Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 6:11 - Buku Lopatulika

11 Pamenepo anafuna anthu akumpitira pansi, ndi kuti, Tidamumva iye alikunenera Mose ndi Mulungu mau amwano.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

11 Pamenepo anafuna anthu akumpitira pansi, ndi kuti, Tidamumva iye alikunenera Mose ndi Mulungu mau amwano.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

11 Tsono iwo adapangira anthu ena kuti azinena kuti, “Tidamumva akunyoza mwachipongwe Mose ndi Mulungu yemwe.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

11 Iwo ananyengerera anthu ena mwamseri kuti anene kuti, “Ife tinamva Stefano akuchitira chipongwe Mose ndiponso Mulungu.”

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 6:11
28 Mawu Ofanana  

Usatola mbiri yopanda pake; usathandizana naye woipa ndi kukhala mboni yochititsa chiwawa.


Ndipo ansembe ndi aneneri ananena kwa akulu ndi kwa anthu onse, kuti, Munthu uyu ayenera kufa; pakuti wanenera mzinda uwu monga mwamva ndi makutu anu.


Pokhala iye mu Chipata cha Benjamini, kapitao wa alonda anali kumeneko, dzina lake Iriya, mwana wa Selemiya, mwana wa Hananiya; ndipo iye anamgwira Yeremiya mneneri, nati, Ulinkupandukira kwa Ababiloni.


Ndi iye wakuchitira mwano dzina la Yehova, amuphe ndithu; khamu lonse limponye miyala ndithu; mlendo ndi wobadwa m'dziko yemwe akachitira dzina la Yehova mwano, awaphe.


Chifukwa chilamulo chinapatsidwa mwa Mose; chisomo ndi choonadi zinadza mwa Yesu Khristu.


Ndipo izi adzachita, chifukwa sanadziwe Atate, kapena Ine.


Tidziwa ife kuti Mulungu analankhula ndi Mose; koma sitidziwa kumene achokera ameneyo.


Pakuti Mose, kuyambira pa mibadwo yakale ali nao m'mizinda yonse amene amlalikira, akuwerenga mau ake m'masunagoge masabata onse.


Koma pamene iwo, anamkana, nachita mwano, anakutumula malaya ake, nati kwa iwo, Mwazi wanu ukhale pa mitu yanu; ine ndilibe kanthu; kuyambira tsopano ndinka kwa amitundu.


nafuula, Amuna a Israele, tithandizeni; ameneyu ndi munthu uja anaphunzitsa onse ponsepo ponenera anthu, ndi chilamulo, ndi malo ano; ndiponso anatenga Agriki nalowa nao mu Kachisi, nadetsa malo ano oyera.


nampempha kuti mlandu wake wa Paulo uipe, kuti amuitane iye adze ku Yerusalemu; iwo amchitira chifwamba kuti amuphe panjira.


Ndipo m'mene anafika iye, Ayuda adatsikawo ku Yerusalemu anaimirira pomzinga iye, namnenera zifukwa zambiri ndi zazikulu, zimene sanathe kuzitsimikiza;


Ndipo ndinawalanga kawirikawiri m'masunagoge onse, ndi kuwakakamiza anene zamwano; ndipo pakupsa mtima kwakukulu pa iwo ndinawalondalonda ndi kuwatsata ngakhale kufikira kumizinda yakunja.


Ndipo sanathe kuipambana nzeru ndi Mzimu amene analankhula naye.


Ndipo anautsa anthu, ndi akulu, ndi alembi, namfikira, namgwira iye, nadza naye kubwalo la akulu a milandu,


naimika mboni zonama, zakunena, Munthu ameneyo saleka kunenera malo oyera amene, ndi chilamulo;


Ndipo tilekerenji kunena, Tichite zoipa kuti zabwino zikadze (monganso ena atinamiza ndi kuti timanena)? Kulanga kwa amenewo kuli kolungama.


ndingakhale kale ndinali wamwano, ndi wolondalonda, ndi wachipongwe; komatu anandichitira chifundo, popeza ndinazichita wosazindikira, wosakhulupirira;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa