Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 74:18 - Buku Lopatulika

18 Mukumbukire ichi, Yehova, mdaniyo anatonza, ndipo anthu opusa ananyoza dzina lanu.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

18 Mukumbukire ichi, Yehova, mdaniyo anatonza, ndipo anthu opusa ananyoza dzina lanu.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

18 Kumbukirani, Inu Chauta, kuti adani amakunyodolani, kuti anthu achipongwe amanyoza dzina lanu.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

18 Kumbukirani momwe mdani wakunyozerani Inu Yehova, momwe anthu opusa apeputsira dzina lanu.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 74:18
16 Mawu Ofanana  

Kapena Yehova Mulungu wanu adzamva mau onse a kazembeyo, amene anamtuma mfumu ya Asiriya mbuye wake, kuti atonze Mulungu wamoyo, nadzamlanga chifukwa cha mau adawamva Yehova Mulungu wanu; chifukwa chake uwakwezere otsalawo pemphero.


Nanenera Mulungu wa Yerusalemu, monga umo amanenera milungu ya mitundu ya anthu a padziko lapansi, ndiyo ntchito ya manja a anthu.


Yehova, kumbukirani ana a Edomu tsiku la Yerusalemu; amene adati, Gamulani, gamulani, kufikira maziko ake.


Ndipulumutseni kwa zolakwa zanga zonse, musandiike ndikhale chotonza cha wopusa.


Wodala iye amene asamalira wosauka! Tsiku la tsoka Yehova adzampulumutsa.


Nyamukani, Mulungu, mudzinenere mlandu nokha; kumbukirani momwe akutonzani wopusa tsiku lonse.


Yehova, kumbukirani chotigwerachi, penyani nimuone chitonzo chathu.


Koma ndinachichita chifukwa cha dzina langa, kuti lisaipsidwe pamaso pa amitundu amene ndinawatulutsa pamaso pao.


Ndipo pakamwa panu mwadzikuza pa Ine, ndi kundichulukitsira mau anu ndawamva Ine.


Ndikadapanda kuopa mkwiyo wa pa mdani, angayese molakwa outsana nao, anganene, Lakwezeka dzanja lathu, ndipo Yehova sanachite ichi chonse.


Kodi mubwezera Yehova chotero, anthu inu opusa ndi opanda nzeru? Kodi si ndiye Atate wanu, Mbuye wanu; anakulengani, nakukhazikitsani?


Ndipo chimzinda chachikulucho chidagawika patatu, ndi mizinda ya amitundu inagwa; ndipo Babiloni waukulu unakumbukika pamaso pa Mulungu, kuti aupatse chikho cha vinyo waukali wa mkwiyo wake.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa