Yuda 1:4 - Buku Lopatulika4 Pakuti pali anthu ena anakwawira m'tseri, ndiwo amene aja adalembedwa maina ao kale, kukalandira chitsutso ichi, anthu osapembedza, akusandutsa chisomo cha Mulungu wathu chikhale chilakolako chonyansa, nakaniza Mfumu wayekha, ndi Ambuye wathu, Yesu Khristu. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20144 Pakuti pali anthu ena anakwawira m'tseri, ndiwo amene aja adalembedwa maina ao kale, kukalandira chitsutso ichi, anthu osapembedza, akusandutsa chisomo cha Mulungu wathu chikhale chilakolako chonyansa, nakaniza Mfumu wayekha, ndi Ambuye wathu, Yesu Khristu. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa4 Paja anthu ena osasamala za Mulungu adaloŵa mobisika pakati panu. Iwo amapotoza kukoma mtima kwa Mulungu, ndi kukuyesa ufulu wochitira zonyansa. Amakana Yesu Khristu, amene Iye yekha ndiye Mbuye wathu ndi Mfumu yathu. Zakuti anthu ameneŵa adzalangidwa zidalembedwa kale lomwe. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero4 Pakuti anthu ena amene za chilango chawo zinalembedwa kale, alowa mobisika pakati panu. Amenewa ndi anthu osapembedza Mulungu, amene amapotoza chisomo cha Mulungu wathu kuchisandutsa ufulu ochitira zonyansa ndiponso amakana Yesu Khristu amene Iye ndiye Mbuye ndi Mfumu yathu. Onani mutuwo |