Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 27:39 - Buku Lopatulika

39 Ndipo anthu akupitirirapo anamchitira mwano Iye ndi kupukusa mitu yao,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

39 Ndipo anthu akupitirirapo anamchitira mwano Iye ndi kupukusa mitu yao,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

39 Anthu amene ankadutsa pamenepo, ankamunyodola nkumapukusa mitu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

39 Ndipo amene amadutsa anamunenera mawu a chipongwe, akupukusa mitu yawo.

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 27:39
18 Mawu Ofanana  

Mau a Yehova akumnenera iye ndi awa, Namwali mwana wamkazi wa Ziyoni akunyoza, akuseka mwana wamkazi wa Yerusalemu, akupukusira mutu pambuyo pako.


Inenso ndikadanena monga inu, moyo wanu ukadakhala m'malo mwa moyo wanga, ndikadalumikizanitsa mau akutsutsana nanu, ndi kukupukusirani mutu wanga.


Pakuti anamasula nsinga zao, nandizunza; anataya chomangira m'kamwa mwao pamaso panga.


pakuti pakamwa pa woipa ndi pakamwa pa chinyengo pananditsegukira; anandilankhulira ndi m'kamwa mwa bodza.


Ndiwakhaliranso chotonza; pakundiona apukusa mutu.


Ndikhoza kuwerenga mafupa anga onse; iwo ayang'ana nandipenyetsetsa ine.


Chotonza chandiswera mtima, ndipo ndidwala ine; ndipo ndinayembekeza wina wondichitira chifundo, koma palibe; ndinayembekeza onditonthoza mtima, osawapeza.


Kodi muyesa chimenechi chabe, nonsenu opita panjira? Penyani nimuone, kodi chilipo chisoni china ngati changachi amandimvetsa ine, chimene Yehova wandisautsa nacho tsiku la mkwiyo wake waukali?


Pamenepo anapachika pamodzi ndi Iye achifwamba awiri, mmodzi kudzanja lamanja, ndi wina kulamanzere.


Ndipo zambiri zina anamnenera Iye, namchitira mwano.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa