Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 9:8 - Buku Lopatulika

8 Lilime lao ndi muvi wakuphera; linena manyengo; wina anena mtendere ndi mnansi wake pakamwa pake, koma m'mtima mwake amlalira.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

8 Lilime lao ndi muvi wakuphera; linena manyengo; wina anena mtendere ndi mnansi wake pakamwa pake, koma m'mtima mwake amlalira.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

8 Lilime lao lili ngati muvi wakuthwa. Aliyense pakamwa pake pamatuluka mau aubwenzi, m'menemo mumtima mwake akukonzekera zomchita mnzake chiwembu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

8 Lilime lawo lili ngati muvi wakuthwa; limayankhula zachinyengo. Aliyense ndi pakamwa pake amayankhula mawu achikondi kwa mnansi wake, koma mu mtima mwake amakonzekera zomuchita chiwembu.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 9:8
21 Mawu Ofanana  

Pofikanso Abinere ku Hebroni, Yowabu anampambutsa kupita naye pakati pa chipata kulankhula naye poduka mphepo; namgwaza pomwepo m'mimba, nafa, chifukwa cha mwazi wa Asahele mbale wake.


Amanena za bodza munthu yense ndi mnansi wake, amanena ndi mlomo wothyasika, ndi mitima iwiri.


Yehova adzadula milomo yonse yothyasika, lilime lakudzitamandira;


Adzakuninkhanji, adzakuonjezeranji, lilime lonyenga iwe?


Musandikoke kundichotsa pamodzi ndi oipa, ndi ochita zopanda pake; amene alankhula zamtendere ndi anansi ao, koma mumtima mwao muli choipa.


Pakuti salankhula zamtendere, koma apangira chiwembu odekha m'dziko.


Pakamwa pake mposalala ngati mafuta amkaka, koma mumtima mwake munali nkhondo, mau ake ngofewa ngati mafuta oyenga, koma anali malupanga osololasolola.


Moyo wanga uli pakati pa mikango; ndigona pakati pa oyaka moto, ndiwo ana a anthu amene mano ao ali nthungo ndi mivi, ndipo lilime lao ndilo lupanga lakuthwa.


Moyo wanga, ukhalire chete Mulungu yekha; pakuti chiyembekezo changa chifuma kwa Iye.


Adzawakhumudwitsa, lilime lao lidzawatsutsa; onse akuwaona adzawathawa.


Wochitira mnzake umboni wonama ndiye chibonga, ndi lupanga, ndi muvi wakuthwa.


Pakuti mwa anthu anga aoneka anthu oipa; adikira monga akutcha misampha; atcha khwekhwe, agwira anthu.


Kodi sindidzawalanga chifukwa cha zimenezi? Ati Yehova; kodi moyo wanga sudzabwezera chilango mtundu woterewu?


Ndipo apinda lilime lao ngati uta wao, liname; koma akula mphamvu m'dzikomo, koma si pachoonadi; pakuti alinkunkabe nachita zoipa, ndipo sandidziwa Ine, ati Yehova.


Muchenjere naye yense mnansi wake, musakhulupirire yense mbale wake; pakuti abale onse amanyenga, ndipo anansi onse adzayenda ndi maugogodi.


Ndipo yense adzanyenga mnansi wake, osanena choonadi; aphunzitsa lilime lao kunena zonama; nadzithodwetsa kuchita zoipa.


Pakuti anthu ake olemera adzala ndi chiwawa, ndi okhalamo amanena bodza, ndi lilime lao limachita monyenga m'kamwa mwao.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa