Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Eksodo 22:21 - Buku Lopatulika

21 Ndipo usasautsa mlendo kapena kumpsinja; pakuti munali alendo m'dziko la Ejipito.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

21 Ndipo usasautsa mlendo kapena kumpsinja; pakuti munali alendo m'dziko la Ejipito.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

21 “Musazunze mlendo kapena kumkhalitsa m'phanthi, poti paja inunso munali alendo ku dziko la Ejipito.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

21 “Musazunze mlendo kapena kumuchitira nkhanza, pakuti inu munali alendo mʼdziko la Igupto.

Onani mutuwo Koperani




Eksodo 22:21
22 Mawu Ofanana  

Indetu, mugwetsera wamasiye msampha, mumkumbira bwenzi lanu mbuna.


Yehova asunga alendo; agwiriziza mwana wamasiye ndi mkazi wamasiye; koma akhotetsa njira ya oipa.


Ine ndine Yehova Mulungu wako, amene ndinatulutsa iwe ku dziko la Ejipito, kunyumba ya ukapolo.


Usampsinja mlendo; pakuti mudziwa mtima wa mlendo popeza munali alendo m'dziko la Ejipito.


phunzirani kuchita zabwino; funani chiweruzo; thandizani osautsidwa, weruzirani ana amasiye, munenere akazi amasiye.


Yehova atero: Chitani chiweruzo ndi chilungamo, landitsani ofunkhidwa m'dzanja la wosautsa; musachite choipa, musamchitire mlendo chiwawa, kapena ana amasiye, kapena akazi amasiye, musakhetse mwazi wosachimwa pamalo pano.


ndi kuleka kutsendereza mlendo, ndi wamasiye, ndi mkazi wamasiye, osakhetsa mwazi wosachimwa m'malo muno, osatsata milungu ina ndi kudziipitsa nayo;


Mwa iwe anapepula atate ndi mai, pakati pa iwe anamchitira mlendo momzunza, mwa iwe anazunza ana amasiye, ndi mkazi wamasiye.


Usamasautsa mnansi wako, kapena kulanda zake; mphotho yake ya wolipidwa isakhale ndi iwe kufikira m'mawa.


Ndipo mlendo akagonera m'dziko mwanu, musamamsautsa.


Mlendo wakugonera kwa inu mumuyese pakati pa inu monga wa m'dziko momwemo; umkonde monga udzikonda wekha; popeza munali alendo m'dziko la Ejipito; Ine ndine Yehova Mulungu wanu.


Ndipo mbale wako akasaukira chuma, ndi dzanja lake lisowa; iwe uzimgwiriziza; akhale nawe monga mlendo wakugonera kwanu.


musazunza mkazi wamasiye, kapena ana amasiye, mlendo kapena waumphawi; ndipo nnena mmodzi wa inu alingirire m'mtima mwake kumchitira choipa munthu mnzake.


Ndipo ndidzayandikiza kwa inu kuti ndiweruze; ndipo ndidzakhala mboni yakufulumira kutsutsa obwebweta, ndi achigololo, ndi olumbira monama; ndi iwo akunyenga wolembedwa ntchito pa kulipira kwake, akazi amasiye, ndi ana amasiye, ndi wakuipsa mlandu wa mlendo, osandiopa Ine, ati Yehova wa makamu.


Ndipo ndinauza oweruza anu muja, ndi kuti, Mverani milandu ya pakati pa abale anu, ndi kuweruza kolungama pakati pa munthu ndi mbale wake, ndi mlendo wokhala naye.


Aweruzira ana amasiye ndi mkazi wamasiye; ndipo akonda mlendo, ndi kumpatsa chakudya ndi chovala.


M'mwemo mukondane naye mlendo; popeza munali alendo m'dziko la Ejipito.


Ndipo mukumbukire kuti munali akapolo m'dziko la Ejipito, ndipo Yehova Mulungu wanu anakuombolani; chifukwa chake ndikuuzani ichi lero lino.


akhale nanu, pakati panu, ku malo asankhako iye m'mudzi mwanu mwina momkonda; musamamsautsa.


Musamanyansidwa naye Mwedomu, popeza ndiye mbale wanu; musamanyansidwa naye Mwejipito, popeza munali alendo m'dziko lake.


Musamaipsa mlandu wa mlendo, kapena wa ana amasiye; kapena kutenga chikole chovala cha mkazi wamasiye;


Wotembereredwa iye wakuipsa mlandu wa mlendo, mwana wamasiye, ndi mkazi wamasiye. Ndi anthu onse anene, Amen.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa