Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




Machitidwe a Atumwi 18:6 - Buku Lopatulika

6 Koma pamene iwo, anamkana, nachita mwano, anakutumula malaya ake, nati kwa iwo, Mwazi wanu ukhale pa mitu yanu; ine ndilibe kanthu; kuyambira tsopano ndinka kwa amitundu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

6 Koma pamene iwo, anamkana, nachita mwano, anakutumula malaya ake, nati kwa iwo, Mwazi wanu ukhale pa mitu yanu; ine ndilibe kanthu; kuyambira tsopano ndinka kwa amitundu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

6 Koma pakuti iwo adaatsutsana naye ndi kumchita chipongwe, Paulo adalekana nawo pakukutumula zovala zake, naŵauza kuti, “Mwadziphetsa ndi mtima wanu. Tsono izo nzanu, ine ndilibe chifukwa. Kuyambira tsopano ndipita kwa akunja.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

6 Koma pamene Ayuda anatsutsana naye ndi kumuchita chipongwe, iye anakutumula zovala zake nati, “Magazi anu akhale pamitu yanu! Ine ndilibe mlandu. Kuyambira tsopano ndipita kwa anthu a mitundu ina.”

Onani mutuwo Koperani




Machitidwe a Atumwi 18:6
37 Mawu Ofanana  

Koma asanafe, Davide adanena naye, Wadziphetsa ndi mtima wako; chifukwa pakamwa pako padachita umboni wakukutsutsa ndi kuti, Ine ndinapha wodzozedwa wa Yehova.


Motero mwazi wao udzabweranso pamutu wake wa Yowabu, ndi pamutu wa mbumba yake, ku nthawi yamuyaya; koma Davide, ndi mbumba yake, ndi banja lake, ndi mpando wake wachifumu adzakhala ndi mtendere wa Yehova ku nthawi yamuyaya.


Ndinakutumulanso malaya anga, ndi kuti, Mulungu akutumule momwemo munthu yense wosasunga mau awa, kunyumba yake, ndi kuntchito yake; inde amkutumule momwemo, namtayire zake zonse. Ndi msonkhano wonse unati, Amen, nalemekeza Yehova. Ndipo anthu anachita monga mwa mau awa.


napereka molira phindu, nalandira choonjezerapo; adzakhala ndi moyo uyu kodi? Sadzakhala ndi moyo, anachita zonyansa izi zonse; kufa adzafadi, mwazi wake umkhalira.


ndipo wina, kumva adamva mau a lipenga, koma osalabadira, likadza lupanga, nilimchotsa, wadziphetsa ndi mtima wake.


Koma mlonda akaona lupanga likudza, osaomba lipenga, osachenjeza anthu, nilidza lupanga, nilichotsa mwa iwo; munthu atengedwadi m'mphulupulu zake, koma mwazi wake ndidzaufunsa padzanja la mlonda.


Pakuti aliyense wakutemberera atate wake kapena mai wake azimupha ndithu; watemberera atate wake kapena amai wake; mwazi wake ukhale pamutu pake.


Ndipo yemwe sadzakulandirani inu kapena kusamva mau anu, pamene mulikutuluka m'nyumbayo, kapena m'mudzimo, sansani fumbi m'mapazi anu.


Iwo ananena kwa Iye, Adzaononga koipa oipawo, nadzapereka mundawo kwa olima ena, amene adzambwezera iye zipatso pa nyengo zake.


Chifukwa chake ndinena kwa inu, Ufumu wa Mulungu udzachotsedwa kwa inu, nudzapatsidwa kwa anthu akupatsa zipatso zake.


Ndipo akapolo ao anatulukira kunjira, nasonkhanitsa onse amene anawapeza, ngakhale oipa, ngakhale abwino; ndipo ukwatiwo unadzala ndi okhala pachakudya.


Ndipo anthu onse anavomereza, ndi kuti, Mwazi wake uli pa ife ndi pa ana athu.


Ndipo ndinena ndi inu, kuti ambiri a kum'mawa ndi a kumadzulo adzafika, nadzakhala pamodzi ndi Abrahamu, ndi Isaki, ndi Yakobo, mu Ufumu wa Kumwamba;


Ndipo zambiri zina anamnenera Iye, namchitira mwano.


Ndipo onse amene sakakulandireni inu, m'mene mutuluka m'mudzi womwewo, sansani fumbi la pa mapazi anu, likhale mboni ya paiwo.


Koma iwo, m'mene adawasansira fumbi la ku mapazi ao anadza ku Ikonio.


Ndipo ndinawalanga kawirikawiri m'masunagoge onse, ndi kuwakakamiza anene zamwano; ndipo pakupsa mtima kwakukulu pa iwo ndinawalondalonda ndi kuwatsata ngakhale kufikira kumizinda yakunja.


komatu kuyambira kwa iwo a mu Damasiko, ndi a mu Yerusalemu, ndi m'dziko lonse la Yudeya, ndi kwa amitundunso ndinalalikira kuti alape, natembenukire kwa Mulungu, ndi kuchita ntchito zoyenera kutembenuka mtima.


Potero, dziwani inu, kuti chipulumutso ichi cha Mulungu chitumidwa kwa amitundu; iwonso adzamva.


Kapena Mulungu ndiye wa Ayuda okhaokha kodi? Si wao wa amitundunso kodi? Eya, wa amitundunso:


Usafulumira kuika manja pa munthu aliyense, kapena usayanjana nazo zoipa za eni; udzisunge wekha woyera mtima.


wolangiza iwo akutsutsana mofatsa; ngati kapena Mulungu awapatse iwo chitembenuziro, kukazindikira choonadi,


Mukatonzedwa pa dzina la Khristu, odala inu; pakuti Mzimu wa ulemerero, ndi Mzimu wa Mulungu apuma pa inu.


m'menemo ayesa nchachilendo kuti simuthamanga nao kufikira kusefukira komwe kwa chitayiko, nakuchitirani mwano;


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa