Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Luka 11:46 - Buku Lopatulika

46 Ndipo anati, Tsoka inunso, achilamulo inu! Chifukwa musenzetsa anthu akatundu osautsa ponyamula, ndipo inu nomwe simukhudza akatunduwo ndi chala chanu chimodzi.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

46 Ndipo anati, Tsoka inunso, achilamulo inu! Chifukwa musenzetsa anthu akatundu osautsa ponyamula, ndipo inu nomwe simukhudza akatunduwo ndi chala chanu chimodzi.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

46 Yesu adati, “Muli ndi tsokanso, inu akatswiri a Malamulo, chifukwa mumasenzetsa anthu katundu wosautsa kunyamula, pamene inuyo simumkhudzako mpang'ono pomwe.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

46 Yesu anayankha kuti, “Tsoka kwa inunso akatswiri a Malamulo chifukwa mumawalemetsa anthu ndi mtolo umene iwo sangathe kunyamula, ndipo inu eni ake simutenga chala chanu kuti muwathandize.

Onani mutuwo Koperani




Luka 11:46
7 Mawu Ofanana  

Tsoka kwa iwo amene alamulira malamulo osalungama, ndi kwa alembi olemba mphulupulu;


Kodi kumeneku si kusala kudya kumene ndinakusankha: kumasula nsinga za zoipa, ndi kumasula zomanga goli, ndi kuleka otsenderezedwa amuke mfulu, ndi kuti muthyole magoli onse?


Ndipo mmodzi wa iwo, mphunzitsi wa malamulo, anamfunsa ndi kumuyesa Iye, nati,


Ndipo mmodzi wa achilamulo anayankha, nanena kwa Iye, Mphunzitsi, ndi kunena izi, mutitonza ifenso.


Tsoka inu, achilamulo! Chifukwa munachotsa chifungulo cha nzeru; inu simunalowamo nokha, ndipo munawaletsa iwo analinkulowa.


Pakuti angakhale iwo omwe odulidwa sasunga lamulo; komatu afuna inu mudulidwe, kuti akadzitamandire m'thupi lanu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa