Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 82:2 - Buku Lopatulika

2 Mudzaweruza mosalunjika kufikira liti, ndi kusamalira nkhope ya oipa?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Mudzaweruza mosalunjika kufikira liti, ndi kusamalira nkhope ya oipa?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Akuti, “Mudzakhalabe mukuweruza mopanda chilungamo mpaka liti? Bwanji mukupitirizabe kumakondera anthu oipa?

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 “Mudzateteza osalungama mpaka liti, ndi kukondera anthu oyipa?

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 82:2
16 Mawu Ofanana  

Ndipo Eliya anayandikira kwa anthu onse, nati, Mukayikakayika kufikira liti? Ngati Yehova ndiye Mulungu, mtsateni Iye; ngati Baala, mumtsate iyeyo. Ndipo panalibe ndi mmodzi yemwe anamuyankha.


Ndipo tsono, kuopa Yehova kukhale pa inu, musamalire ndi kuchita; pakuti palibe chosalungama kwa Yehova Mulungu wathu, kapena kusamalira monga mwa nkhope ya munthu, kapena kulandira mphatso.


Ndisati ndisamalire nkhope ya munthu, kapena kumtchula munthu maina omdyola nao;


Nanga kwa Iye wosasamalira nkhope za akalonga, wosasiyanitsa pakati pa wolemera ndi wosauka? Pakuti onsewo ndiwo ntchito ya manja ake.


Mudzamvumvulukira munthu mpaka liti, kumupha iye, nonsenu, monga khoma lopendekeka, ndi mpanda woweyeseka?


Ndipo Mose ndi Aroni analowa kwa Farao nanena naye, Atero Yehova, Mulungu wa Ahebri, Ukana kudzichepetsa pamaso panga kufikira liti? Lola anthu anga amuke, akanditumikire;


Kukometsa mlandu wa wamphulupulu mwatsankho sikuli kwabwino, ngakhale kuchitira chetera wolungama.


Atero Ambuye Yehova, Likufikireni akalonga a Israele inu, lekani kuchita chiwawa, ndi kulanda za eni ake; muchite chiweruzo ndi chilungamo; lekani kupirikitsa anthu anga m'zolowa zao, ati Ambuye Yehova.


Musamachita chisalungamo pakuweruza mlandu; usamavomereza munthu wosauka, kapena kulemekeza munthu womveka; uweruze mlandu wa munthu mnzako molungama.


Ndipo Yesu anayankha nati, Ha, obadwa osakhulupirira ndi amphulupulu, ndidzakhala ndi inu nthawi yanji? Ndidzalekerera inu nthawi yanji? Mudze naye kwa Ine kuno.


Koma iwo akuyesedwa ali kanthu (ngati anali otani kale, kulibe kanthu kwa ine; Mulungu salandira nkhope ya munthu) iwo omvekawo sanandionjezere ine kanthu;


Musamasamalira munthu poweruza mlandu; ang'ono ndi akulu muwamvere chimodzimodzi; musamaopa nkhope ya munthu; popeza chiweruzo ncha Mulungu; ndipo mlandu ukakukanikani mubwere nao kwa ine, ndidzaumva.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa