Mlaliki 7:7 - Buku Lopatulika7 Indetu nsautso uyalutsa wanzeru; ndi mtulo uipitsa mtima. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20147 Indetu nsautso uyalutsa wanzeru; ndi mtulo uipitsa mtima. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa7 Ndithudi kuzunza ena kumamsandutsa munthu wanzeru kuti akhale wopusa, ndipo kulandira chiphuphu kumaononga mtima. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero7 Kuzunza ena kumasandutsa munthu wanzeru kukhala chitsiru, ndipo chiphuphu chimawononga mtima. Onani mutuwo |
Ndikalipo ine; chitani umboni wonditsutsa pamaso pa Yehova, ndi pamaso pa wodzozedwa wake; ndinalanda ng'ombe ya yani? Kapena ndinalanda bulu wa yani? Ndinanyenga yani? Ndinasutsa yani? Ndinalandira m'manja mwa yani chokometsera mlandu kutseka nacho maso anga? Ngati ndinatero ndidzachibwezera kwa inu.