Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 14:5 - Buku Lopatulika

5 Pamenepa anaopaopatu, pakuti Mulungu ali mu mbadwo wa wolungama.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Pamenepa anaopaopatu, pakuti Mulungu ali mu mbadwo wa wolungama.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Tsonotu iwo adzachita mantha aakulu, pakuti Mulungu amakhala pa mbali ya anthu abwino.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Awo ali apowo, agwidwa ndi mantha aakulu, pakuti Mulungu ali mʼgulu la olungama.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 14:5
19 Mawu Ofanana  

Pamenepo mfumu Ahasuwero anati kwa mkazi wamkulu Estere, ndi kwa Mordekai Myuda, Taonani, ndampatsa Estere nyumba ya Hamani, ndi iyeyu anampachika pamtanda, chifukwa anatulutsa dzanja lake pa Ayuda.


Mbeu yake idzakhala yamphamvu padziko lapansi; mbadwo wa oongoka mtima udzadalitsidwa.


Mbumba ya anthu idzamtumikira; kudzanenedwa za Ambuye ku mibadwo yakudza.


Uwu ndi mbadwo wa iwo akufuna Iye, iwo akufuna nkhope yanu, Mulungu wa Yakobo.


Yehova wa makamu ali ndi ife, Mulungu wa Yakobo ndiye pamsanje pathu.


Mulungu ali m'kati mwake, sudzasunthika, Mulungu adzauthandiza mbandakucha.


Yehova wa makamu ali ndi ife; Mulungu wa Yakobo ndiye pamsanje pathu.


Pamenepo anaopa kwakukulu, popanda chifukwa cha kuopa, pakuti Mulungu anamwaza mafupa a iwo akuzinga iwe; unawachititsa manyazi, pakuti Mulungu anawakaniza.


ndikadati, Ndidzafotokozera chotere, taonani, ndikadachita chosakhulupirika ndi mbadwo wa ana ako.


Kuopa kwakukulu ndi mantha ziwagwera; padzanja lanu lalikulu akhala chete ngati mwala; kufikira apita anthu anu, Yehova, kufikira apita anthu amene mudawaombola.


Woipa athawa palibe momthamangitsa; koma olungama alimba mtima ngati mkango.


Tafuula, takuwa iwe, wokhala mu Ziyoni, chifukwa Woyera wa Israele wa m'kati mwako ali wamkulu.


usaope, pakuti Ine ndili pamodzi ndi iwe; usaopsedwe, pakuti Ine ndine Mulungu wako; ndidzakulimbitsa; inde, ndidzakuthangata; inde, ndidzakuchirikiza ndi dzanja langa lamanja la chilungamo.


Panganani upo, koma udzakhala chabe; nenani mau, koma sadzachitika; pakuti Mulungu ali pamodzi ndi ife.


Onani namwali adzaima, nadzabala mwana wamwamuna, ndipo adzamutcha dzina lake, Imanuele. Ndilo losandulika, Mulungu nafe.


Koma inu ndinu mbadwa yosankhika, ansembe achifumu, mtundu woyera mtima, anthu a mwini wake, kotero kuti mukalalikire zoposazo za Iye amene anakuitanani mutuluke mumdima, mulowe kuunika kwake kodabwitsa;


Ndipo kunali kunthunthumira kuzithando, kuthengoko, ndi pakati pa anthu onse; a ku kaboma ndi owawanya omwe ananthunthumira; ndi dziko linagwedezeka; chomwecho kunali kunthunthumira kwakukulu koposa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa