Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mlaliki 8:9 - Buku Lopatulika

9 Zonsezi ndaziona ndi kuyang'anitsa mtima wanga ntchito zonse zichitidwa pansi pano; nthawi yakuti wina apweteka mnzake pomlamulira.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Zonsezi ndaziona ndi kuyang'anitsa mtima wanga ntchito zonse zichitidwa pansi pano; nthawi yakuti wina apweteka mnzake pomlamulira.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Zonsezi ndidaziwona pamene ndinkalingalira mumtima mwanga zonse zimene zimachitika pansi pano. Nthaŵi zonse pali ena amene amalamulira anzao mwankhanza.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Zonsezi ndinaziona pamene ndinalingalira mu mtima mwanga, zonse zimene zimachitika pansi pano. Ilipo nthawi imene ena amalamulira anzawo mwankhanza.

Onani mutuwo Koperani




Mlaliki 8:9
15 Mawu Ofanana  

Napha ana a Zedekiya pamaso pake, namkolowola Zedekiya maso ake, nammanga ndi maunyolo amkuwa, namuka naye ku Babiloni.


Popeza madziwo anabwerera, namiza magaleta ndi apakavalo, ndiwo nkhondo yonse ya Farao imene idalowa pambuyo pao m'nyanja; sanatsale wa iwowa ndi mmodzi yense.


Ndaona ntchito zonse zipangidwa kunja kuno; ndipo zonsezo ndi chabe ndi kungosautsa mtima.


Ndaona vuto limene Mulungu wapatsa ana a anthu kuti avutidwe nalo.


Ndiponso ndinaona kunja kuno malo akuweruza, komweko kuli zoipa; ndi malo a chilungamo, komweko kuli zoipa.


Ndinabweranso tsono ndi kupenyera nsautso zonse zimachitidwa kunja kuno; ndipo taona, misozi ya otsenderezedwa, koma analibe wakuwatonthoza; ndipo akuwatsendereza anali ndi mphamvu koma iwowa analibe wakuwatonthoza.


Pali choipa chovuta ndachiona kunja kuno, ndicho, chuma chilikupweteka eni ake pochikundika;


Pakuti monga mu unyinji wa maloto muli zachabe motero mochuluka mau; koma dziopa Mulungu.


Ukaona anthu alikutsendereza aumphawi, ndi kuchotsa chilungamo ndi chiweruzo mwachiwawa pa dera lina la dziko, usazizwepo; pakuti mkulu wopambana asamalira; ndipo alipo akulu ena oposa amenewo.


Ndinapotoka ndi mtima wanga womwe kudziwa ndi kusanthula ndi kufunafuna nzeru ndi malongosoledwe a zinthu, ndi kudziwa kuti udyo ndiwo utsiru, ndi kuti kupusa ndi misala;


Indetu nsautso uyalutsa wanzeru; ndi mtulo uipitsa mtima.


Koma Sihoni mfumu ya Hesiboni sanatilole kupitira kwao; popeza Yehova Mulungu wanu anaumitsa mzimu wake, nalimbitsa mtima wake, kuti ampereke m'dzanja lanu, monga lero lino.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa