Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Yeremiya 9:10 - Buku Lopatulika

10 Chifukwa cha mapiri ndidzagwa misozi ndi kulira, chifukwa cha mabusa a chipululu ndidzachita maliro, chifukwa apserera, kuti anthu sangathe kupitirirapo; ndiponso anthu sangathe kumva mau a ng'ombe zao; mbalame za mlengalenga ndi nyama zathawa, zapita.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

10 Chifukwa cha mapiri ndidzagwa misozi ndi kulira, chifukwa cha mabusa a chipululu ndidzachita maliro, chifukwa apserera, kuti anthu sangathe kupitirirapo; ndiponso anthu sangathe kumva mau a ng'ombe zao; mbalame za mlengalenga ndi nyama zathawa, zapita.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

10 Ine ndidati, “Ndidzamva chisoni ndi kulira mokweza chifukwa cha mapiri. Ndidzadandaula chifukwa cha mabusa am'chipululu popeza kuti malo onsewo aonongeka. Palibe amene amapitako, sikumveka nkulira kwa ng'ombe komwe. Mbalame zonse zouluka ndiponso nyama zakuthengo zathaŵa, osaonekanso.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

10 Ndidzakhetsa misozi ndi kulira kwamphamvu chifukwa cha mapiri ndipo ndidzadandaula chifukwa cha msipu wa ku chipululu. Malo onsewo awonongeka ndipo palibe amene amapitako, ndipo sikumveka kulira kwa ngʼombe. Mbalame zamlengalenga zathawa ndipo nyama zakuthengo zachokako.

Onani mutuwo Koperani




Yeremiya 9:10
30 Mawu Ofanana  

Taona, ndidzakuyesa iwe choombera tirigu chatsopano chakuthwa chokhala ndi mano; iwe udzaomba mapiri ndi kuwapera asalale, ndi kusandutsa zitunda mungu.


Pakuti, kunena za malo ako osiyidwa ndi abwinja ndi dziko lako limene lapasulidwa tsopano, ndithu iwe udzakhala wochepera okhalamo, ndi iwo amene anakumeza iwe adzakhala kutali.


Abusa ambiri aononga munda wanga wampesa, apondereza gawo langa, pondikondweretsa apayesa chipululu chopanda kanthu.


Apayesa bwinja; pandilirira ine, pokhala bwinja; dziko lonse lasanduka bwinja; chifukwa palibe munthu wosamalira.


Dziko lidzalira masiku angati, nilifota therere la minda yonse? Chifukwa cha zoipa za iwo okhalamo, zithedwa zinyama, ndi mbalame; pakuti iwo anati, Iye sadzaona chitsiriziro chathu.


Mbidzi zinaima pamapiri oti see, zipumira mphepo wefuwefu ngati ankhandwe; maso ao alema, chifukwa palibe udzu.


Ana a mikango anambangulira iye, nakweza mau; anapasula dziko lake, mizinda yake yatenthedwa, mulibenso wokhalamo.


Osati Ali kuti Yehova amene anatikweza kuchokera kudziko la Ejipito, natitsogolera m'chipululu, m'dziko loti see ndi la maenje, m'dziko la chilala ndi la mthunzi wa imfa, m'dziko losapitanso anthu, losamangamo anthu?


Pakuti dziko ladzala ndi achigololo; pakuti chifukwa cha temberero dziko lirira, mabusa a kuchipululu auma; kuyenda kwao kuli koipa, ndi mphamvu yao siili yabwino.


Pakuti mtundu wa anthu udzatuluka kumpoto kudzamenyana naye, udzachititsa dziko lake bwinja, losakhalamo anthu; athawa, apita, anthu ndi nyama.


Meta tsitsi lako, iwe Yerusalemu, nulitaye, nukweze maliro pa mapiri oti see; pakuti Yehova wakana ndi kusiya mbadwo umene aukwiyira.


Ha, ndikadatonthoza mtima wanga kuletsa chisoni chake? Mtima wanga walefuka m'kati mwa ine.


Chifukwa cha zimenezi ndilira; diso langa, diso langatu likudza madzi: Pakuti wonditonthoza, wotsitsimutsa moyo wanga, anditalikira; ana anga asungulumwa, pakuti adaniwo apambana.


Maso anga alefuka ndi misozi, m'kati mwanga mugwedezeka; chiwindi changa chagwa pansi chifukwa cha kupasuka kwa mwana wamkazi wa anthu a mtundu wanga; chifukwa tiana ndi oyamwa akomoka m'makwalala a mzindawu.


paphiri la Ziyoni lopasukalo ankhandwe ayendapo.


Ndikapititsa zilombo zoipa pakati padziko, ndi kupulula ana, kuti likhale lachipululu losapitako munthu chifukwa cha zilombo,


Ndipo iwe wobadwa ndi munthu, Takwezera Tiro nyimbo ya maliro;


Silidzapitamo phazi la munthu, kapena phazi la nyama losapitamo, losakhalamo anthu zaka makumi anai.


Ndipo ndidzasanduliza dziko likhale lachipululu ndi lodabwitsa, ndi mphamvu yake yodzikuza idzatha, ndi mapiri a Israele adzakhala achipululu, osapitako munthu.


Pokhala inu ponse mizinda idzapasuka, ndi misanje idzakhala yabwinja; kuti maguwa anu a nsembe akhale opasuka ndi mabwinja, ndi mafano anu asweke nalekeke, ndi zoimiritsa zanu zadzuwa zilikhidwe, ndi ntchito zanu zifafanizidwe.


Chifukwa chake dziko lidzachita chisoni, ndi aliyense wokhalamo adzalefuka, pamodzi ndi nyama zakuthengo, ndi mbalame za m'mlengalenga; ndi nsomba za m'nyanja zomwe zidzachotsedwa.


Mudzimangire chiguduli m'chuuno mwanu, nimulire, ansembe inu; bumani otumikira kuguwa la nsembe inu; lowani, gonani usiku wonse m'chiguduli, inu otumikira Mulungu wanga; pakuti nsembe yaufa ndi nsembe yothira zaletsedwera nyumba ya Mulungu wanu.


Ndifuulira kwa Inu Yehova, pakuti moto wapsereza mabusa a m'chipululu, ndi malawi a moto anatentha mitengo yonse yakuthengo.


Tamverani mau awa ndinenawa, akhalire inu nyimbo ya maliro, nyumba ya Israele inu.


Chifukwa chake atero Yehova, Mulungu wa makamu, Ambuye, M'makwalala onse mudzakhala kulira, ndi m'miseu yonse adzati, Kalanga ine! Kalanga ine! Nadzaitana wakumunda adze kumaliro, ndi odziwa maliridwe a nthetemya alire.


Tsiku ilo adzanena fanizo lakunena inu, nadzalira maliro olemerera, ndi kuti, Tapasuka konse; iye asintha gawo la anthu anga; ha! Andichotsera ili! Agawira opikisana minda yathu.


Momwemo Ziyoni adzalimidwa ngati munda chifukwa cha inu, ndi mu Yerusalemu mudzasanduka miunda, ndi phiri la nyumba ngati misanje ya m'nkhalango.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa