Masalimo 14 - Buku LopatulikaAnthu oipadi ( Mas. 53 ) Kwa Mkulu wa Nyimbo. Salimo la Davide. 1 Wauchitsiru amati mumtima mwake, Kulibe Mulungu. Achita zovunda, achita ntchito zonyansa; kulibe wakuchita bwino. 2 Yehova mu Mwamba anaweramira pa ana a anthu, kuti aone ngati aliko wanzeru, wakufuna Mulungu. 3 Anapatuka onse; pamodzi anavunda mtima; palibe wakuchita bwino ndi mmodzi yense. 4 Kodi onse ochita zopanda pake sadziwa kanthu? Pakudya anthu anga monga akudya mkate, ndipo saitana pa Yehova. 5 Pamenepa anaopaopatu, pakuti Mulungu ali mu mbadwo wa wolungama. 6 Munyazitsa uphungu wa wozunzika, koma Yehova ndiye pothawira pake. 7 Mwenzi chipulumutso cha Israele chitachokera ku Ziyoni! Pakubweretsa Yehova anthu ake a m'nsinga, pamenepo adzakondwera Yakobo, nadzasekera Israele. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi