Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Chivumbulutso 16:9 - Buku Lopatulika

9 Ndipo anatenthedwa anthu ndi kutentha kwakukulu; ndipo anachitira mwano dzina la Mulungu wokhala nao ulamuliro pa miliri iyi; ndipo sanalape kuti amchitire ulemu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

9 Ndipo anatenthedwa anthu ndi kutentha kwakukulu; ndipo anachitira mwano dzina la Mulungu wokhala nao ulamuliro pa miliri iyi; ndipo sanalapa kuti amchitire ulemu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

9 Anthu adapserera nako kutentha koopsako, ndipo adayamba kunyoza dzina la Mulungu, amene ali ndi ulamuliro pa miliri imeneyi. Komabe iwo sadatembenuke mtima kuti azitamanda Mulungu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

9 Anapserera nako kutentha kwakukuluko ndipo anatukwana Mulungu, amene anali ndi ulamuliro pa miliri imeneyi, koma anakana kulapa ndi kumulemekeza.

Onani mutuwo Koperani




Chivumbulutso 16:9
20 Mawu Ofanana  

Akali chilankhulire nao, tapenyani, wamtsikira mthengayo; ndi mfumu inati, Taonani, choipa ichi chichokera kwa Yehova; ndilindiranjinso Yehova?


Ndipo nthawi ya nsautso yake anaonjeza kulakwira Yehova, mfumu Ahazi yemweyo.


Nanga bwanji mukali chimenyedwere kuti inu mulikupandukirabe? Mutu wonse ulikudwala, ndi mtima wonse walefuka.


Ndipo iwo adzapitirira ovutidwa ndi anjala, ndipo padzakhala kuti pokhala ndi njala iwo adzadziputa okha, ndi kutemberera mfumu yao, ndi Mulungu wao; ndi kugadamira nkhope zao kumwamba;


Ndipo panali atapita masiku ambiri, kuti Yehova anati kwa ine, Uka, pita ku Yufurate, nukatenge kumeneko mpango uja, ndinakuuza iwe ukaubise kumeneko.


Yehova Inu, maso anu sali pachoonadi kodi? Munawapanda iwo, koma sanaphwetekedwe mtima; munawatha iwo, koma akana kudzudzulidwa; alimbitsa nkhope zao koposa mwala; akana kubwera.


M'chodetsa chako muli dama, popeza ndinakuyeretsa; koma sunayeretsedwa, sudzayeretsedwanso kukuchotsera chodetsa chako, mpaka nditakwaniritsa ukali wanga pa iwe.


Ndinena kwa inu, Iaitu; koma ngati inu simutembenuka mtima, mudzaonongeka nonse momwemo.


Ndinena kwa inu, Iaitu; koma ngati simutembenuka mtima, mudzaonongeka nonse chimodzimodzi.


kuti pakudzanso ine, Mulungu wanga angandichepse pa inu, ndipo ndingalirire ambiri a iwo amene adachimwa kale, osalapa pa chodetsa, ndi chigololo, ndi kukhumba zonyansa zimene anachita.


Ndipo Yoswa anati kwa Akani, Mwana wanga, uchitiretu ulemu Yehova Mulungu wa Israele, numlemekeze Iye; nundiuze tsopano, wachitanji? Usandibisire.


Ndipo panthawipo panali chivomezi chachikulu, ndipo limodzi la magawo khumi a mzinda lidagwa; ndipo anaphedwa m'chivomezicho anthu zikwi zisanu ndi ziwiri; ndipo otsalawo anakhala amantha, napatsa ulemerero kwa Mulungu wa mu Mwamba.


ndi kunena ndi mau aakulu, Opani Mulungu, mpatseni ulemerero; pakuti yafika nthawi ya chiweruziro chake; ndipo mlambireni Iye amene analenga kumwamba ndi dziko lapansi ndi nyanja ndi akasupe amadzi.


Ndipo anatsika kumwamba matalala aakulu, lonse lolemera ngati talente, nagwa pa anthu; ndipo anthu anachitira Mulungu mwano chifukwa cha mliri wa matalala, pakuti mliri wake ndi waukulu ndithu.


Ndipo ndampatsa iye nthawi kuti alape; koma safuna kulapa kusiyana nacho chigololo chake.


Ndipo otsala a anthu osaphedwa nayo miliri iyo sanalape ntchito ya manja ao, kuti asapembedzere ziwanda, ndi mafano agolide, ndi asiliva, ndi amkuwa, ndi a mwala, ndi amtengo, amene sangathe kupenya, kapena kumva, kapena kuyenda;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa