Chivumbulutso 17:3 - Buku Lopatulika3 Ndipo ananditenga kunka nane kuchipululu, mu Mzimu; ndipo ndinaona mkazi alinkukhala pachilombo chofiira, chodzala ndi maina a mwano, chakukhala nayo mitu isanu ndi iwiri ndi nyanga khumi. Onani mutuwoChichewa Buku Lopatulika Bible 20143 Ndipo ananditenga kunka nane kuchipululu, mu Mzimu; ndipo ndinaona mkazi alinkukhala pachilombo chofiira, chodzala ndi maina a mwano, chakukhala nayo mitu isanu ndi iwiri ndi nyanga khumi. Onani mutuwoBuku Loyera Catholic Edition - Chichewa3 Tsono mngelo uja adanditenga chamumzimu kupita nane ku chipululu. Kumeneko ndidaona mkazi atakhala pa chilombo chofiira. Pathupi ponse chilombocho chidaalembedwa maina onyozera Mulungu. Chinali ndi mitu isanu ndi iŵiri ndi nyanga khumi. Onani mutuwoMawu a Mulungu mu Chichewa Chalero3 Kenaka mngeloyo anandinyamula mwa Mzimu Woyera kupita nane ku chipululu. Kumeneko ndinaona mkazi atakhala pa chirombo chofiira chokutidwa ndi mayina a chipongwe ndipo chinali ndi mitu isanu ndi iwiri ndi nyanga khumi. Onani mutuwo |
malonda a golide, ndi a siliva, ndi a mwala wa mtengo wake, ndi a ngale, ndi a nsalu yabafuta, ndi a chibakuwa, ndi a yonyezimira, ndi a mlangali; ndi mitengo yonse ya fungo lokoma, ndi chotengera chilichonse cha minyanga ya njovu, ndi chotengera chilichonse chamtengo wa mtengo wake wapatali, ndi chamkuwa ndi chachitsulo, ndi chansangalabwi;