Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Masalimo 55:21 - Buku Lopatulika

21 Pakamwa pake mposalala ngati mafuta amkaka, koma mumtima mwake munali nkhondo, mau ake ngofewa ngati mafuta oyenga, koma anali malupanga osololasolola.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

21 Pakamwa pake mposalala ngati mafuta amkaka, koma mumtima mwake munali nkhondo, mau ake ngofewa ngati mafuta oyenga, koma anali malupanga osololasolola.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

21 Mau ake anali osalala kupambana batala, komabe mumtima mwake munali zankhondo. Mau ake anali ofeŵa kupambana mafuta, komabe anali ndi malupanga osololasolola.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

21 Mawu ake ndi osalala kuposa batala komabe nkhondo ili mu mtima mwake; mawu ake ndi osalala kwambiri kuposa mafuta, komatu mawuwo ndi malupanga osololoka.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 55:21
16 Mawu Ofanana  

Ndiponso ndidzatumikira yani? Si pamaso pa mwana wake nanga? Monga ndinatumikira pamaso pa atate wanu, momwemo ndidzakhala pamaso panu.


Kodi idzachulukitsa mau akukupembedza? Kapena idzanena nawe mau ofatsa?


Amanena za bodza munthu yense ndi mnansi wake, amanena ndi mlomo wothyasika, ndi mitima iwiri.


Musandikoke kundichotsa pamodzi ndi oipa, ndi ochita zopanda pake; amene alankhula zamtendere ndi anansi ao, koma mumtima mwao muli choipa.


Moyo wanga uli pakati pa mikango; ndigona pakati pa oyaka moto, ndiwo ana a anthu amene mano ao ali nthungo ndi mivi, ndipo lilime lao ndilo lupanga lakuthwa.


Onani abwetuka pakamwa pao; m'milomo mwao muli lupanga, pakuti amati, Amva ndani?


Komatu amkhalira upo kuti amkankhire pansi ulemu wake; akondwera nao mabodza; adalitsa ndi m'kamwa mwao, koma atemberera mumtima.


Amene anola lilime lao ngati lupanga, napiringidza mivi yao, ndiyo mau akuwawitsa;


Alipo wonena mwansontho ngati kupyoza kwa lupanga; koma lilime la anzeru lilamitsa.


Lilime lonama lida omwewo linawasautsa; ndipo m'kamwa mosyasyalika mungoononga.


Ndipo Yudasi, womperekayo anayankha nati, Kodi ndine, Rabi? Iye ananena kwa iye, Iwe watero.


Ndipo pokhala pamgonero, mdierekezi adatha kuika mu mtima wake wa Yudasi mwana wa Simoni Iskariote, kuti akampereke Iye,


Ndipo Saulo analamulira anyamata ake, nati, Mulankhule naye Davide m'tseri, ndi kuti, Taonani mfumu akondwera nanu, ndi anyamata ake onse akukondani; chifukwa chake tsono, khalani mkamwini wa mfumu.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa