Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 14:2 - Buku Lopatulika

2 Yehova mu Mwamba anaweramira pa ana a anthu, kuti aone ngati aliko wanzeru, wakufuna Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

2 Yehova m'Mwamba anaweramira pa ana a anthu, kuti aone ngati aliko wanzeru, wakufuna Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

2 Chauta kumwambako waŵerama, akuyang'ana anthu pansi pano, kuti aone ngati angakhalepo mmodzi wanzeru wofunitsitsa Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

2 Yehova kumwamba wayangʼana pansi, kuyangʼana anthu onse kuti aone ngati alipo wina wanzeru, amene amafunafuna Mulungu.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 14:2
29 Mawu Ofanana  

Ndipo Yehova anatsikira kudzaona mzinda ndi nsanja imene analinkumanga ana a anthu.


ndidzatsikatu ndikaone ngati anachita monse monga kulira kwake kumene kunandifikira: ngati sanatero ndidzadziwa.


Ndipo Mulungu anaona dziko lapansi, ndipo taonani, linavunda; pakuti anthu onse anavunditsa njira yao padziko lapansi.


Koma zapezeka zokoma mwa inu, popeza mwazichotsa zifanizo m'dzikomo, mwalunjikitsanso mtima wanu kufuna Mulungu.


wakuika mtima wake kufuna Mulungu Yehova, Mulungu wa makolo ake, chinkana sanayeretsedwe monga mwa mayeretsedwe a malo opatulika.


Munthu nchiyani kuti akhale woyera, wobadwa ndi mkazi kuti akhale wolungama?


Wokhala nazo nzeru asamalire izi, ndipo azindikire zachifundo za Yehova.


Yehova ali mu Kachisi wake woyera, Yehova, mpando wachifumu wake uli mu Mwamba; apenyerera ndi maso ake, ayesa ana a anthu ndi zikope zake.


Ofatsa anachiona, nakondwera, ndipo inu, ofuna Mulungu, mtima wanu ukhale ndi moyo.


Sadziwa, ndipo sazindikira; amayendayenda mumdima; maziko onse a dziko lapansi agwedezeka.


Munthu wopulukira sachidziwa; ndi munthu wopusa sachizindikira ichi;


Pamenepo udzazindikira chilungamo ndi chiweruzo, zolunjika ndi mayendedwe onse abwino.


Achibwana inu, chenjerani, opusa inu, khalani ndi mtima wozindikira;


wachibwana ndani? Apatukire kuno. Ati kwa yense wopanda nzeru,


Wazibwana yense apatukire kuno; iti kwa yense wosowa nzeru,


Ponyala nthambi zake zidzathyoledwa; akazi adzafika, nazitentha ndi moto, pakuti ali anthu opanda nzeru; chifukwa chake Iye amene anawalenga sadzawachitira chisoni, ndi Iye amene anawaumba sadzawakomera mtima.


Funani Yehova popezeka Iye, itanani Iye pamene ali pafupi;


Tayang'anani kunsi kuchokera kumwamba, taonani pokhala panu poyera, ndi pa ulemerero wanu, changu chanu ndi ntchito zanu zamphamvu zili kuti? Mwanditsekerezera zofunafuna za mtima wanu ndi chisoni chanu.


Mwenzi mutang'amba kumwamba ndi kutsikira pansi, kuti mapiri agwedezeke pamaso panu;


Ndipo pamene iwo adzati kwa iwe, Funa kwa olaula, ndi obwebweta, amene alira pyepye, nang'ung'udza; kodi anthu sadzafuna kwa Mulungu wao? Chifukwa cha amoyo, kodi adzafuna kwa akufa?


Pakuti anthu anga apusa, sandidziwa Ine; ali ana opulukira sazindikira; ali ochenjera kuchita choipa koma kuchita chabwino sakudziwa.


Thamangani inu kwina ndi kwina m'miseu ya Yerusalemu, taonanitu, dziwani, ndi kufunafuna m'mabwalo ake, kapena mukapeza munthu, kapena alipo wakuchita zolungama, wakufuna choonadi; ndipo ndidzamkhululukira.


kufikira Yehova adzazolika kumwamba ndi kuona.


Ambiri adzadzitsuka ndi kudziyeretsa, nadzayesedwa ndi moto; koma oipa adzachita moipa; ndipo palibe mmodzi wa oipa adzazindikira; koma aphunzitsi ndiwo adzazindikira.


Chifukwa unalemera mtima wa anthu awa, ndipo m'makutu ao anamva mogontha, ndipo maso ao anatsinzina; kuti asaone konse ndi maso, asamve ndi makutu, asazindikire ndi mtima wao, asatembenuke, ndipo ndisawachiritse iwo.


palibe mmodzi wakudziwitsa, palibe mmodzi wakulondola Mulungu;


koma wopanda chikhulupiriro sikutheka kumkondweretsa; pakuti iye wakudza kwa Mulungu ayenera kukhulupirira kuti alipo, ndi kuti ali wobwezera mphotho iwo akumfuna Iye.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa