsa wolungama ndi ndalama, ndi wosowa chifukwa cha nsapato; ndiwo amene aliralira fumbi lapansi lili pamutu pa wosauka, napotoza njira ya wofatsa; ndipo munthu ndi atate wake amuka kwa namwali yemweyo, kuti aipse dzina langa loyera;
Ndipo ndidzayandikiza kwa inu kuti ndiweruze; ndipo ndidzakhala mboni yakufulumira kutsutsa obwebweta, ndi achigololo, ndi olumbira monama; ndi iwo akunyenga wolembedwa ntchito pa kulipira kwake, akazi amasiye, ndi ana amasiye, ndi wakuipsa mlandu wa mlendo, osandiopa Ine, ati Yehova wa makamu.
koma wakudzitamandira adzitamandire adzikweze umo, kuti ali wakuzindikira, ndi kundidziwa Ine, kuti ndine Yehova wakuchita zokoma mtima, chiweruziro, ndi chilungamo m'dziko lapansi, pakuti m'menemo ndikondwerera, ati Yehova.
amene apalamulitsa munthu mlandu, namtchera msampha iye amene adzudzula pachipata, nambweza wolungama ndi chinthu chachabe.
ndiye wakuchitira chiweruzo osautsika; ndiye wakupatsa anjala chakudya; Yehova amasula akaidi. Yehova apenyetsa osaona; Yehova aongoletsa onse owerama; Yehova akonda olungama. Yehova asunga alendo; agwiriziza mwana wamasiye ndi mkazi wamasiye; koma akhotetsa njira ya oipa.
Kodi muli chete ndithu poyenera inu kunena zolungama? Muweruza ana anthu molunjika kodi? Wolungama adzakondwera pakuona kubwezera chilango, adzasamba mapazi ake m'mwazi wa woipa. Ndipo anthu adzati, Indedi, pali mphotho kwa wolungama. Indedi, pali Mulungu wakuweruza padziko lapansi. Inde, mumtima muchita zosalungama; padziko lapansi mugawira anthu chiwawa cha m'manja mwanu.
Kodi kumeneku si kusala kudya kumene ndinakusankha: kumasula nsinga za zoipa, ndi kumasula zomanga goli, ndi kuleka otsenderezedwa amuke mfulu, ndi kuti muthyole magoli onse? Kodi si ndiko kupatsa chakudya chako kwa anjala, ndi kuti ubwere nao kunyumba kwako aumphawi otayika? Pakuona wamaliseche kuti umveke, ndi kuti usadzibisire wekha a chibale chako?
Musamasautsa wolembedwa ntchito, wakukhala waumphawi ndi wosauka, wa abale anu kapena wa alendo ali m'dziko mwanu, m'midzi mwanu. Pa tsiku lake muzimpatsa kulipira kwake, lisalowepo dzuwa; pakuti ndiye waumphawi, ndi mtima wake ukhumba uku; kuti angakulirireni kwa Yehova, ndipo kukukhalireni tchimo.
Mzinda wokhulupirika wasanduka wadama! Wodzala chiweruzowo! Chilungamo chinakhalamo koma tsopano ambanda.
Usalande za waumphawi chifukwa ali waumphawi, ngakhale kutsendereza wosauka kubwalo. Pakuti Yehova adzanenera mlandu wao; omwe akwatula zao Iye adzakwatula moyo wao.
Apulumutsa aumphawi kulupanga la kukamwa kwao, ndi kudzanja la wamphamvu. Potero aumphawi ali nacho chiyembekezo, ndi mphulupulu yatsekedwa pakamwa.
Tsoka kwa iwo amene ayesa zoipa zabwino, ndi zabwino zoipa; amene aika mdima m'malo mwa kuyera, ndi kuyera m'malo mwa mdima; amene aika zowawa m'malo mwa zotsekemera, ndi zotsekemera m'malo mwa zowawa!
Koma tsoka inu, Afarisi! Chifukwa mupereka limodzi la magawo khumi la timbeu tonunkhira, ndi timbeu tokometsa chakudya ndi ndiwo zonse, ndipo mumaleka chiweruzo ndi chikondi cha Mulungu; mwenzi mutachita izi, ndi kusasiya zinazo.
Tamverani ichi, inu akumeza aumphawi, ndi kuwatha ofatsa m'dziko, ndi kuti, Mwezi wokhala upita liti, kuti tigulitse dzinthu? Ndi Sabata, kuti titsegulire tirigu? Ndi kuchepsa efa, ndi kukulitsa sekeli, ndi kuchenjerera nayo miyeso yonyenga; kuti tigule osauka ndi ndalama, ndi aumphawi ndi nsapato, ndi kugulitsa nsadwa za tirigu.
Usatola mbiri yopanda pake; usathandizana naye woipa ndi kukhala mboni yochititsa chiwawa. Ndipo uzibzala m'munda mwako zaka zisanu ndi chimodzi, ndi kututa zipatso zako; koma chaka chachisanu ndi chiwiri uuleke, ugone; kuti aumphawi a anthu a mtundu wako adyemo, ndipo zotsalira nyama zakuthengo zizidye; momwemo uzichita ndi munda wako wampesa, ndi munda wako wa azitona. Uzichita ntchito yako masiku asanu ndi limodzi, koma tsiku lachisanu ndi chiwiri uzipumula; kuti ng'ombe yako ndi bulu wako zipumule, ndi kuti mwana wa mdzakazi wako ndi mlendo atsitsimuke. Ndipo samalirani zonse ndanena ndi inu; nimusatchule dzina la milungu ina; lisamveke pakamwa pako. Muzindichitira Ine madyerero katatu m'chaka. Uzisunga chikondwerero cha Mkate wopanda chotupitsa; masiku asanu ndi awiri uzidya mkate wopanda chotupitsa, monga ndinakuuza, nyengo yoikika, mwezi wa Abibu, pakuti m'menemo unatuluka mu Ejipito; koma asaoneke munthu pamaso panga opanda kanthu; ndi chikondwerero cha Masika, zipatso zoyamba za ntchito zako, zimene udazibzala m'munda; ndi chikondwerero cha Kututa, pakutha chaka, pamene ututa ntchito zako za m'munda. Katatu m'chaka amuna onse azioneka pamaso pa Ambuye Yehova. Usapereka mwazi wa nsembe yanga pamodzi ndi mkate wa chotupitsa; ndi mafuta a madyerero anga asagonamo kufikira m'mawa. Uzibwera nazo zoyambayamba za m'munda mwako kunyumba ya Yehova Mulungu wako. Usaphike mwanawambuzi mu mkaka wa make. Usatsata unyinji wa anthu kuchita choipa; kapena usachita umboni kumlandu, ndi kupatukira kutsata unyinji ndi kukhotetsa mlandu; Taona, ndituma mthenga akutsogolere, kukusunga panjira, ndi kukufikitsa pamaso pomwe ndakonzeratu. Musamalire iye, ndi kumvera mau ake; musamuwawitsa mtima, pakuti sadzakhululukira zolakwa zanu; popeza dzina langa lili m'mtima mwake. Pakuti ukamveratu mau ake, ndi kuchita zonse ndizilankhula, ndidzakhala mdani wa adani ako, ndipo ndidzasautsa akusautsa iwe. Pakuti mthenga wanga adzakutsogolera, nadzakufikitsa kwa Aamori, ndi Ahiti, ndi Aperizi, ndi Akanani, Ahivi, ndi Ayebusi; ndipo ndidzawaononga. Usagwadira milungu yao, kapena kuwatumikira, kapena kuchita monga mwa ntchito zao; koma uwapasule konse, ndi kugamulatu zoimiritsa zao. Ndipo muzitumikira Yehova Mulungu wanu, potero adzadalitsa chakudya chako, ndi madzi ako; ndipo ndidzachotsa nthenda pakati pa iwe. M'dziko mwanu simudzakhala wakutaya mwana, kapena wosabala; ndidzakwaniritsa kuwerenga kwa masiku ako. Ndidzatumiza kuopsa kwanga kukutsogolere, ndipo ndidzapirikitsa anthu onse amene udzafika kwao, ndipo ndidzachita kuti adani ako onse adzakuonetsa m'mbuyo mwao. Ndipo ndidzatumiza mavu akutsogolere amene adzaingitsa Ahivi, Akanani, ndi Ahiti, pamaso pako. Sindidzawaingitsa pamaso pako chaka chimodzi; kuti dziko lingakhale bwinja, ndi zilombo zakuthengo zingakuchulukire. kapena usakometsera munthu wosauka pa mlandu wake.
Musamachita chisalungamo pakuweruza mlandu; usamavomereza munthu wosauka, kapena kulemekeza munthu womveka; uweruze mlandu wa munthu mnzako molungama.
Chifukwa chake Yehova adzadikira, kuti akukomereni mtima, ndipo chifukwa chake Iye adzakuzidwa, kuti akuchitireni inu chifundo; pakuti Yehova ndiye Mulungu wa chiweruziro; odala ali onse amene amdikira Iye.
Monga nkhwali iumatira pa mazira amene sinaikire, momwemo iye amene asonkhanitsa chuma, koma mosalungama; pakati pa masiku ake chidzamsiya iye, ndipo pa chitsirizo adzakhala wopusa.
Ndinabweranso tsono ndi kupenyera nsautso zonse zimachitidwa kunja kuno; ndipo taona, misozi ya otsenderezedwa, koma analibe wakuwatonthoza; ndipo akuwatsendereza anali ndi mphamvu koma iwowa analibe wakuwatonthoza.
Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! Chifukwa mupereka limodzi la magawo khumi la timbeu tonunkhira, ndi katsabola, ndi la chitowe, nimusiya zolemera za chilamulo, ndizo kuweruza kolungama, ndi kuchitira chifundo, ndi chikhulupiriro; koma zijazo munayenera kuzichita, osasiya izi zomwe.
Musazunza mkazi wamasiye, kapena mwana wamasiye aliyense. Ukawazunza ndi kakuti konse, nakandilirira pang'ono ponse iwowa, ndidzamvadi kulira kwao;
Ndipo chiweruziro chabwerera m'mbuyo, ndi chilungamo chaima patali; pakuti choona chagwa m'khwalala, ndi kuongoka sikungalowe. Inde choona chisoweka; iye amene asiya choipa, zifunkhidwa zake; ndipo Yehova anaona ichi, ndipo chidamuipira kuti palibe chiweruzo.
Musabwezere choipa, okondedwa, koma patukani pamkwiyo; pakuti kwalembedwa, Kubwezera kuli kwanga, Ine ndidzabwezera, ati Ambuye.
Wotembereredwa iye wakuipsa mlandu wa mlendo, mwana wamasiye, ndi mkazi wamasiye. Ndi anthu onse anene, Amen.
Yehova adzalowa m'bwalo la milandu ndi okalamba a anthu ake, ndi akulu ake: Ndinu amene mwadya munda wampesa, zofunkha za waumphawi zili m'nyumba zanu; muti bwanji inu, amene mupsinja anthu anga, ndi kupera nkhope ya wosauka? Ati Ambuye, Yehova wa makamu.
Kukometsa mlandu wa wamphulupulu mwatsankho sikuli kwabwino, ngakhale kuchitira chetera wolungama.
Koma Yehova akhala chikhalire, anakonzeratu mpando wachifumu wake kuti aweruze. Ndipo Iyeyu adzaweruza dziko lapansi m'chilungamo, nadzaweruza anthu molunjika. Ndipo Yehova adzakhala msanje kwa iye wokhalira mphanthi. Msanje m'nyengo za nsautso;
Pakuti mwa anthu anga aoneka anthu oipa; adikira monga akutcha misampha; atcha khwekhwe, agwira anthu. Monga chikwere chodzala ndi mbalame, chomwecho nyumba zao zadzala ndi chinyengo; chifukwa chake akula, alemera. Anenepa, anyezimira; inde apitiriza kuchita zoipa; sanenera ana amasiye mlandu wao, kuti apindule; mlandu wa aumphawi saweruza. Sindidzawalanga kodi chifukwa cha zimenezi? Ati Yehova; kodi moyo wanga sudzabwezera chilango mtundu wotere?
Wonena kwa woipa, Wolungama iwe; magulu a anthu adzamtemberera, mitundu ya anthu idzamkwiyira. Omwe amdzudzula adzasekera, nadzadalitsika ndithu.
Mundionetseranji zopanda pake, ndi kundionetsa zovuta? Pakuti kufunkha ndi chiwawa zili pamaso panga; ndipo pali ndeu, nauka makani. Pakuti chilamulo chalekeka, ndi chiweruzo sichitulukira konse; popeza woipa azinga wolungama, chifukwa chake chiweruzo chituluka chopindika.
Ndipo kodi Mulungu sadzachitira chilungamo osankhidwa ake akumuitana usana ndi usiku, popeza aleza nao mtima? Ndinena ndi inu, adzawachitira chilungamo posachedwa. Koma Mwana wa Munthu pakudza Iye, adzapeza chikhulupiriro padziko lapansi kodi?
Koma iye amene ali nacho chuma cha dziko lapansi, naona mbale wake ali wosowa ndi kutsekereza chifundo chake pommana iye, nanga chikondi cha Mulungu chikhala mwa iye bwanji?
Wotsendereza waumphawi kuti achulukitse chuma chake, ndi wopatsa wolemera kanthu, angosauka.
Usalandira chokometsera mlandu; pakuti chokometsera mlandu chidetsa maso a openya, ndipo chisanduliza mlandu wa olungama.
Kodi uyenera kuyanjana ndi Inu mpando wachifumu wa kusakaza, wakupanga chovuta chikhale lamulo? Asonkhana pamodzi pa moyo wa wolungama, namtsutsa wa mwazi wosachimwa.
Ndipo kunali, atamva Ahabu kuti Naboti Myezireele wafa, Ahabu anauka kukatsikira ku munda wampesa wa Naboti, kuulandira.
Ukaona anthu alikutsendereza aumphawi, ndi kuchotsa chilungamo ndi chiweruzo mwachiwawa pa dera lina la dziko, usazizwepo; pakuti mkulu wopambana asamalira; ndipo alipo akulu ena oposa amenewo.
Munthu woipa alandira chokometsera mlandu chotulutsa m'mfunga, kuti apatukitse mayendedwe a chiweruzo.
pakuti ndinali ndi njala, ndipo munandipatsa Ine kudya; ndinali ndi ludzu, ndipo munandimwetsa Ine; ndinali mlendo, ndipo munachereza Ine; wamaliseche Ine, ndipo munandiveka; ndinadwala, ndipo munadza kucheza ndi Ine; ndinali m'nyumba yandende, ndipo munadza kwa Ine.
Tsoka iye amene amanga nyumba yake ndi chisalungamo, ndi zipinda zapamwamba ndi chosaweruza bwino; amene agwiritsa mnzake ntchito osamlipira, osampatsa mphotho yake;
Ndipo Iye anati kwa iwo, Yang'anirani, mudzisungire kupewa msiriro uliwonse; chifukwa moyo wake wa munthu sulingana ndi kuchuluka kwa zinthu zake ali nazo.
Ndipo mudzachita chiyani tsiku lakudza woyang'anira, ndi chipasuko chochokera kutali? Mudzathawira kwa yani kufuna kuthangatidwa? Mudzasiya kuti ulemerero wanu?
Nanga tsono achuma inu, lirani ndi kuchema chifukwa cha masautso anu akudza pa inu. Tengani, abale, chitsanzo cha kumva zowawa ndi kuleza mtima, aneneri amene analankhula m'dzina la Ambuye. Taonani tiwayesera odala opirirawo; mudamva za chipiriro cha Yobu, ndipo mwaona chitsiriziro cha Ambuye, kuti Ambuye ali wodzala chikondi, ndi wachifundo. Koma makamaka, abale anga, musalumbire, kungakhale kutchula kumwamba kapena dziko, kapena lumbiro lina lililonse; koma inde wanu akhale inde, ndi iai wanu akhale iai; kuti mungagwe m'chiweruziro. Kodi wina wa inu akumva zowawa? Apemphere. Kodi wina asekera? Aimbire. Pali wina kodi adwala mwa inu? Adziitanire akulu a Mpingo, ndipo apemphere pa iye, atamdzoza ndi mafuta m'dzina la Ambuye: ndipo pemphero la chikhulupiriro lidzapulumutsa wodwalayo, ndipo Ambuye adzamuukitsa; ndipo ngati adachita machimo adzakhululukidwa kwa iye. Chifukwa chake muvomerezane wina ndi mnzake machimo anu, ndipo mupempherere wina kwa mnzake kuti muchiritsidwe. Pemphero la munthu wolungama likhoza kwakukulu m'machitidwe ake. Eliya anali munthu wakumva zomwezi tizimva ife, ndipo anapemphera chipempherere kuti isavumbe mvula; ndipo siinagwe mvula padziko zaka zitatu kudza miyezi isanu ndi umodzi. Ndipo anapempheranso; ndipo m'mwamba munatsika mvula, ndi dziko lidabala zipatso zake. Abale anga, ngati wina wa inu asochera posiyana ndi choonadi, ndipo ambweza iye mnzake; Chuma chanu chaola ndi zovala zanu zajiwa ndi njenjete. azindikire, kuti iye amene abweza wochimwa kunjira yake yosochera adzapulumutsa munthu kwa imfa, ndipo adzavundikira machimo aunyinji. Golide wanu ndi siliva wanu zachita dzimbiri, ndipo dzimbiri lake lidzachita mboni zoneneza inu, ndipo zidzadya nyama yanu ngati moto. Mwadzikundikira chuma masiku otsiriza. Taonani, mphotho ya antchitowo anasenga m'minda yanu, yosungidwa ndi inu powanyenga, ifuula; ndipo mafuulo a osengawo adalowa m'makutu a Ambuye wa makamu.
Mafupa anga onse adzanena, Yehova, afanana ndi Inu ndani, wakulanditsa wozunzika kwa iye amene amposa mphamvu, ndi wozunzika ndi waumphawi kwa iye amfunkhira?
Pakuti chiyembekezo cha wonyoza Mulungu nchiyani pomlikhatu Mulungu, pomchotsera moyo wake? Kodi Mulungu adzamvera kufuula kwake, ikamdzera nsautso?
Chifukwa chake zinthu zilizonse mukafuna kuti anthu achitire inu, inunso muwachitire iwo zotero; pakuti icho ndicho chilamulo ndi aneneri.
Pakuti Yehova akonda chiweruzo, ndipo sataya okondedwa ake. Asungika kosatha, koma adzadula mbumba za oipa.
Ndipo mudzapulumutsa anthu osautsidwa; koma maso anu ali pa odzikuza kuti muwachepetse.
Koma ine ndikadafuna Mulungu, ndikadaikira mlandu wanga Mulungu; amene achita zazikulu ndi zosalondoleka, zinthu zodabwitsa zosawerengeka.
Iye amene ayenda molungama, nanena molunjika; iye amene anyoza phindu lonyenga, nasansa manja ake kusalandira zokometsera milandu, amene atseka makutu ake kusamva za mwazi, natsinzina maso ake kusayang'ana choipa;
Alipo akusendeza malire; alanda gulu la zoweta, nazidyetsa. M'mimba mudzamuiwala; mphutsi zidzamudya mokondwera. Sadzamkumbukiranso; ndipo chosalungama chidzathyoledwa ngati mtengo. Alusira chumba wosabala, osamchitira wamasiye chokoma. Mulungu awakhalitsa amphamvu mwa mphamvu yake; iwo aukanso m'mene anayesa kuti sadzakhala ndi moyo. Awalola akhale osatekeseka, ndipo alimbikapo; koma maso ake ali panjira zao. Akwezeka; m'kamphindi kuli zii; inde atsitsidwa, achotsedwa monga ena onse, adulidwa ngati tirigu ngala zake. Ndipo ngati si kutero, anditsutsa ndani kuti ndili wabodza, ndi kuyesa mau anga opanda pake? Akankhizira kwao bulu wa amasiye, atenga ng'ombe ya mfedwa ikhale chikole. Apatukitsa aumphawi m'njira; osauka a padziko abisala pamodzi.
Inu Yehova, mudziwa; mundikumbukire ine, mundiyang'anire Ine, mundibwezere chilango pa ondisautsa ine; musandichotse m'chipiriro chanu; dziwani kuti chifukwa cha Inu ndanyozedwa.
Zonsezi ndaziona ndi kuyang'anitsa mtima wanga ntchito zonse zichitidwa pansi pano; nthawi yakuti wina apweteka mnzake pomlamulira.
Ndipo anthu a makamu anamfunsa iye, nanena, Ndipo tsono tizichita chiyani? Koma iye anayankha nanena kwa iwo, Iye amene ali nao malaya awiri apatse kwa iye amene alibe; ndi iye amene ali nazo zakudya achite chomwecho.
usaope, pakuti Ine ndili pamodzi ndi iwe; usaopsedwe, pakuti Ine ndine Mulungu wako; ndidzakulimbitsa; inde, ndidzakuthangata; inde, ndidzakuchirikiza ndi dzanja langa lamanja la chilungamo.
Kumbukirani am'nsinga, monga am'nsinga anzao; ochitidwa zoipa, monga ngati inunso adatero nanu m'thupi.
Mzimu wa Ambuye Yehova uli pa ine; pakuti Yehova wandidzoza ine ndilalikire mau abwino kwa ofatsa; Iye wanditumiza ndikamange osweka mtima, ndikalalikire kwa am'nsinga mamasulidwe, ndi kwa omangidwa kutsegulidwa kwa m'ndende; Ndidzakondwa kwambiri mwa Yehova, moyo wanga udzakondwerera mwa Mulungu wanga; pakuti Iye wandiveka ine ndi zovala za chipulumutso, nandifunda chofunda cha chilungamo, monga mkwati avala nduwira, ndi monga mkwatibwi adzikometsa yekha ndi miyala yamtengo. Pakuti monga dziko liphukitsa mphundu zake, ndi monga munda umeretsa zobzalamo, momwemo Ambuye Yehova adzaphukitsa chilungamo ndi matamando pamaso pa amitundu onse. ndikalalikire chaka chokomera Yehova, ndi tsiku lakubwezera la Mulungu wathu; ndikatonthoze mtima wa onse amene akulira maliro;
Usampsinja mlendo; pakuti mudziwa mtima wa mlendo popeza munali alendo m'dziko la Ejipito.
Zipangizonso za womana zili zoipa; iye apangira ziwembu zakuononga waumphawi ndi mau onama, ngakhale pamene wosowa alankhula zoona.