Machitidwe a Atumwi 26:11 - Buku Lopatulika11 Ndipo ndinawalanga kawirikawiri m'masunagoge onse, ndi kuwakakamiza anene zamwano; ndipo pakupsa mtima kwakukulu pa iwo ndinawalondalonda ndi kuwatsata ngakhale kufikira kumizinda yakunja. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 201411 Ndipo ndinawalanga kawirikawiri m'masunagoge onse, ndi kuwakakamiza anene zamwano; ndipo pakupsa mtima kwakukulu pa iwo ndinawalondalonda ndi kuwatsata ngakhale kufikira kumidzi yakunja. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa11 Kaŵirikaŵiri ndinkaŵalanga m'nyumba zonse zamapemphero, ndi kuyesa kuŵakakamiza kuti amnyoze Yesuyo. Ndinkaŵachitira ukali woopsa, kotero kuti ndinkaŵazunza ngakhale ku mizinda ya ku maiko achilendo.” Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero11 Nthawi zambiri ndinkapita mʼsunagoge iliyonse kuti alangidwe, ndipo ndinayesera kuwakakamiza kuti achitire chipongwe Mulungu. Mu mkwiyo wangawo, ndimapita ngakhale ku mizinda yachilendo kuti ndikawazunze. Onani mutuwo |