Eksodo 23:8 - Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero8 “Musamalandire chiphuphu, pakuti chiphuphu chimadetsa mʼmaso anthu oweruza ndi kusintha mawu awo kuti mlandu uyipire osalakwa. Onani mutuwoBuku Lopatulika8 Usalandira chokometsera mlandu; pakuti chokometsera mlandu chidetsa maso a openya, ndipo chisanduliza mlandu wa olungama. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20148 Usalandira chokometsera mlandu; pakuti chokometsera mlandu chidetsa maso a openya, nichisanduliza mlandu wa olungama. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa8 Usalandire chiphuphu poti chimadetsa m'maso anthu oweruza, ndipo motero mlandu umaipira anthu osalakwa. Onani mutuwo |
Ine ndili pano. Ngati ndinalakwa chilichonse nditsutseni pamaso pa Yehova ndi wodzozedwa wake. Kodi ndinalanda ngʼombe ya yani? Kodi ndinalanda bulu wa yani? Kodi ndani amene ndinamudyera masuku pa mutu? Kodi ndinazunza yani? Kodi ndinalandira kwa yani chiphuphu choti nʼkundidetsa mʼmaso? Ngati ndinachita chilichonse cha izi, ine ndidzakubwezerani.”