Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Mateyu 9:3 - Buku Lopatulika

3 Ndipo onani, ena a alembi ananena mumtima mwao, Uyu achitira Mulungu mwano.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

3 Ndipo onani, ena a alembi ananena mumtima mwao, Uyu achitira Mulungu mwano.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

3 Apo aphunzitsi ena a Malamulo adayamba kudzifunsa mumtima mwao kuti, “Munthu ameneyu akuchita chipongwe Mulungu.”

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

3 Pamenepo aphunzitsi ena amalamulo anaganiza mu mtima mwawo kuti, “Munthu uyu akuchitira Mulungu mwano.”

Onani mutuwo Koperani




Mateyu 9:3
13 Mawu Ofanana  

Ndi iye wakuchitira mwano dzina la Yehova, amuphe ndithu; khamu lonse limponye miyala ndithu; mlendo ndi wobadwa m'dziko yemwe akachitira dzina la Yehova mwano, awaphe.


Koma munthu wakuchita kanthu dala, ngakhale wobadwa m'dziko kapena mlendo, yemweyo achitira Yehova mwano; ndipo munthuyo amsadze pakati pa anthu a mtundu wake.


Pomwepo mkulu wa ansembe anang'amba zovala zake, nati, Achitira Mulungu mwano; tifuniranji mboni zina? Onani, tsopano mwamva mwanowo;


pakuti anawaphunzitsa monga mwini mphamvu, wosanga alembi ao.


Mwamva mwano wake; muyesa bwanji? Ndipo onse anamtsutsa Iye kuti ayenera kufa.


Indetu, ndinena ndi inu, Adzakhululukidwa machimo onse a ana a anthu, ndi zamwano zilizonse adzachita mwano nazo;


koma aliyense adzachitira Mzimu Woyera mwano alibe kukhululukidwa nthawi yonse, koma anapalamuladi tchimo losatha;


Pakuti m'kati mwake mwa mitima ya anthu, mutuluka maganizo oipa, zachiwerewere,


Ndipo alembi ndi Afarisi anayamba kuyesayesa mumtima mwao, kuti, Ndani Uyu alankhula zomchitira Mulungu mwano? Ndani angathe kukhululukira machimo, koma Mulungu yekha?


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa