Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Mlaliki 8:10 - Buku Lopatulika

10 Ndipo ndinaona oipa alikuikidwa m'manda ndi kupita; ndipo omwe anachita zolungama anachokera kumalo opatulika akumzinda nawaiwala; ichinso ndi chabe.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Ndipo ndinaona oipa alikuikidwa m'manda ndi kupita; ndipo omwe anachita zolungama anachokera kumalo opatulika akumudzi nawaiwala; ichinso ndi chabe.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Pambuyo pake ndidaona oipa akuikidwa m'manda. Iwowo kale ankaloŵa ndi kumatuluka m'malo oyera, ndipo mumzindamo anthu ankaŵatamanda m'mene ankachita zinthu zoterezi. Zimenezinso nzachabechabe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Kenaka, ndinaona anthu oyipa akuyikidwa mʼmanda, iwo amene ankalowa ndi kumatuluka mʼmalo opatulika ndipo ankatamandidwa mu mzindawo pamene ankachita zimenezi. Izinso ndi zopandapake.

Onani mutuwo Koperani




Mlaliki 8:10
14 Mawu Ofanana  

Ngati akunga ziputu zomka ndi mphepo, ngati mungu wouluzika ndi nkuntho?


Ndaiwalika m'mtima monga wakufa, ndikhala monga chotengera chosweka.


Amayesa wolungama wodala pomkumbukira; koma dzina la oipa lidzavunda.


Zoyamba zija sizikumbukiridwa; ngakhale zomwe zilinkudzazo, omwe adzakhalabe m'tsogolomo, sadzazikumbukirai.


Pakuti wanzeru saposa chitsiru kukumbukidwa nthawi zonse; pakuti zonse zooneka kale zidzaiwalika m'tsogolomo. Ndipo wanzeru amwalira bwanji ngati chitsirutu.


koma anapezedwamo mwamuna wanzeru wosauka, yemweyo napulumutsa mzindawo ndi nzeru yake; koma panalibe anthu anakumbukira wosauka ameneyo.


Pakuti amoyo adziwa kuti tidzafa; koma akufa sadziwa kanthu bii, sadzalandira mphotho; pakuti angoiwalika.


Inu Yehova, chiyembekezo cha Israele, onse amene akukusiyani Inu adzakhala ndi manyazi; onse ondichokera Ine adzalembedwa m'dothi, chifukwa asiya Yehova, kasupe wa madzi amoyo.


Ndipo kunali kuti wopemphayo adafa, ndi kuti anatengedwa iye ndi angelo kunka kuchifuwa cha Abrahamu; ndipo mwini chumayo adafanso, naikidwa m'manda.


naimika mboni zonama, zakunena, Munthu ameneyo saleka kunenera malo oyera amene, ndi chilamulo;


Koma wolungama wangayo adzakhala ndi moyo wochokera m'chikhulupiriro: Ndipo ngati abwerera, moyo wanga ulibe kukondwera mwa iye.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa