Marko 7:6 - Buku Lopatulika6 Ndipo Iye ananena nao, Yesaya ananenera bwino za inu onyenga, monga mwalembedwa, Anthu awa andilemekeza Ine ndi milomo yao, koma mtima wao ukhala kutali ndi Ine. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20146 Ndipo Iye ananena nao, Yesaya ananenera bwino za inu onyenga, monga mwalembedwa, Anthu awa andilemekeza Ine ndi milomo yao, koma mtima wao ukhala kutali ndi Ine. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa6 Yesu adaŵayankha kuti, “Inu anthu achiphamaso, ndithu mneneri Yesaya adaanenadi zoona muja adaalemba kuti, “ ‘Anthu aŵa amangondilemekeza ndi pakamwa chabe, koma mtima wao uli kutalitali ndi Ine. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero6 Iye anayankha kuti, “Yesaya ananena zoona pamene ananenera za inu achiphamaso; monga kunalembedwa kuti: “Anthu awa amandilemekeza Ine ndi milomo yawo, koma mitima yawo ili kutali ndi Ine. Onani mutuwo |