Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti

- Zotsatsa -




2 Petro 2:12 - Buku Lopatulika

12 Koma awo, ngati zamoyo zopanda nzeru, nyama zobadwa kuti zikodwe ndi kuonongedwa, akuchitira mwano pa zinthu osazidziwa, adzaonongeka m'kuononga kwao,

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

12 Koma awo, ngati zamoyo zopanda nzeru, nyama zobadwa kuti zikodwe ndi kuonongedwa, akuchitira mwano pa zinthu osazidziwa, adzaonongeka m'kuononga kwao,

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

12 Koma anthu aŵa ali ngati nyama chabe, zolengedwa zopanda nzeru, zobadwira kuti zizigwidwa ndi kumaphedwa. Amanyoza mwachipongwe zinthu zosazidziŵa. Ndipo monga nyama zija, iwo omwe adzaonongedwa,

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

12 Koma anthu awa amachita chipongwe zinthu zimene sakuzidziwa. Ali ngati zirombo zopanda nzeru. Zirombo zolengedwa kuti zigwidwe ndi kuwonongedwa, ndipo ngati zirombozo adzawonongedwa.

Onani mutuwo Koperani




2 Petro 2:12
17 Mawu Ofanana  

Pakuti aona anzeru amafa, monga aonongekera wopusa, wodyerera momwemo, nasiyira ena chuma chao.


Munthu wopulukira sachidziwa; ndi munthu wopusa sachizindikira ichi;


Zindikirani, opulukira inu mwa anthu; ndipo opusa inu, mudzachita mwanzeru liti?


Wochimwa adzakankhidwa m'kuipa kwake; koma wolungama akhulupirirabe pomwalira.


Pakuti abusa apulukira, sanafunsire kwa Yehova; chifukwa chake sanapindule; zoweta zao zonse zabalalika.


Koma onse pamodzi apulukira ndi kupusa; mtengo ndiwo chilangizo, chopanda pake.


Koma inu, Yehova, mundidziwa ine; mundiona ine, muyesa mtima wanga ngati utani nanu; muwatulutse iwo monga nkhosa za kuphedwa, ndi kuwakonzeratu tsiku lakuphedwa.


Pakuti anthu anga apusa, sandidziwa Ine; ali ana opulukira sazindikira; ali ochenjera kuchita choipa koma kuchita chabwino sakudziwa.


Ndipo ine ndinati, Ndithu amenewo ali aumphawi; ali opusa; pakuti sadziwa njira ya Yehova, kapena chiweruzo cha Mulungu wao.


Ndipo ndidzakutsanulira mkwiyo wanga, ndidzakuuzira ndi moto wa kuzaza kwanga, ndidzakuperekanso m'manja mwa anthu ankharwe odziwa kuononga.


zakuba, zakupha, zachigololo, masiriro, zoipa, chinyengo, chinyanso, diso loipa, mwano, kudzikuza, kupusa:


Pamenepo anatinso kwa iwo; Ndimuka Ine, ndipo mudzandifuna, ndipo m'tchimo lanu mudzafa: kumene ndimukako Ine, simudziwa kudza inu.


Pakuti wakufesera kwa thupi la iye yekha, chochokera m'thupi adzatuta chivundi; koma wakufesera kwa Mzimu, chochokera mu Mzimu adzatuta moyo wosatha.


(ndizo zonse zakuonongedwa pochita nazo), monga mwa malangizo ndi maphunziro a anthu?


mwa izi adatipatsa malonjezano a mtengo wake ndi aakulu ndithu; kuti mwa izi mukakhale oyanjana nao umulungu wake, mutapulumuka kuchivundi chili padziko lapansi m'chilakolako.


ndi kuwalonjeza ufulu, pamene iwo eni ali akapolo a chivundi; pakuti chimene munthu agonjetsedwa nacho, adzakhala kapolo wa chimenecho.


Koma iwowa zimene sazidziwa azichitira mwano; ndipo zimene azizindikira chibadwire, monga zamoyo zopanda nzeru, mu izi atayika.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa