Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


108 Mau a m'Baibulo Okhudza Kupanda Chiyero

108 Mau a m'Baibulo Okhudza Kupanda Chiyero

Ndikufuna ndikuuzeni, bwenzi langa, kuti ngati tikulankhula za kuyenda mu kuunika kwa Mulungu, koma sitikutsatira Mawu Ake, ndipo tikuyembekezera ena kuti azitsatira, tikudinyenga tokha. Tikhoza kuona zotsatirapo zake zoipa m'miyoyo yathu. Monga mmene Baibulo limatiuza pa 1 Yohane 2:9, “Iye amene anena kuti ali m’kuunika, koma adana ndi mbale wake, ali mu mdima kufikira tsopano.”

Ubale wathu ndi Mulungu umadalira pa kutsatira ziphunzitso za Yesu ndi kutsanzira iye. N’zovuta nthawi zina, makamaka m’dziko lomwe nthawi zambiri limasokoneza zabwino ndi zoipa. Komabe, ndikofunikira kuti zochita zathu zionetse chikondi cha Mulungu. Mitima yathu iyenera kukhala yodzala ndi chikondi chenicheni ndi kuona mtima.

Nthawi zambiri timaona zolakwa za ena, koma sitiziona zathu. Tiyenera kuyesetsa kusintha maganizo athuwa oipa. Tiyeni tipemphe Mulungu kuti atipatse mtima wowona mtima tsiku lililonse. Ndikukhulumbira kuti Mulungu angatithandize kukhala anthu omwe amafuna kuti tikhale.




Mateyu 7:5

Wonyenga iwe! Tayamba kuchotsa m'diso lako mtandawo, ndipo pomwepo udzapenyetsa kuchotsa kachitsotso m'diso la mbale wako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 26:25

Pamene akometsa mau ake usamkhulupirire; pakuti m'mtima mwake muli zonyansa zisanu ndi ziwiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 52:4

ukonda mau onse akuononga, lilime lachinyengo, iwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 15:7-8

Onyenga inu! Yesaya ananenera bwino za inu, ndi kuti, Anthu awa andilemekeza Ine ndi milomo yao; koma mtima wao uli kutali ndi Ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 5:9

Pakuti m'kamwa mwao mulibe mau okhazikika; m'kati mwao m'mosakaza; m'mero mwao ndi manda apululu; lilime lao asyasyalika nalo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 4:20

Munthu akati, kuti, Ndikonda Mulungu, nadana naye mbale wake, ali wabodza: pakuti iye wosakonda mbale wake amene wamuona, sangathe kukonda Mulungu amene sanamuone.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:1-2

Yang'anirani kuti musachite zolungama zanu pamaso pa anthu kuti muonekere kwa iwo; pakuti ngati mutero mulibe mphotho ndi Atate wanu wa Kumwamba. Ufumu wanu udze. Kufuna kwanu kuchitidwe, monga Kumwamba chomwecho pansi pano. Mutipatse ife lero chakudya chathu chalero. Ndipo mutikhululukire mangawa athu, monga ifenso takhululukira amangawa anthu. Ndipo musatitengere kokatiyesa, koma mutipulumutse kwa woipayo. Pakuti ngati mukhululukira anthu zolakwa zao adzakhululukira inunso Atate wanu wa Kumwamba. Koma ngati simukhululukira anthu zolakwa zao, Atate wanunso sadzakhululukira zolakwa zanu. Ndipo pamene ponse musala kudya, musakhale ndi nkhope yachisoni, ngati onyengawo; pakuti aipitsa nkhope zao, kuti aonekere kwa anthu kuti alinkusala kudya. Indetu ndinena kwa inu, Iwo alandiriratu mphotho zao. Koma iwe, posala kudya, dzola mutu wako, ndi kusamba nkhope yako: kuti usaonekere kwa anthu kuti ulikusala kudya, koma kwa Atate wako ali m'tseri: ndipo Atate wako wakuona m'tseri adzakubwezera iwe. Musadzikundikire nokha chuma padziko lapansi, pamene njenjete ndi dzimbiri ziononga; ndi pamene mbala ziboola ndi kuba: Chifukwa chake pamene paliponse upatsa mphatso zachifundo, usamaomba lipenga patsogolo pako, monga amachita onyenga m'masunagoge, ndi m'makwalala, kotero kuti atamandidwe ndi anthu. Indetu ndinena kwa inu, Iwo alandiriratu mphotho zao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 26:23

Milomo yofunitsitsa ndi mtima woipa ikunga mbale yadothi anaimata ndi mphala ya siliva.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:15

Yang'anirani mupewe aneneri onyenga, amene adza kwa inu ndi zovala zankhosa, koma m'kati mwao ali mimbulu yolusa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:5

Ndipo pamene mupemphera, musakhale monga onyengawo; chifukwa iwo akonda kuimirira ndi kupemphera m'masunagoge, ndi pa mphambano za makwalala, kuti aonekere kwa anthu. Indetu ndinena kwa inu, Iwo alandiriratu mphotho zao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 3:5

akukhala nao maonekedwe a chipembedzo, koma mphamvu yake adaikana; kwa iwonso udzipatule.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 1:26

Ngati wina adziyesera ali wopembedza Mulungu, ndiye wosamanga lilime lake, koma adzinyenga mtima wake, kupembedza kwake kwa munthuyu nkopanda pake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 6:16

Ndipo pamene ponse musala kudya, musakhale ndi nkhope yachisoni, ngati onyengawo; pakuti aipitsa nkhope zao, kuti aonekere kwa anthu kuti alinkusala kudya. Indetu ndinena kwa inu, Iwo alandiriratu mphotho zao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:3-5

Ndipo upenya bwanji kachitsotso kali m'diso la mbale wako, koma mtanda uli m'diso la iwe mwini suuganizira? Kapena udzati bwanji kwa mbale wako, Tandilola ndichotse kachitsotso m'diso lako; ndipo ona, mtandawo ulimo m'diso lakoli. Wonyenga iwe! Tayamba kuchotsa m'diso lako mtandawo, ndipo pomwepo udzapenyetsa kuchotsa kachitsotso m'diso la mbale wako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 32:6

Pakuti wopusa adzanena zopusa, ndi mtima wake udzachita mphulupulu, kuchita zoipitsa, ndi kunena za Yehova molakwira, kusowetsa konse mtima wanjala, ndi kulepheretsa chakumwa cha waludzu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 11:29

Wovuta banja lake adzalowa m'zomsautsa; wopusa adzatumikira wanzeru.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 15:7-9

Onyenga inu! Yesaya ananenera bwino za inu, ndi kuti, Anthu awa andilemekeza Ine ndi milomo yao; koma mtima wao uli kutali ndi Ine. Koma andilambira Ine kwachabe, ndi kuphunzitsa maphunzitso, malangizo a anthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 22:18

Koma Yesu anadziwa kuipa kwao, nati, Mundiyeseranji Ine, onyenga inu?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 23:1-3

Pomwepo Yesu analankhula ndi makamu a anthu ndi ophunzira ake, Ndipo musatchedwa atsogoleri, pakuti alipo mmodzi Mtsogoleri wanu, ndiye Khristu. Koma wamkulu wopambana wa inu adzakhala mtumiki wanu. Ndipo aliyense amene akadzikuza yekha adzachepetsedwa; koma amene adzichepetsa mwini yekha adzakulitsidwa. Koma tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! Chifukwa mutsekera anthu Ufumu wa Kumwamba pamaso pao; pakuti inu nokha simulowamo, ndipo muwaletsa amene alikulowa, kuti asalowemo. Tsoka inu alembi ndi Afarisi, onyenga! Chifukwa mupitapita kunyanja ndi kumtunda kuyesa munthu mmodzi mtembenuki; ndipo m'mene akhala wotere, mumsandutsa mwana wa Gehena woposa inu kawiri. Tsoka inu, atsogoleri akhungu, amene munena, Amene aliyense akalumbira kutchula Kachisi, palibe kanthu; koma amene akalumbira kutchula golide wa Kachisi, wadzimangirira. Inu opusa, ndi akhungu: pakuti choposa nchiti, golide kodi, kapena Kachisi amene ayeretsa golideyo? Ndiponso, Amene aliyense akalumbira kutchula guwa la nsembe, palibe kanthu; koma amene akalumbira kutchula mtulo wa pamwamba pake wadzimangirira. Inu akhungu, pakuti choposa nchiti, mtulo kodi, kapena guwa la nsembe limene liyeretsa mtulowo? nanena, Alembi ndi Afarisi akhala pa mpando wa Mose; Chifukwa chake wakulumbira kutchula guwa la nsembe, alumbira limenelo ndi zonse za pamwamba pake. Ndipo wakulumbira kutchula Kachisi, alumbira ameneyo ndi Iye wakukhala momwemo. Ndipo wakulumbira kutchula Kumwamba, alumbira chimpando cha Mulungu, ndi Iye wakukhala pomwepo. Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! Chifukwa mupereka limodzi la magawo khumi la timbeu tonunkhira, ndi katsabola, ndi la chitowe, nimusiya zolemera za chilamulo, ndizo kuweruza kolungama, ndi kuchitira chifundo, ndi chikhulupiriro; koma zijazo munayenera kuzichita, osasiya izi zomwe. Atsogoleri akhungu inu, akukuntha udzudzu, koma mumeza ngamira. Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! Chifukwa mutsuka kunja kwake kwa chikho ndi mbale, koma m'katimo iwo adzala ndi kulanda ndi kusadziletsa. Mfarisi iwe wakhungu, yambawatsuka m'kati mwa chikho ndi mbale, kuti kunja kwake kukhalenso koyera. Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! Chifukwa mufanafana ndi manda opaka njereza, amene aonekera okoma kunja kwake, koma adzala m'katimo ndi mafupa a anthu akufa ndi zonyansa zonse. Chomwecho inunso muonekera olungama pamaso pa anthu, koma m'kati muli odzala ndi chinyengo ndi kusaweruzika. Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! Chifukwa mumanga nyumba za pa manda a aneneri, ndipo mukonza manda a anthu olungama, chifukwa chake zinthu zilizonse zimene iwo akauza inu, chitani nimusunge; koma musatsanza ntchito zao; pakuti iwo amalankhula, koma samachita.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 23:5

Koma amachita ntchito zao zonse kuti aonekere kwa anthu; pakuti akulitsa chitando chake cha njirisi zao, nakulitsa mphonje,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 23:13

Koma tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! Chifukwa mutsekera anthu Ufumu wa Kumwamba pamaso pao; pakuti inu nokha simulowamo, ndipo muwaletsa amene alikulowa, kuti asalowemo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 23:23-28

Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! Chifukwa mupereka limodzi la magawo khumi la timbeu tonunkhira, ndi katsabola, ndi la chitowe, nimusiya zolemera za chilamulo, ndizo kuweruza kolungama, ndi kuchitira chifundo, ndi chikhulupiriro; koma zijazo munayenera kuzichita, osasiya izi zomwe. Atsogoleri akhungu inu, akukuntha udzudzu, koma mumeza ngamira. Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! Chifukwa mutsuka kunja kwake kwa chikho ndi mbale, koma m'katimo iwo adzala ndi kulanda ndi kusadziletsa. Mfarisi iwe wakhungu, yambawatsuka m'kati mwa chikho ndi mbale, kuti kunja kwake kukhalenso koyera. Tsoka inu, alembi ndi Afarisi, onyenga! Chifukwa mufanafana ndi manda opaka njereza, amene aonekera okoma kunja kwake, koma adzala m'katimo ndi mafupa a anthu akufa ndi zonyansa zonse. Chomwecho inunso muonekera olungama pamaso pa anthu, koma m'kati muli odzala ndi chinyengo ndi kusaweruzika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 7:6

Ndipo Iye ananena nao, Yesaya ananenera bwino za inu onyenga, monga mwalembedwa, Anthu awa andilemekeza Ine ndi milomo yao, koma mtima wao ukhala kutali ndi Ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 12:15

Kodi tipereke kapena tisapereke? Koma Iye anadziwa chinyengo chao, nati kwa iwo, Mundiyeseranji? Nditengereni rupiya latheka, kuti ndilione. Ndipo analitenga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 6:41-42

Ndipo uyang'aniranji kachitsotso kali m'diso la mbale wako, koma mtanda wa m'diso la iwe mwini suuzindikira? Kapena ungathe bwanji kunena kwa mbale wako, Mbale iwe, leka ndichotse kachitsotso kali m'diso lako, wosayang'anira iwe mwini mtanda uli m'diso lako? Wonyenga iwe! Yamba wachotsa mtandawo m'diso lako, ndipo pomwepo udzayang'anitsa bwino kuchotsa kachitsotso ka m'diso la mbale wako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 11:39-44

Koma Ambuye anati kwa iye, Tsopano inu Afarisi muyeretsa kunja kwake kwa chikho ndi mbale, koma m'kati mwanu mudzala zolanda ndi zoipa. Ndipo mutikhululukire ife machimo athu; pakuti ifenso tikhululukira munthu yense wa mangawa athu. Ndipo musatitengere ife kokatiyesa. Opusa inu, kodi Iye wopanga kunja kwake sanapangenso m'kati mwake? Koma patsani mphatso yachifundo za m'katimo; ndipo onani, zonse zili zoyera kwa inu. Koma tsoka inu, Afarisi! Chifukwa mupereka limodzi la magawo khumi la timbeu tonunkhira, ndi timbeu tokometsa chakudya ndi ndiwo zonse, ndipo mumaleka chiweruzo ndi chikondi cha Mulungu; mwenzi mutachita izi, ndi kusasiya zinazo. Tsoka inu, Afarisi! Chifukwa mukonda mipando yaulemu m'masunagoge, ndi kupatsidwa moni m'misika. Tsoka inu! Chifukwa muli ngati manda osaoneka, ndipo anthu akuyendayenda pamwamba pao sadziwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 11:46

Ndipo anati, Tsoka inunso, achilamulo inu! Chifukwa musenzetsa anthu akatundu osautsa ponyamula, ndipo inu nomwe simukhudza akatunduwo ndi chala chanu chimodzi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 12:1-2

Pomwepo pamene anthu a zikwizikwi a khamu anasonkhana pamodzi, kotero kuti anapondana, Iye anayamba kunena kwa ophunzira ake poyamba, Tachenjerani nokha ndi chotupitsa mikate cha Afarisi, chimene chili chinyengo. Ndipo aliyense amene adzanenera Mwana wa Munthu zoipa adzakhululukidwa; koma amene anenera Mzimu Woyera zamwano sadzakhululukidwa. Ndipo pamene paliponse adzamuka nanu kumlandu wa m'sunagoge ndi kwa akulu, ndi aulamuliro, musade nkhawa ndi kuti mukadzikanira bwanji, ndipo ndi mau otani, kapena mukanena chiyani; pakuti Mzimu Woyera adzaphunzitsa inu nthawi yomweyo zimene muyenera kuzinena. Ndipo munthu wa m'khamulo anati kwa Iye, Mphunzitsi, uzani mbale wanga agawane ndi ine chuma chamasiye. Koma anati kwa iye, Munthu iwe, ndani anandiika Ine ndikhale woweruza, kapena wakugawira inu? Ndipo Iye anati kwa iwo, Yang'anirani, mudzisungire kupewa msiriro uliwonse; chifukwa moyo wake wa munthu sulingana ndi kuchuluka kwa zinthu zake ali nazo. Ndipo Iye ananena nao fanizo, kuti, Munda wake wa munthu mwini chuma unapatsa bwino. Ndipo anaganizaganiza mwa yekha nanena, Ndidzatani ine, popeza ndilibe mosungiramo zipatso zanga? Ndipo anati Ndidzatere: ndidzapasula nkhokwe zanga, ndi kumanganso zazikulu, ndipo ndidzasungiramo dzinthu zanga zonse, ndi chuma changa. Ndipo ndidzati kwa moyo wanga, Moyo iwe, uli nacho chuma chambiri chosungika kufikira zaka zambiri; tapumulatu, nudye, numwe, nukondwere. Koma kulibe kanthu kovundikiridwa kamene sikadzaululidwa; ndi kobisika kamene sikadzadziwika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 16:15

Ndipo anati kwa iwo, Inu ndinu odziyesera nokha olungama pamaso pa anthu; koma Mulungu azindikira mitima yanu; chifukwa ichi chimene chikuzika mwa anthu chili chonyansa pamaso pa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 7:24

Musaweruze monga maonekedwe, koma weruzani chiweruziro cholungama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 2:1-3

Chifukwa chake uli wopanda mau owiringula, munthu iwe, amene uli yense wakuweruza; pakuti m'mene uweruza wina, momwemo udzitsutsa iwe wekha, pakuti iwe wakuweruza, umachita zomwezo. koma ulemerero ndi ulemu ndi mtendere kwa munthu aliyense wakuchita zabwino, kuyambira Myuda, ndiponso Mgriki; pakuti Mulungu alibe tsankho. Pakuti onse amene anachimwa opanda lamulo adzaonongeka opanda lamulo; ndi onse amene anachimwa podziwa lamulo adzaweruzidwa ndi lamulo; pakuti akumvaimva lamulo sakhala olungama pamaso pa Mulungu, koma akuchita lamulo adzayesedwa olungama. Pakuti pamene anthu a mitundu akukhala opanda lamulo, amachita mwa okha za lamulo, omwewo angakhale alibe lamulo, adzikhalira okha ngati lamulo; popeza iwo aonetsa ntchito ya lamulolo yolembedwa m'mitima yao, ndipo chikumbumtima chao chichitiranso umboni pamodzi nao, ndipo maganizo ao wina ndi mnzake anenezana kapena akanirana; tsiku limene Mulungu adzaweruza ndi Khristu Yesu zinsinsi za anthu, monga mwa Uthenga wanga Wabwino. Koma ngati iwe unenedwa Myuda, nukhazikika palamulo, nudzitamandira pa Mulungu, nudziwa chifuniro chake, nuvomereza zinthu zoposa, utaphunzitsidwa m'chilamulo, nulimbika mumtima kuti iwe wekha uli wotsogolera wa akhungu, nyali ya amene akhala mumdima, Ndipo tidziwa kuti kuweruza kwa Mulungu kuli koona pa iwo akuchita zotere. wolangiza wa opanda nzeru, mphunzitsi wa tiana, wakukhala m'chilamulo ndi chionekedwe cha nzeru ndi cha choonadi; ndiwe tsono wakuphunzitsa wina, kodi ulibe kudziphunzitsa mwini? Iwe wakulalikira kuti munthu asabe, kodi ulikuba mwini wekha? Iwe wakunena kuti munthu asachite chigololo, kodi umachita chigololo mwini wekha? Iwe wakudana nao mafano, umafunkha za mu Kachisi kodi? Iwe wakudzitamandira pachilamulo, kodi uchitira Mulungu mwano ndi kulakwa kwako m'chilamulo? Pakuti dzina la Mulungu lichitidwa mwano chifukwa cha inu, pakati pa anthu a mitundu, monga mwalembedwa. Pakuti inde mdulidwe uli wabwino, ngati iwe umachita lamulo; koma ngati uli wolakwira lamulo, mdulidwe wako wasanduka kusadulidwa. Chifukwa chake ngati wosadulidwa asunga zoikika za chilamulo, kodi kusadulidwa kwake sikudzayesedwa ngati mdulidwe? Ndipo kusadulidwa, kumene kuli kwa chibadwidwe, ngati kukwanira chilamulo, kodi sikudzatsutsa iwe, amene uli nao malembo ndi mdulidwe womwe, ndiwe wolakwira lamulo? Pakuti siali Myuda amene akhala wotere pamaso, kapena suli mdulidwe umene uli wotere pamaso, m'thupimo; koma Myuda ndiye amene akhala wotere mumtima; ndipo mdulidwe uli wa mtima, mumzimu, si m'malembo ai; kuyamika kwake sikuchokera kwa anthu, koma kwa Mulungu. Ndipo uganiza kodi, munthu iwe, amene umaweruza iwo akuchita zotere, ndipo uzichitanso iwe mwini, kuti udzapulumuka pa mlandu wa Mulungu?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 2:17-24

Koma ngati iwe unenedwa Myuda, nukhazikika palamulo, nudzitamandira pa Mulungu, nudziwa chifuniro chake, nuvomereza zinthu zoposa, utaphunzitsidwa m'chilamulo, nulimbika mumtima kuti iwe wekha uli wotsogolera wa akhungu, nyali ya amene akhala mumdima, Ndipo tidziwa kuti kuweruza kwa Mulungu kuli koona pa iwo akuchita zotere. wolangiza wa opanda nzeru, mphunzitsi wa tiana, wakukhala m'chilamulo ndi chionekedwe cha nzeru ndi cha choonadi; ndiwe tsono wakuphunzitsa wina, kodi ulibe kudziphunzitsa mwini? Iwe wakulalikira kuti munthu asabe, kodi ulikuba mwini wekha? Iwe wakunena kuti munthu asachite chigololo, kodi umachita chigololo mwini wekha? Iwe wakudana nao mafano, umafunkha za mu Kachisi kodi? Iwe wakudzitamandira pachilamulo, kodi uchitira Mulungu mwano ndi kulakwa kwako m'chilamulo? Pakuti dzina la Mulungu lichitidwa mwano chifukwa cha inu, pakati pa anthu a mitundu, monga mwalembedwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:9

Chikondano chikhale chopanda chinyengo. Dana nacho choipa; gwirizana nacho chabwino.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 5:6-8

Kudzitamanda kwanu sikuli bwino. Kodi simudziwa kuti chotupitsa pang'ono chitupitsa mtanda wonse? Tsukani chotupitsa chakale, kuti mukakhale mtanda watsopano, monga muli osatupa. Pakutinso Paska wathu waphedwa, ndiye Khristu; chifukwa chake tichita phwando, si ndi chotupitsa chakale, kapena ndi chotupitsa cha dumbo, ndi kuipa mtima, koma ndi mkate wosatupa wa kuona mtima, ndi choonadi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 13:1-3

Ndingakhale ndilankhula malilime a anthu, ndi a angelo, koma ndilibe chikondi, ndikhala mkuwa woomba, kapena nguli yolira. Koma pamene changwiro chafika, tsono chamderamdera chidzakhala chabe. Pamene ndinali mwana, ndinalankhula ngati mwana, ndinalingirira ngati mwana, ndinawerenga ngati mwana; tsopano ndakhala munthu, ndayesa chabe zachibwana. Pakuti tsopano tipenya m'kalirole, ngati chimbuuzi; koma pomwepo maso ndi maso. Tsopano ndizindikira mderamdera; koma pomwepo ndidzazindikiratu, monganso ndazindikiridwa. Ndipo tsopano zitsala zitatu izi: chikhulupiriro, chiyembekezo, chikondi; koma chachikulu cha izi ndicho chikondi. Ndipo ndingakhale ndikhoza kunenera, ndipo ndingadziwe zinsinsi zonse, ndi nzeru zonse, ndipo ndingakhale ndili nacho chikhulupiriro chonse, kuti ndikasendeza mapiri, koma ndilibe chikondi, ndili chabe. Ndipo ndingakhale ndipereka chuma changa chonse kudyetsa osauka, ndipo ndingakhale ndipereka thupi langa alitenthe m'moto, koma ndilibe chikondi, sindipindula kanthu ai.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 11:13-15

Pakuti otere ali atumwi onyenga, ochita ochenjerera, odzionetsa ngati atumwi a Khristu. Ndipo kulibe kudabwa; pakuti Satana yemwe adzionetsa ngati mngelo wa kuunika. Chifukwa chake sikuli kanthu kwakukulu ngatinso atumiki ake adzionetsa monga atumiki a chilungamo; amene chimaliziro chao chidzakhala monga ntchito zao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 2:11-13

Koma pamene Kefa anadza ku Antiokeya ndinatsutsana naye pamaso pake, pakuti anatsutsika wolakwa. Pakuti asanafike ena ochokera kwa Yakobo, anadya pamodzi ndi amitundu; koma atadza iwo, anadzibweza, ndi kudzipatula yekha, pakuopa iwo a ku mdulidwe. Ndipo Ayuda otsala anawagwiranso m'maso pamodzi naye; kotero kuti Barnabasinso anatengedwa ndi kugwira m'maso kwao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Agalatiya 5:9

Chotupitsa pang'ono chitupitsa mtanda wonse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:25

Mwa ichi, mutataya zonama, lankhulani zoona yense ndi mnzake; pakuti tili ziwalo wina ndi mnzake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 5:6-7

Asakunyengeni inu munthu ndi mau opanda pake, pakuti chifukwa cha izi umadza mkwiyo wa Mulungu pa ana a kusamvera. Chifukwa chake musakhale olandirana nao;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 1:15-18

Enatu alalikiranso Khristu chifukwa cha kaduka ndi ndeu; koma enanso chifukwa cha kukoma mtima; ena atero ndi chikondi, podziwa kuti anandiika ndichite chokanira cha Uthenga Wabwino; koma ena alalikira Khristu mochokera m'chotetana, kosati koona, akuyesa kuti adzandibukitsira chisautso m'zomangira zanga. Potero nchiyani? Chokhacho kuti monsemo, ngati pamaso pokha, ngati m'choonadi, Khristu alalikidwa; ndipo m'menemo ndikondwera, komanso ndidzakondwera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Afilipi 2:3

musachite kanthu monga mwa chotetana, kapena monga mwa ulemerero wopanda pake, komatu ndi kudzichepetsa mtima, yense ayese anzake omposa iye mwini;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 2:23

Zimene zili naotu manenedwe a nzeru m'kutumikira kwa chifuniro cha mwini wake, ndi kudzichepetsa, ndi kusalabadira thupi; koma zilibe mphamvu konse yakuletsa chikhutitso cha thupi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:9

musamanamizana wina ndi mnzake; popeza mudavula munthu wakale pamodzi ndi ntchito zake,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 2:5

Pakuti sitinayende nao mau osyasyalika nthawi iliyonse monga mudziwa, kapena kupsinjika msiriro, mboni ndi Mulungu;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Atesalonika 5:21-22

Yesani zonse; sungani chokomacho, Mupewe maonekedwe onse a choipa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 1:5-6

koma chitsirizo cha chilamuliro ndicho chikondi chochokera mu mtima woyera ndi m'chikumbu mtima chokoma ndi chikhulupiriro chosanyenga; zimenezo, ena pozilambalala anapatukira kutsata mau opanda pake;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 4:1-2

Koma Mzimu anena monenetsa, kuti m'masiku otsiriza ena adzataya chikhulupiriro, ndi kusamala mizimu yosocheretsa ndi maphunziro a ziwanda, Pakuti kukalingako tigwiritsa ntchito ndi kuyesetsa, chifukwa chiyembekezo chathu tili nacho pa Mulungu wamoyo, amene ali Mpulumutsi wa anthu onse, makamaka wa okhulupirira. Lamulira izi, nuziphunzitse. Munthu asapeputse ubwana wako; komatu khala chitsanzo kwa iwo okhulupirira, m'mau, m'mayendedwe, m'chikondi, m'chikhulupiriro, m'kuyera mtima. Kufikira ndidza ine, usamalire kuwerenga, kuchenjeza, kulangiza. Usanyalapse mphatsoyo ili mwa iwe, yopatsidwa kwa iwe mwa chinenero, pamodzi ndi kuika kwa manja a akulu. Izi uzisamalitse; mu izi ukhale; kuti kukula mtima kwako kuonekere kwa onse. Udzipenyerere wekha, ndi chiphunzitsocho. Uzikhala mu izi; pakuti pochita ichi udzadzipulumutsa iwe wekha ndi iwo akumva iwe. m'maonekedwe onyenga a iwo onena mabodza, olochedwa m'chikumbu mtima mwao monga ndi chitsulo chamoto;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 5:24-25

Zochimwa za anthu ena zili zooneka kale, zitsogola kunka kumlandu; koma enanso ziwatsata. Momwemonso pali ntchito zokoma zinaonekera kale; ndipo zina zosati zotere sizingathe kubisika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Tito 1:15-16

Zonse ziyera kwa iwo amene ayera mtima; koma kwa iwo odetsedwa ndi osakhulupirira kulibe kanthu koyera; komatu zadetsedwa nzeru zao ndi chikumbumtima chao. Avomereza kuti adziwa Mulungu, koma ndi ntchito zao amkana Iye, popeza ali onyansitsa, ndi osamvera, ndi pa ntchito zonse zabwino osatsimikizidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Tito 3:3

Pakuti kale ifenso tinali opusa, osamvera, onyengeka, akuchitira ukapolo zilakolako ndi zokondweretsa za mitundumitundu, okhala m'dumbo ndi njiru, odanidwa, odana wina ndi mnzake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ahebri 10:22

tiyandikire ndi mtima woona, m'chikhulupiriro chokwanira, ndi mitima yathu yowazidwa kuichotsera chikumbumtima choipa, ndi matupi athu osambitsidwa ndi madzi oyera;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 1:22

Khalani akuchita mau, osati akumva okha, ndi kudzinyenga nokha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 3:10-12

Mochokera m'kamwa momwemo mutuluka chiyamiko ndi temberero. Abale anga, izi siziyenera kutero. Kodi kasupe atulutsira pa uno womwewo madzi okoma ndi owawa? Kodi mkuyu ukhoza kubala azitona, abale anga, kapena mpesa kubala nkhuyu? Kotero madzi amchere sangathe kutulutsa okoma.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 4:4

Akazi achigololo inu, kodi simudziwa kuti ubwenzi wa dziko lapansi uli udani ndi Mulungu? Potero, iye amene afuna kukhala bwenzi la dziko lapansi adziika mdani wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 1:22

Popeza mwayeretsa moyo wanu pakumvera choonadi kuti mukakonde abale ndi chikondi chosanyenga, mukondane kwenikweni kuchokera kumtima;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 2:1

Momwemo pakutaya choipa chonse, ndi chinyengo chonse, ndi maonekedwe onyenga, ndi kaduka, ndi masinjiriro onse,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 3:10-11

Pakuti, Iye wofuna kukonda moyo, ndi kuona masiku abwino, aletse lilime lake lisanene choipa, ndi milomo yake isalankhule chinyengo; ndipo apatuke pachoipa, nachite chabwino; afunefune mtendere ndi kuulondola.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 3:16

ndi kukhala nacho chikumbumtima chabwino, kuti umo akunenerani, iwo akunenera konama mayendedwe anu abwino mu Khristu akachitidwe manyazi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 4:8

koposa zonse mukhale nacho chikondano chenicheni mwa inu nokha; pakuti chikondano chikwiriritsa unyinji wa machimo;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 1:6

Tikati kuti tiyanjana ndi Iye, ndipo tiyenda mumdima, tinama, ndipo sitichita choonadi;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 2:4

Iye wakunena kuti, Ndimdziwa Iye, koma wosasunga malamulo ake, ali wabodza, ndipo mwa iye mulibe choonadi;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Yohane 3:18

Tiana, tisakonde ndi mau, kapena ndi lilime, komatu ndi kuchita ndi m'choonadi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yuda 1:4

Pakuti pali anthu ena anakwawira m'tseri, ndiwo amene aja adalembedwa maina ao kale, kukalandira chitsutso ichi, anthu osapembedza, akusandutsa chisomo cha Mulungu wathu chikhale chilakolako chonyansa, nakaniza Mfumu wayekha, ndi Ambuye wathu, Yesu Khristu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yuda 1:16

Amenewo ndiwo odandaula, oderera, akuyenda monga mwa zilakolako zao (ndipo pakamwa pao alankhula zazikuluzikulu), akutama anthu chifukwa cha kupindula nako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 26:4

Sindinakhala pansi ndi anthu achabe; kapena kutsagana nao anthu othyasika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 50:16-17

Koma kwa woipa Mulungu anena, Uli nao chiyani malemba anga kulalikira, ndi kutchula pangano langa pakamwa pako? Popeza udana nacho chilangizo, nufulatira mau anga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 55:21

Pakamwa pake mposalala ngati mafuta amkaka, koma mumtima mwake munali nkhondo, mau ake ngofewa ngati mafuta oyenga, koma anali malupanga osololasolola.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 78:36-37

Koma anamsyasyalika pakamwa pao, namnamiza ndi lilime lao. Popeza mtima wao sunakonzekere Iye, ndipo sanakhazikike m'chipangano chake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 101:7

Wakuchita chinyengo sadzakhala m'kati mwa nyumba yanga; wakunena mabodza sadzakhazikika pamaso panga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 11:9

Wonyoza Mulungu aononga mnzake ndi m'kamwa mwake; koma olungama adzapulumuka pakudziwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 11:20

Okhota mtima anyansa Yehova; koma angwiro m'njira zao amsekeretsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 15:8

Nsembe ya oipa inyansa Yehova; koma pemphero la oongoka mtima limkondweretsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 16:2

Njira zonse za munthu ziyera pamaso pake; koma Yehova ayesa mizimu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 20:6

Anthu ambiri abukitsa yense kukoma mtima kwake; koma ndani angapeze munthu wokhulupirika?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 21:27

Nsembe ya oipa inyansa; makamaka pakudza nayo iwo mwachiwembu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 23:7

Pakuti monga asinkha m'kati mwake, ali wotere; ati kwa iwe, Idya numwe; koma mtima wake suli pa iwe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 26:23-26

Milomo yofunitsitsa ndi mtima woipa ikunga mbale yadothi anaimata ndi mphala ya siliva. Wakuda mnzake amanyenga ndi milomo yake; koma akundika chinyengo m'kati mwake. Pamene akometsa mau ake usamkhulupirire; pakuti m'mtima mwake muli zonyansa zisanu ndi ziwiri. Angakhale abisa udani wake pochenjera, koma udyo wake udzavumbulutsidwa posonkhana anthu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Miyambo 28:13

Wobisa machimo ake sadzaona mwai; koma wakuwavomereza, nawasiya adzachitidwa chifundo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 1:11-15

Nditani nazo nsembe zanu zochulukazo? Ati Yehova; ndakhuta nazo nsembe zopsereza za nkhosa zamphongo ndi mafuta a nyama zonenepa; sindisekera ndi mwazi wa ng'ombe zamphongo, ngakhale wa anaankhosa, ngakhale wa atonde. Pakudzaonekera inu pamaso pa Ine, ndani wafuna chimenechi m'dzanja lanu, kupondaponda m'mabwalo mwanga? Musadze nazonso, nsembe zachabechabe; nsembe zofukiza zindinyansa; tsiku lokhala mwezi ndi Sabata, kumema misonkhano, sindingalole mphulupulu ndi misonkhano. Masiku anu okhala mwezi ndi nthawi ya zikondwerero zanu mtima wanga uzida; zindivuta Ine; ndalema ndi kupirira nazo. Ndipo pamene mutambasula manja anu, ndidzakubisirani inu maso anga; inde pochulukitsa mapemphero anu Ine sindidzamva; manja anu adzala mwazi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 29:13

Ndipo Ambuye anati, Popeza anthu awa ayandikira ndi Ine ndi m'kamwa mwao, nandilemekeza ndi milomo yao, koma mtima wao uli kutali ndi Ine, ndi mantha ao akundiopa Ine, ndi lamulo la anthu analiphunzira;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 48:1

Imvani inu ichi, banja la Yakobo, amene mutchedwa ndi dzina la Israele, amene munatuluka m'madzi a Yuda amene mulumbira dzina la Yehova ndi kutchula dzina la Mulungu wa Israele, koma si m'zoona, pena m'chilungamo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 9:8

Lilime lao ndi muvi wakuphera; linena manyengo; wina anena mtendere ndi mnansi wake pakamwa pake, koma m'mtima mwake amlalira.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 33:31-32

Ndipo akudzera monga amadzera anthu, nakhala pansi pamaso pako ngati anthu anga, namva mau ako, koma osawachita; pakuti pakamwa pao anena mwachikondi, koma mtima wao utsata phindu lao. Ndipo taona, akuyesa iwe ngati nyimbo yachikondi ya woimba bwino, woimba limba bwino; pakuti akumva mau ako, koma osawachita.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Hoseya 6:6

Pakuti ndikondwera nacho chifundo, si nsembe ai; ndi kumdziwa Mulungu kuposa nsembe zopsereza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Amosi 5:21-24

Ndidana nao, ndinyoza zikondwerero zanu, sindidzakondwera nayo misonkhano yanu yoletsa. Inde, mungakhale mupereka kwa Ine nsembe zanu zopsereza, ndi nsembe zaufa, sindidzazilandira Ine; ndi nsembe zoyamika za ng'ombe zanu zonenepa, sindidzazisamalira Ine. Mundichotsere phokoso la nyimbo zanu; sindifuna kumva mayimbidwe a zisakasa zanu. Koma chiweruzo chiyende ngati madzi, ndi chilungamo ngati mtsinje wosefuka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mika 6:6-8

Ndidzafika kwa Yehova ndi chinai, ndi kuwerama kwa Mulungu Wam'mwamba? Kodi ndifike kwa Iye ndi nsembe zopsereza, ndi anaang'ombe a chaka chimodzi? Kodi Yehova adzakondwera nazo nkhosa zamphongo zikwi, kapena ndi mitsinje ya mafuta zikwi khumi? Kodi ndipereke mwana wanga woyamba chifukwa cha kulakwa kwanga, chipatso cha thupi langa chifukwa cha kuchimwa kwa moyo wanga? Iye anakuuza, munthuwe, chomwe chili chokoma; ndipo Yehova afunanji nawe koma kuti uchite cholungama, ndi kukonda chifundo ndi kuyenda modzichepetsa ndi Mulungu wako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Zekariya 7:5-6

Nena kwa anthu onse a m'dziko, ndi kwa ansembe, kuti, Muja mukasala ndi kulira mwezi wachisanu, ndi wachisanu ndi chitatu, zaka izi makumi asanu ndi awiri, kodi mukasalira Ine, Inedi? Ndipo pamene mukadya si ndinu, mukamwa si ndinu kodi?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Malaki 1:6-8

Mwana alemekeza atate wake, ndi mnyamata mbuye wake; ngati Ine tsono ndine atate, uli kuti ulemu wanga? Ngati Ine ndine mbuye, kundiopa kuli kuti? Ati Yehova wa makamu kwa inu ansembe akupeputsa dzina langa. Ndipo mukuti, Tapeputsa dzina lanu motani? Mupereka mkate wodetsedwa paguwa langa la nsembe; ndipo mukuti, Takudetsani motani? M'menemo, mwakuti munena, Gome la Yehova nlonyozeka. Ndipo pamene mupereka yakhungu ikhale nsembe, mukuti, Palibe choipa! Ndi popereka yotsimphina ndi yodwala, palibe choipa! Kaiperekeni kwa kazembe wanu, mudzamkomera kodi? Kapena adzakuvomerezani kodi? Ati Yehova wa makamu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Malaki 1:13-14

Mukutinso, Taonani, ncholemetsa ichi! Ndipo mwachipeputsa, ati Yehova wa makamu; ndipo mwabwera nazo zofunkha, ndi zotsimphina, ndi zodwala; momwemo mubwera nayo nsembe; kodi ndiyenera kuilandira kudzanja lanu? Ati Yehova. Koma wotembereredwa wonyengayo, wokhala nayo yaimuna m'gulu lake, nawinda, naphera Yehova nsembe chinthu chachilema; pakuti Ine ndine mfumu yaikulu, ati Yehova wa makamu; ndipo dzina langa ndi loopsa pakati pa amitundu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 23:33

Njoka inu, obadwa inu a mamba, mudzatha bwanji kuthawa kulanga kwake kwa Gehena?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 12:38-40

Ndipo m'chiphunzitso chake ananena, Yang'anirani mupewe alembi, akufuna kuyendayenda ovala miinjiro, ndi kulonjeredwa pamisika, ndi kukhala nayo mipando yaulemu m'sunagoge, ndi malo aulemu pamaphwando: Ndipo anatumanso kapolo wina kwa iwo; ndipo ameneyu anamlasa mutu, namchitira zomchititsa manyazi. amenewo alusira nyumba za akazi amasiye, napemphera monyenga mau ambiri; amenewa adzalandira kulanga koposa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 9:41

Yesu anati kwa iwo, Mukadakhala osaona simukadakhala nalo tchimo; koma tsopano munena, kuti, Tipenya: tchimo lanu likhala.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 2:21-23

ndiwe tsono wakuphunzitsa wina, kodi ulibe kudziphunzitsa mwini? Iwe wakulalikira kuti munthu asabe, kodi ulikuba mwini wekha? Iwe wakunena kuti munthu asachite chigololo, kodi umachita chigololo mwini wekha? Iwe wakudana nao mafano, umafunkha za mu Kachisi kodi? Iwe wakudzitamandira pachilamulo, kodi uchitira Mulungu mwano ndi kulakwa kwako m'chilamulo?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 3:13

M'mero mwao muli manda apululu; ndi lilime lao amanyenga; ululu wa mamba uli pansi pa milomo yao;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 16:17-18

Ndipo ndikudandaulirani, abale, yang'anirani iwo akuchita zopatutsana ndi zophunthwitsa, kosalingana ndi chiphunzitsocho munachiphunzira inu; ndipo potolokani pa iwo. Pakuti otere satumikira Ambuye wathu Khristu, koma mimba yao; ndipo ndi mau osalaza ndi osyasyalika asocheretsa mitima ya osalakwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 15:33

Musanyengedwe; mayanjano oipa aipsa makhalidwe okoma.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 10:17-18

Koma iye wodzitamandira adzitamandire mwa Ambuye; pakuti si iye amene adzitama yekha, koma iye amene Ambuye amtama ali wovomerezeka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Akorinto 11:20

Pakuti mulola ngati wina akuyesani inu akapolo, ngati wina alikwira inu, ngati wina alanda zanu, ngati wina adzikuza, ngati wina akupandani pankhope.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 4:14

Kuti tisakhalenso makanda, ogwedezekagwedezeka, natengekatengeka ndi mphepo yonse ya chiphunzitso, ndi tsenga la anthu, ndi kuchenjerera kukatsata chinyengo cha kusocheretsa;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aefeso 5:6

Asakunyengeni inu munthu ndi mau opanda pake, pakuti chifukwa cha izi umadza mkwiyo wa Mulungu pa ana a kusamvera.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:5-6

Chifukwa chake fetsani ziwalozo zili padziko; dama, chidetso, chifunitso chamanyazi, chilakolako choipa, ndi chisiriro, chimene chili kupembedza mafano; chifukwa cha izi zomwe ukudza mkwiyo wa Mulungu pa ana a kusamvera;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 6:5

makani opanda pake a anthu oipsika nzeru ndi ochotseka choonadi, akuyesa kuti chipembedzo chipindulitsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 4:3-4

Pakuti idzafika nthawi imene sadzalola chiphunzitso cholamitsa; komatu poyabwa m'khutu adzadziunjikitsa aphunzitsi monga mwa zilakolako za iwo okha: ndipo adzalubza dala pachoonadi, nadzapatukira kutsata nthano zachabe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Tito 1:10-11

Pakuti alipo ambiri osamvera mau, olankhula zopanda pake, ndi onyenga, makamaka iwo akumdulidwe, amene ayenera kutsekedwa pakamwa; ndiwo amene apasula mabanja banja lonse, ndi kuphunzitsa zosayenera chifukwa cha chisiriro chonyansa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Ambuye Mulungu wanga, Atate wabwino, zikomo chifukwa cha kukhalapo kwanu kwabwino m'moyo wanga. Mwachita zinthu zabwino kwa ine, simunandipusitsepo. Ambuye, pothawirapo panga lokhazikika, ndimalambira dzina lanu. Atate Woyera, ndikudziwa kuti ndikufunika kukhalapo kwanu ndi kuchotsa chilichonse chomwe chili mumtima mwanga. Sindikufuna kukhala munthu yemweyo, wokhala moyo wodzionetsera ndi chinyengo, woweruza ndi kutsutsa zomwe sindikuzidziwa, wonena za moyo wa ena pomwe wanga uli chisokonezo. Ndikudziwa kuti ndalankhula mopanda ulemu kwa iwo omwe anandithandiza m'njira zosiyanasiyana, pomwe inu m'mawu mwanu mukuti: "Tisakhale achinyengo, choyamba tichotse mtanda m'diso lathu, ndipo tidzatha kuona bwino kuti tichotse kathumba m'diso la m'bale wathu." Ambuye, ndithandizeni kusintha khalidwe langa lachinyengo lomwe landibweretsera mavuto m'moyo wanga, lomwe landipangitsa kuti ndikane ndi anthu omwe amandizungulira. Sinthani maganizo anga kuti ndikhale munthu wowona mtima wopanda choopa, ndisiye tsankho, chifukwa monga momwe ndimaweruzira ena, ndidzaweruzidwanso, ndipo ndi muyeso womwe ndimayesera ena, ndidzayesedwanso. Ndidalitseni kuti ndiyende motsatira mawu anu ndi kuphunzira kukhala moyo woopa inu, kuti Mzimu wanu Woyera ukhale mfumu m'moyo wanga kuti ndiyende m'chifuniro chanu tsiku lililonse ndikusiya chilichonse chomwe chimandizungulira. Ndikukana chinyengo chilichonse chomwe chingakhale mwa ine. M'dzina la Yesu. Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa