Masalimo 82 - Buku LopatulikaOweruza aweruza bwino Salimo la Asafu. 1 Mulungu aima mu msonkhano wa Mulungu, aweruza pakati pa milungu. 2 Mudzaweruza mosalunjika kufikira liti, ndi kusamalira nkhope ya oipa? 3 Weruzani osauka ndi amasiye; weruzani molungama ozunzika ndi osowa. 4 Pulumutsani osauka ndi aumphawi; alanditseni m'dzanja la oipa. 5 Sadziwa, ndipo sazindikira; amayendayenda mumdima; maziko onse a dziko lapansi agwedezeka. 6 Ndinati Ine, Inu ndinu milungu, ndi ana a Wam'mwambamwamba nonsenu. 7 Komatu mudzafa monga anthu, ndipo mudzagwa monga wina wa akulu. 8 Ukani, Mulungu, weruzani dziko lapansi; pakuti Inu mudzalandira amitundu onse. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi