Eksodo 23:8 - Buku Lopatulika8 Usalandira chokometsera mlandu; pakuti chokometsera mlandu chidetsa maso a openya, ndipo chisanduliza mlandu wa olungama. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20148 Usalandira chokometsera mlandu; pakuti chokometsera mlandu chidetsa maso a openya, nichisanduliza mlandu wa olungama. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa8 Usalandire chiphuphu poti chimadetsa m'maso anthu oweruza, ndipo motero mlandu umaipira anthu osalakwa. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero8 “Musamalandire chiphuphu, pakuti chiphuphu chimadetsa mʼmaso anthu oweruza ndi kusintha mawu awo kuti mlandu uyipire osalakwa. Onani mutuwo |
Ndikalipo ine; chitani umboni wonditsutsa pamaso pa Yehova, ndi pamaso pa wodzozedwa wake; ndinalanda ng'ombe ya yani? Kapena ndinalanda bulu wa yani? Ndinanyenga yani? Ndinasutsa yani? Ndinalandira m'manja mwa yani chokometsera mlandu kutseka nacho maso anga? Ngati ndinatero ndidzachibwezera kwa inu.