Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Yeremiya 9:9 - Buku Lopatulika

9 Kodi sindidzawalanga chifukwa cha izi? Ati Yehova; kodi moyo wanga sudzabwezera chilango mtundu wotere?

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Kodi sindidzawalanga chifukwa cha izi? Ati Yehova; kodi moyo wanga sudzabwezera chilango mtundu wotere?

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Kodi zimenezi ndipanda kuŵalanga nazo? Monga ndisaulipsire mtundu wotere wa anthu?” Akutero Chauta

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Kodi ndilekerenji kuwalanga chifukwa cha zimenezi? akutero Yehova. ‘Kodi ndisawulipsire mtundu wotere wa anthu?’ ”

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 9:9
12 Mawu Ofanana  

Chifukwa chake Ambuye ati, Yehova wa makamu wamphamvu wa Israele, Ha! Ndidzatonthoza mtima wanga pochotsa ondivuta, ndi kubwezera chilango adani anga;


Ndipo mudzachita chiyani tsiku lakudza woyang'anira, ndi chipasuko chochokera kutali? Mudzathawira kwa yani kufuna kuthangatidwa? Mudzasiya kuti ulemerero wanu?


Pakuti pa miyala yosalala ya m'chigwa pali gawo lako; iyo ndiyo gawo lako; ndiyo imene unaitsanulirira nsembe yothira, ndi kupereka nsembe yaufa. Kodi ndidzapembedzedwa pa zinthu zimenezi?


Apayesa bwinja; pandilirira ine, pokhala bwinja; dziko lonse lasanduka bwinja; chifukwa palibe munthu wosamalira.


Dziko lidzalira masiku angati, nilifota therere la minda yonse? Chifukwa cha zoipa za iwo okhalamo, zithedwa zinyama, ndi mbalame; pakuti iwo anati, Iye sadzaona chitsiriziro chathu.


Ndinaona, ndipo taona, panalibe munthu, ndi mbalame zonse zakumwamba zinathawa.


Sindidzawalanga kodi chifukwa cha zimenezi? Ati Yehova; kodi moyo wanga sudzabwezera chilango mtundu wotere?


Kodi sindidzawalanga chifukwa cha zimenezi? Ati Yehova; kodi moyo wanga sudzabwezera chilango mtundu woterewu?


Chifukwa chake dziko lidzachita chisoni, ndi aliyense wokhalamo adzalefuka, pamodzi ndi nyama zakuthengo, ndi mbalame za m'mlengalenga; ndi nsomba za m'nyanja zomwe zidzachotsedwa.


Ndifuulira kwa Inu Yehova, pakuti moto wapsereza mabusa a m'chipululu, ndi malawi a moto anatentha mitengo yonse yakuthengo.


Tamverani mau awa ndinenawa, akhalire inu nyimbo ya maliro, nyumba ya Israele inu.


Namwali wa Israele wagwa, sadzaukanso; wagwetsedwa pa nthaka yake, palibe womuutsa.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa