Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 82:1 - Buku Lopatulika

1 Mulungu aima mu msonkhano wa Mulungu, aweruza pakati pa milungu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

1 Mulungu aima mu msonkhano wa Mulungu, aweruza pakati pa milungu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 Mulungu akutsogolera msonkhano wakumwamba. Akugamula mlandu milungu ya pansi pano.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

1 Mulungu akutsogolera msonkhano waukulu; Iye akuweruza pakati pa “milungu.”

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 82:1
12 Mawu Ofanana  

Ndidzakuyamikani ndi mtima wanga wonse; ndidzaimba zakukulemekezani patsogolo pa milungu.


Mulungu wa milungu, Yehova, wanena, aitana dziko lapansi kuyambira kutuluka kwa dzuwa kufikira kulowa kwake.


Ndipo anthu adzati, Indedi, pali mphotho kwa wolungama. Indedi, pali Mulungu wakuweruza padziko lapansi.


Inde, mumtima muchita zosalungama; padziko lapansi mugawira anthu chiwawa cha m'manja mwanu.


Koma iwe, dzisankhire mwa anthu ako onse, amuna anzeru, akuopa Mulungu, amuna oona, akudana nalo phindu la chinyengo; nuwaikire iwo oterewa, akulu a pa zikwi, akulu a pa mazana, akulu a pa makumi asanu, akulu a pa makumi;


pamenepo mbuye wake azifika naye kwa oweruza, nafike naye kukhomo, kapena kumphuthu, ndipo mbuye wake am'boole khutu lake ndi lisungulo; ndipo iye azimgwirira ntchito masiku onse.


Usapeputsa oweruza, kapena kutemberera mkulu wa anthu a mtundu wako.


Ukaona anthu alikutsendereza aumphawi, ndi kuchotsa chilungamo ndi chiweruzo mwachiwawa pa dera lina la dziko, usazizwepo; pakuti mkulu wopambana asamalira; ndipo alipo akulu ena oposa amenewo.


Yehova aimirira kuti atsutsane, naimiriranso kuti aweruze mitundu ya anthu.


Ngati anawatcha milungu iwo amene mau a Mulungu anawadzera (ndipo cholemba sichingathe kuthyoka),


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa