Biblia Todo Logo
Mavesi a Baibulo
- Zotsatsa -


110 Mau a M'Baibulo Okhudza Kunena Zoipa Mulungu

110 Mau a M'Baibulo Okhudza Kunena Zoipa Mulungu

Nkhani ya kunyoza Mulungu yatchulidwa kambirimbiri m’Baibulo. Kuchitira mwano kapena kunyoza dzina la Mulungu si nkhani yopepuka m’Malemba. Mwachitsanzo, m’buku la Ekisodo 20:7, Mulungu anati, “Usatchule dzina la Yehova Mulungu wako pachabe; pakuti Yehova sadzam’leka wopanda mlandu iye amene atchula dzina lake pachabe.”

Kunyoza Mulungu kumakhudza kuyera kwake ndipo kumasonyeza kusalemekeza dzina lake. Yesu nayenso anatiphunzitsa kufunika kosamala mawu athu, poti “mawu onse achabechabe amene anthu amalankhula, adzawawerengera mlandu tsiku lachiweruzo” (Mateyu 12:36). Choncho, tiyenera kusamala kwambiri mawu athu ndikupewa mitundu yonse ya kunyoza Mulungu.

Kunyoza Mulungu n’kochititsa manyazi kwa Mulungu woyera ndipo tiyenera kupewa ngati tikufuna kukhala moyo wotsatira mfundo za m’Baibulo. Ndikukhulupirira kuti zimenezi zikukulimbikitsa kusamala mawu ako ndikufuna chisomo cha Mulungu pa chilichonse chimene umanena. Baibulo limati machimo onse adzakhululukidwa koma wonyoza Mzimu Woyera sadzakhululukidwa. Choncho usakayikire ntchito ya Mzimu Woyera chifukwa si udindo wathu kuweruza mitima ya anthu. Yesu ndiye woweruza yekha. Ndikukupempha kuti usamalire moyo wako kuti usatayike.

Tiyeni tonse tizisamala mawu athu ndikulemekeza Mulungu pa chilichonse chimene timachita kapena kunena.




Mateyu 12:31

Chifukwa chake ndinena kwa inu, Machimo onse, ndi zonena zonse zamwano, zidzakhululukidwa kwa anthu; koma chamwano cha pa Mzimu Woyera sichidzakhululukidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 13:6

Ndipo chinatsegula pakamwa pake kukanena zamwano pa Mulungu, kuchitira mwano dzina lake, ndi chihema chake, ndi iwo akukhala mu Mwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 24:16

Ndi iye wakuchitira mwano dzina la Yehova, amuphe ndithu; khamu lonse limponye miyala ndithu; mlendo ndi wobadwa m'dziko yemwe akachitira dzina la Yehova mwano, awaphe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 12:31-32

Chifukwa chake ndinena kwa inu, Machimo onse, ndi zonena zonse zamwano, zidzakhululukidwa kwa anthu; koma chamwano cha pa Mzimu Woyera sichidzakhululukidwa. Ndipo aliyense amene anganenere Mwana wa Munthu zoipa, adzakhululukidwa; koma aliyense amene anganenere Mzimu Woyera zoipa sadzakhululukidwa nthawi ino kapena ilinkudzayo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 13:1

Ndipo ndinaimirira pa mchenga wa nyanja. Ndipo ndinaona chilombo chilinkutuluka m'nyanja, chakukhala nazo nyanga khumi, ndi mitu isanu ndi iwiri, ndi pa nyanga zake nduwira zachifumu khumi, ndi pamitu pake maina a mwano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 17:3

Ndipo ananditenga kunka nane kuchipululu, mu Mzimu; ndipo ndinaona mkazi alinkukhala pachilombo chofiira, chodzala ndi maina a mwano, chakukhala nayo mitu isanu ndi iwiri ndi nyanga khumi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 20:7

Usatchule dzina la Yehova Mulungu wako pachabe; chifukwa Yehova sadzamuyesa iye wosachimwa, amene atchula pachabe dzina lakelo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 20:27

Chifukwa chake wobadwa ndi munthu iwe, lankhula ndi nyumba ya Israele, nunene nao, Atero Ambuye Yehova, Mwa ichinso atate anu anandichitira mwano pakundilakwira Ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 3:28-29

Indetu, ndinena ndi inu, Adzakhululukidwa machimo onse a ana a anthu, ndi zamwano zilizonse adzachita mwano nazo; koma aliyense adzachitira Mzimu Woyera mwano alibe kukhululukidwa nthawi yonse, koma anapalamuladi tchimo losatha;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Danieli 3:29

Chifukwa chake ndilamulira kuti anthu ali onse, mtundu uliwonse, ndi a manenedwe ali onse, akunenera molakwira Mulungu wa Sadrake, Mesaki, ndi Abedenego, adzadulidwa nthulinthuli, ndi nyumba zao zidzasanduka dzala; popeza palibe mulungu wina akhoza kulanditsa motero.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 19:12

Musamalumbira monama ndi kutchula dzina langa, ungaipse dzina la Mulungu wako; Ine ndine Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Akolose 3:8

Koma tsopano tayani inunso zonsezi: mkwiyo, kupsa mtima, dumbo, mwano, zonyansa zotuluka m'kamwa mwanu:

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 18:6

Koma pamene iwo, anamkana, nachita mwano, anakutumula malaya ake, nati kwa iwo, Mwazi wanu ukhale pa mitu yanu; ine ndilibe kanthu; kuyambira tsopano ndinka kwa amitundu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 19:37

Pakuti mwatenga anthu awa, osakhala olanda za mu Kachisi, kapena ochitira mulungu wathu mwano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 22:28

Usapeputsa oweruza, kapena kutemberera mkulu wa anthu a mtundu wako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 2:24

Pakuti dzina la Mulungu lichitidwa mwano chifukwa cha inu, pakati pa anthu a mitundu, monga mwalembedwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 52:5

Chifukwa chake kodi ndichitenji pano? Ati Yehova; popeza anthu anga achotsedwa popanda kanthu? Akuwalamulira awaliritsa, ati Yehova; ndipo dzina langa lichitidwa mwano tsiku lonse kosalekeza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yakobo 2:7

Kodi sachitira mwano iwowa dzina lokomali muitanidwa nalo?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Petro 2:12

Koma awo, ngati zamoyo zopanda nzeru, nyama zobadwa kuti zikodwe ndi kuonongedwa, akuchitira mwano pa zinthu osazidziwa, adzaonongeka m'kuononga kwao,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 13:5

Ndipo anachipatsa icho m'kamwa molankhula zazikulu ndi zamwano; ndipo anachipatsa ulamuliro wa kutero miyezi makumi anai ndi iwiri.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 16:9

Ndipo anatenthedwa anthu ndi kutentha kwakukulu; ndipo anachitira mwano dzina la Mulungu wokhala nao ulamuliro pa miliri iyi; ndipo sanalape kuti amchitire ulemu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mafumu 19:6

Nanena nao Yesaya, Muzitero kwa mbuye wanu, Atero Yehova, Musamaopa mau mudawamva, amene anyamata a mfumu ya Asiriya anandichitira nao mwano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 5:11

Usatchule dzina la Yehova Mulungu wako pachabe; chifukwa Yehova sadzamuyesa iye wosachimwa amene atchula pachabe dzina lakelo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 16:11

nachitira mwano Mulungu wa mu Mwamba chifukwa cha zowawa zao ndi zilonda zao; ndipo sanalape ntchito zao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 3:28

Indetu, ndinena ndi inu, Adzakhululukidwa machimo onse a ana a anthu, ndi zamwano zilizonse adzachita mwano nazo;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 23:13

Ndipo samalirani zonse ndanena ndi inu; nimusatchule dzina la milungu ina; lisamveke pakamwa pako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 6:11

Pamenepo anafuna anthu akumpitira pansi, ndi kuti, Tidamumva iye alikunenera Mose ndi Mulungu mau amwano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 12:32

Ndipo aliyense amene anganenere Mwana wa Munthu zoipa, adzakhululukidwa; koma aliyense amene anganenere Mzimu Woyera zoipa sadzakhululukidwa nthawi ino kapena ilinkudzayo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Luka 12:10

Ndipo aliyense amene adzanenera Mwana wa Munthu zoipa adzakhululukidwa; koma amene anenera Mzimu Woyera zamwano sadzakhululukidwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 21:10

ndipo muike anthu awiri, anthu oipa, pamaso pake, kuti amchitire umboni, ndi kuti, Watemberera Mulungu ndi mfumu; nimumtulutse ndi kumponya miyala kumupha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 37:6

Ndipo Yesaya anati kwa iwo, Mukati kwa mbuyanu, Atero Yehova, musaope mau amene wawamva iwe, amene atumiki a mfumu ya Asiriya andilalatira Ine.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 3:29

koma aliyense adzachitira Mzimu Woyera mwano alibe kukhululukidwa nthawi yonse, koma anapalamuladi tchimo losatha;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 26:11

Ndipo ndinawalanga kawirikawiri m'masunagoge onse, ndi kuwakakamiza anene zamwano; ndipo pakupsa mtima kwakukulu pa iwo ndinawalondalonda ndi kuwatsata ngakhale kufikira kumizinda yakunja.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 26:65

Pomwepo mkulu wa ansembe anang'amba zovala zake, nati, Achitira Mulungu mwano; tifuniranji mboni zina? Onani, tsopano mwamva mwanowo;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 1:13

ndingakhale kale ndinali wamwano, ndi wolondalonda, ndi wachipongwe; komatu anandichitira chifundo, popeza ndinazichita wosazindikira, wosakhulupirira;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 74:18

Mukumbukire ichi, Yehova, mdaniyo anatonza, ndipo anthu opusa ananyoza dzina lanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 139:20

Popeza anena za Inu moipa, ndi adani anu atchula dzina lanu mwachabe.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 3:8

Ndipo tilekerenji kunena, Tichite zoipa kuti zabwino zikadze (monganso ena atinamiza ndi kuti timanena)? Kulanga kwa amenewo kuli kolungama.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 6:1

Onse amene ali akapolo a m'goli, ayesere ambuye a iwo okha oyenera ulemu wonse, kuti dzina la Mulungu ndi chiphunzitso zisachitidwe mwano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 3:2

Pakuti anthu adzakhala odzikonda okha, okonda ndalama, odzitamandira, odzikuza, amwano, osamvera akuwabala, osayamika,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 21:6

Azikhala opatulikira Mulungu wao, osaipsa dzina la Mulungu wao; popeza amapereka nsembe zamoto za Yehova, mkate wa Mulungu wao; chifukwa chake akhale opatulika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 74:10

Wotsutsanayo adzatonza kufikira liti, Mulungu? Kodi mdani adzanyoza dzina lanu nthawi yonse?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 9:3

Ndipo onani, ena a alembi ananena mumtima mwao, Uyu achitira Mulungu mwano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 13:45

Koma Ayuda, pakuona makamu a anthu, anadukidwa, natsutsana nazo zolankhulidwa ndi Paulo, nachita mwano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 74:23

Musaiwale mau a iwo otsutsana ndi Inu; kusokosera kwa iwo akuukirani Inu kumakwera kosaleka.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 65:7

zoipa zanuzanu pamodzi ndi zoipa za makolo anu, ati Yehova, amene anafukiza zonunkhira pamapiri, nandichitira mwano pazitunda; chifukwa chake Ine ndidzayesa ntchito yao yakale ilowe pa chifuwa chao.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Timoteyo 1:20

a iwo ali Himeneo ndi Aleksandro, amene ndawapereka kwa Satana, kuti aphunzire kusalankhula zamwano.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 27:39

Ndipo anthu akupitirirapo anamchitira mwano Iye ndi kupukusa mitu yao,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 10:3

Pakuti woipa adzitamira chifuniro cha moyo wake, adalitsa wosirira, koma anyoza Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 73:9

Pakamwa pao anena zam'mwamba, ndipo lilime lao liyendayenda m'dziko lapansi.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Petro 2:10

koma makamaka iwo akutsata za thupi, m'chilakolako cha zodetsa, napeputsa chilamuliro; osaopa kanthu, otsata chifuniro cha iwo eni, santhunthumira kuchitira mwano akulu aulemerero;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Mafumu 21:13

Ndipo anthu aja awiri oipawo analowa, nakhala pamaso pake, ndipo anthu oipawo anamchitira umboni wonama Nabotiyo, pamaso pa anthu onse, nati, Naboti anatemberera Mulungu ndi mfumu. Pamenepo anamtulutsa m'mzinda, namponya miyala, namupha.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 15:19

Pakuti mumtima muchokera maganizo oipa, zakupha, zachigololo, zachiwerewere, zakuba, za umboni wonama, zamwano;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 43:27-28

Atate wako woyamba anachimwa, ndi otanthauzira ako andilakwira Ine. Chifukwa chake ndidzaipitsa akulu a Kachisi, ndipo ndidzasanduliza Yakobo akhale temberero, ndi Israele akhale chitonzo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 44:16

Chifukwa cha mau a wotonza wochitira mwano; chifukwa cha mdani ndi wobwezera chilango.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 35:12

Ndipo udzadziwa kuti Ine Yehova ndidamva zamwano zako zonse udazinena pa mapiri a Israele, ndi kuti, Apasuka, apatsidwa kwa ife tiwadye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 107:11

popeza anapikisana nao mau a Mulungu, napeputsa uphungu wa Wam'mwambamwamba;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 13:5-6

Ndipo anachipatsa icho m'kamwa molankhula zazikulu ndi zamwano; ndipo anachipatsa ulamuliro wa kutero miyezi makumi anai ndi iwiri. Ndipo chinatsegula pakamwa pake kukanena zamwano pa Mulungu, kuchitira mwano dzina lake, ndi chihema chake, ndi iwo akukhala mu Mwamba.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yuda 1:15

kudzachitira onse chiweruziro, ndi kutsutsa osapembedza onse, pa ntchito zao zonse zosapembedza, ndi pa zolimba zimene ochimwa osapembedza adalankhula pa Iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 23:16

Yehova wa makamu atero, Musamvere mau a aneneri amene anenera kwa inu; akuphunzitsani zachabe; anena masomphenya a mtima wao, si a m'kamwa mwa Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 36:20

Mwa milungu yonse ya maiko awa, inapulumutsa dziko lao m'manja mwanga ndi iti, kuti Yehova adzapulumutsa Yerusalemu m'manja mwanga?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 1:30

akazitape, osinjirira, akumuda Mulungu, achipongwe, odzitama, amatukutuku, oyamba zoipa, osamvera akulu ao,

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 5:11

M'mwemo, Pali Ine, ati Ambuye Yehova, popeza wadetsa malo anga opatulika ndi zonyansa zako zonse ndi zoipsa zako zonse, ndidzakuchepsa; diso langa silidzalekerera, ndi Inenso sindidzachita chifundo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Levitiko 18:21

Ndipo usamapereka a mbumba yako kuwapitiriza kumoto chifukwa cha Moleki; usamaipsa dzina la Mulungu wako; Ine ndine Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Numeri 15:30

Koma munthu wakuchita kanthu dala, ngakhale wobadwa m'dziko kapena mlendo, yemweyo achitira Yehova mwano; ndipo munthuyo amsadze pakati pa anthu a mtundu wake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mafumu 19:22

Ndiye yani wamtonza ndi kumchitira mwano? Ndiye yani wamkwezera mau ndi kumgadamira maso ako m'mwamba? Ndiye Woyerayo wa Israele.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yobu 15:13

Kuti utembenuza mzimu wako utsutsane ndi Mulungu, ndi kulola mau otere atuluke m'kamwa mwako.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 26:74-75

Pamenepo iye anayamba kutemberera ndi kulumbira, kuti, Sindidziwa munthuyo. Ndipo pompo tambala analira. Ndipo Petro anakumbukira mau amene Yesu adati, Asanalire tambala udzandikana katatu. Ndipo anatulukira kunja, nalira ndi kuwawa mtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 57:4

Ndiye yani mudzikondweretsa momseka? Ndani mulikumyasamira kukamwa, ndi kumtulutsira lilime? Kodi inu simuli ana akulakwa, mbeu yonama?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Samueli 12:14

Koma popeza pakuchita ichi munapatsa chifukwa chachikulu kwa adani a Yehova cha kuchitira mwano, mwanayonso wobadwira inu adzafa ndithu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 5:34-37

koma Ine ndinena kwa inu, Musalumbire konse, kapena kutchula Kumwamba, chifukwa kuli chimpando cha Mulungu; kapena kutchula dziko lapansi, chifukwa lili popondapo mapazi ake; kapena kutchula Yerusalemu, chifukwa kuli mzinda wa Mfumu yaikulukulu. Kapena usalumbire kumutu wako, chifukwa sungathe kuliyeretsa mbuu kapena kulidetsa bii tsitsi limodzi. Koma manenedwe anu akhale, Inde, inde; Iai, iai; ndipo choonjezedwa pa izo chichokera kwa woipayo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 36:20

Ndipo pofika iwo kwa amitundu kumene anamukako, anadetsa dzina langa loyera; popeza anthu ananena za iwowa, Awa ndi anthu a Yehova, natuluka m'dziko mwake.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 7:30

Pakuti ana a Yuda anachita choipa pamaso panga, ati Yehova; naika zonyansa zao m'nyumba yotchedwa dzina langa, kuti aliipitse.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Marko 7:22

zakuba, zakupha, zachigololo, masiriro, zoipa, chinyengo, chinyanso, diso loipa, mwano, kudzikuza, kupusa:

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 89:51-52

Chimene adani anu, Yehova, atonza nacho; chimene atonzera nacho mayendedwe a wodzozedwa wanu. Wodalitsika Yehova kunthawi yonse. Amen ndi Amen.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 65:3

anthu amene andiputa Ine kumaso kwanga nthawi zonse, apereka nsembe m'minda, nafukizira zonunkhira panjerwa;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Atesalonika 2:4

amene atsutsana nazo, nadzikuza pa zonse zotchedwa Mulungu, kapena zopembedzeka; kotero kuti iye wakhala pansi ku Kachisi wa Mulungu, nadzionetsera yekha kuti ali Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 50:16-17

Koma kwa woipa Mulungu anena, Uli nao chiyani malemba anga kulalikira, ndi kutchula pangano langa pakamwa pako? Popeza udana nacho chilangizo, nufulatira mau anga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 23:11

Pakuti mneneri ndi wansembe onse awiri adetsedwa; inde, m'nyumba yanga ndapeza zoipa zao, ati Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 5:24

Chifukwa chake monga ngati lilime la moto likutha chiputu, ndi monga udzu wouma ugwa pansi m'malawi, momwemo muzu wao udzakhala monga wovunda, maluwa ao adzauluka m'mwamba ngati fumbi; chifukwa kuti iwo akana chilamulo cha Yehova wa makamu, nanyoza mau a Woyera wa Israele.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 10:33

Ayuda anamyankha Iye, Chifukwa cha ntchito yabwino sitikuponyani miyala, koma chifukwa cha mwano; ndi kuti Inu, muli munthu, mudziyesera nokha Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Mbiri 32:17

Analemberanso makalata a kunyoza Yehova Mulungu wa Israele, ndi kunena motsutsana ndi Iye, ndi kuti, Monga milungu ya mitundu ya anthu a m'maiko, imene siinalanditse anthu ao m'dzanja langa, momwemo Mulungu wa Hezekiya sadzalanditsa anthu ake m'dzanja mwanga.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 10:15

Kodi nkhwangwa idzadzikweza yokha, pa iye amene adula nayo? Kodi chochekera chidzadzikweza chokha pa iye amene achigwedeza, ngati chibonga ingamgwedeze iye amene ainyamula, ngati ndodo inganyamule kanthu popeza ili mtengo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 66:3

Wakupha ng'ombe alingana ndi wakupha munthu; iye wapereka nsembe ya mwanawankhosa alingana ndi wothyola khosi la galu; wothira nsembe yaufa akunga wothira mwazi wa nkhumba; wofukiza lubani akunga wodalitsa fano; inde iwo asankha njira zaozao, ndipo moyo wao ukondwerera m'zonyansa zao;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 31:18

Ikhale yosalankhula milomo ya mabodza, imene imalankhula mwachipongwe pa olungama mtima, ndi kudzikuza ndi kunyoza.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 8:12

Kodi anakhala ndi manyazi pamene anachita zonyansa? Iai, sanakhale ndi manyazi, sananyale; chifukwa chake adzagwa mwa iwo amene akugwa, nthawi ya kuyang'aniridwa kwao adzagwetsedwa, ati Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 2:23-24

Iwe wakudzitamandira pachilamulo, kodi uchitira Mulungu mwano ndi kulakwa kwako m'chilamulo? Pakuti dzina la Mulungu lichitidwa mwano chifukwa cha inu, pakati pa anthu a mitundu, monga mwalembedwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 57:6

Pakuti pa miyala yosalala ya m'chigwa pali gawo lako; iyo ndiyo gawo lako; ndiyo imene unaitsanulirira nsembe yothira, ndi kupereka nsembe yaufa. Kodi ndidzapembedzedwa pa zinthu zimenezi?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Chivumbulutso 2:9

Ndidziwa chisautso chako, ndi umphawi wako (komatu uli wachuma), ndi mwano wa iwo akunena za iwo okha kuti ali Ayuda, osakhala Ayuda, komatu sunagoge wa Satana.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Petro 4:14

Mukatonzedwa pa dzina la Khristu, odala inu; pakuti Mzimu wa ulemerero, ndi Mzimu wa Mulungu apuma pa inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
2 Timoteyo 3:5

akukhala nao maonekedwe a chipembedzo, koma mphamvu yake adaikana; kwa iwonso udzipatule.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 7:51

Ouma khosi ndi osadulidwa mtima ndi makutu inu, mukaniza Mzimu Woyera nthawi zonse; monga anachita makolo anu, momwemo inu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Deuteronomo 18:20-22

Koma mneneri wakuchita modzikuza ndi kunena mau m'dzina langa, amene sindinamlamulire anene, kapena kunena m'dzina la milungu ina, mneneri ameneyo afe. Ndipo mukati m'mtima mwanu, Tidzazindikira bwanji mau amene Yehova sananene? Mneneri akanena m'dzina la Yehova, koma mau adanenawa sachitika, nisafika, ndiwo mau Yehova sanawanene; mneneriyo ananena modzikuza, musamuope iye.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 23:36

Ndipo katundu wa Yehova simudzatchulanso konse; pakuti mau a munthu adzakhala katundu wake; pakuti mwasokoneza mau a Mulungu wamoyo, Yehova wa makamu, Mulungu wathu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Machitidwe a Atumwi 9:4

ndipo anagwa pansi, namva mau akunena naye, Saulo, Saulo, Undilondalonderanji?

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yesaya 41:29

Taona, iwo onse, ntchito zao zikhala zopanda pake ndi zachabe; mafano ao osungunula ndiwo mphepo ndi masokonezo.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
1 Akorinto 6:10

kapena ambala, kapena osirira, kapena oledzera, kapena olalatira, kapena olanda, sadzalowa Ufumu wa Mulungu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:53

Ndinasumwa kwakukulu, chifukwa cha oipa akusiya chilamulo chanu.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 8:12-13

Pamenepo anati kwa ine, Wobadwa ndi munthu iwe, wapenya kodi chochita akulu a nyumba ya Israele mumdima, aliyense m'chipinda chake cha zifanizo? Pakuti ati, Yehova satipenya, Yehova wataya dziko. Anatinso kwa ine, Udzaonanso zonyansa zazikulu zina azichita.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yeremiya 14:14-15

Ndipo Yehova anati kwa ine, Aneneri anenera zonama m'dzina langa; sindinatume iwo, sindinauze iwo, sindinanene nao; anenera kwa inu masomphenya onama, ndi ula, ndi chinthu chachabe, ndi chinyengo cha mtima wao. Chifukwa chake atero Yehova za aneneri onenera m'dzina langa, ndipo sindinawatume, koma ati, Lupanga ndi chilala sizidzakhala m'dziko muno; ndi lupanga ndi chilala aneneriwo adzathedwa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 44:15

Tsiku lonse chimpepulo changa chikhala pamaso panga, ndipo manyazi a pankhope panga andikuta.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Masalimo 119:139-140

Changu changa chinandithera, popeza akundisautsa anaiwala mau anu. Ndinakondwera m'njira ya mboni zanu, koposa ndi chuma chonse. Mau anu ngoyera ndithu; ndi mtumiki wanu awakonda.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Ezekieli 13:6-9

Iwo aona zopanda pake, ndi phenda labodza amene anena, Atero Yehova; koma Yehova sanawatume, nayembekezetsa anthu kuti mauwo adzakhazikika. Simunaona masomphenya opanda pake kodi? Simunanena ula wabodza kodi? Pakunena inu, Atero Yehova; chinkana sindinanene? Chifukwa chake atero Ambuye Yehova, Popeza mwanena zopanda pake, ndi kuona mabodza, chifukwa chake taonani, ndikhala Ine wotsutsana nanu, ati Ambuye Yehova. Ndi dzanja langa lidzakhala lotsutsana nao aneneri akuona zopanda pake, ndi kupenda za bodza; sadzakhala mu msonkhano wa anthu anga, kapena kulembedwa m'buku lolembedwamo nyumba ya Israele; kapena kulowa m'dziko la Israele; ndipo mudzadziwa kuti Ine ndine Ambuye Yehova.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 12:34

Akubadwa inu a njoka, mungathe bwanji kulankhula zabwino, inu akukhala oipa? Pakuti m'kamwa mungolankhula mwa kusefuka kwake kwa mtima.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Yohane 8:49

Yesu anayankha, Ndilibe chiwanda Ine; koma ndilemekeza Atate wanga, ndipo inu mundipeputsa.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Aroma 12:14

Dalitsani iwo akuzunza inu; dalitsani, musawatemberere.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Mateyu 7:21-23

Si yense wakunena kwa Ine, Ambuye, Ambuye, adzalowa mu Ufumu wa Kumwamba; koma wakuchitayo chifuniro cha Atate wanga wa Kumwamba. Ambiri adzati kwa Ine tsiku lomwelo, Ambuye, Ambuye, kodi sitinanenere mau m'dzina lanu, ndi m'dzina lanunso kutulutsa ziwanda, ndi kuchita m'dzina lanunso zamphamvu zambiri? Ndipo pamenepo ndidzafukulira iwo, Sindinakudziweni inu nthawi zonse; chokani kwa Ine, inu akuchita kusaweruzika.

Mutu    |  Mabaibulo Koperani
Eksodo 34:14

pakuti musalambira mulungu wina; popeza Yehova dzina lake ndiye Wansanje, ali Mulungu wansanje;

Mutu    |  Mabaibulo Koperani

Pemphero kwa Mulungu

Chauta wamphamvuyonse ndi waulemerero, ulemerero ndi ulemu zikhale kwa Inu, ndinu woyenera kulandira kutamandidwa konse, muzunguliridwa ndi ukulu ndi mphamvu, mumakhala kwamuyaya, ndinu woyera ndi wolamulira, ndinu wangwiro ndi wodabwitsa Atate wanga wokondedwa, zikomo chifukwa cha kukoma mtima kwanu kwa ine, zikomo chifukwa chondizungulira ndi chisomo chanu ndi chifundo chanu, ndikukuyamikirani chifukwa chondipatsa moyo, ndikukuyamikirani chifukwa chondiphunzitsa kudzera m'mawu anu amtengo wapatali, mmenemo ndimapeza chitsogozo choyendera molungama pamaso panu, zikomo chifukwa chondichenjeza, kundilanga ndi kundionetsa choonadi chanu. Mawu anu ndi nyali ya mapazi anga ndi kuunika kwa njira yanga, tsiku lililonse ndikufuna kusunga malamulo ndi malangizo anu, ndipatseni chilakolako cha kukhala pamaso panu kuti nthawi zonse ndikhale ndi mtima woyera pamaso panu, Yesu ndikukuyamikirani chifukwa cha Mzimu Woyera, nthawi zonse ndimalandira chitonthozo ndi chikondi chake, sindingathe kunena zoipa za iye, ndaona mphamvu yake m'moyo wanga, ndikupemphani kuti mukhululukire onse amene akukayikira chifuniro chanu, ndipo maso a kuzindikira kwawo atsegulidwe kuti miyoyo yawo ipulumutsidwe ku gehena, ndikhululukireni Ambuye chifukwa cha amene akunena zoipa za mawu anu ndi kunena chilichonse kuti awononge thupi la Khristu, chonde tikhululukireni chifukwa cha kuipa konseku ndi kutipatsa ufulu ndi chipulumutso kwa anthu anu, m'dzina la Yesu, Ameni.
Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa