M'mavesi osiyanasiyana a m'Baibulo, tikulimbikitsidwa kuti tisamachite miseche. Mwachitsanzo, mu bukhu la Aefeso 4:29, limatiuza kuti, "Mawu alionse oipa asatuluke m'kamwa mwanu, koma oti angakhoze kulimbikitsa ena, malinga ndi chifuniro chawo, kuti apereke chisomo kwa iwo akumva."
Mulungu akufuna kuti mawu athu akhale olimbikitsa ndi omanga, osati owononga. Tikamanena miseche, sitikungowononga mbiri ya munthu wina, koma tikuwononganso yathu, chifukwa mawu athu amasonyeza umunthu wathu ndi makhalidwe athu.
Baibulo limatilangizanso kufunika kwa chilungamo ndi choonadi. Mu Levitiko 19:16 limati, "Usamanene miseche pakati pa anthu a mtundu wako; usaime moyo wa mnansi wako: Ine ndine Yehova."
Ndikufuna kukuuzani kuti Baibulo limatiuza kuti tisamale ndi mawu athu ndikupewa miseche. M'malo moipitsa ndi kuwononga mbiri ya ena, tiyenera kukhala anthu olankhula zoona, chilungamo, ndi mawu olimbikitsa.
Motsatira mfundo izi za m'Baibulo, tidzathandiza kumanga dziko lomwe miseche siilipo, komanso lomwe ulemu ndi choonadi zimalamulira. Zikomo.
Musamanenerana, abale. Wonenera mbale, kapena woweruza mbale wake, anenera lamulo, naweruza lamulo: koma ngati uweruza lamulo, suli wochita lamulo, komatu woweruza.
Zilipo zinthu zisanu ndi chimodzi Yehova azida; ngakhale zisanu ndi ziwiri zimnyansa:
Maso akunyada, lilime lonama, ndi manja akupha anthu osachimwa;
mtima woganizira ziwembu zoipa, mapazi akuthamangira mphulupulu m'mangum'mangu;
mboni yonama yonong'ona mabodza, ndi wopikisanitsa abale.
Ndipo ndinena kwa inu, kuti mau onse opanda pake, amene anthu adzalankhula, adzawawerengera mlandu wake tsiku la kuweruza.
ndi kukhala nacho chikumbumtima chabwino, kuti umo akunenerani, iwo akunenera konama mayendedwe anu abwino mu Khristu akachitidwe manyazi.
Wakuneneza mnzake m'tseri ndidzamdula; wa maso odzikuza ndi mtima wodzitama sindidzamlola.
Anthu oneneza anali mwa iwe, kuti akhetse mwazi; ndipo anadya pamapiri mwa iwe, pakati pa iwe anachita zamanyazi.
Pakuti, Iye wofuna kukonda moyo, ndi kuona masiku abwino, aletse lilime lake lisanene choipa, ndi milomo yake isalankhule chinyengo;
Pakuti ndiopa, kuti kaya, pakudza ine, sindidzakupezani inu otere onga ndifuna, ndipo ine ndidzapezedwa ndi inu wotere wonga simufuna; kuti kaya pangakhale chotetana, kaduka, mikwiyo, zilekanitso, maugogodi, ukazitape, zodzikuza, mapokoso;
Nkhani yonse yovunda isatuluke m'kamwa mwanu, koma ngati pali ina yabwino kukumangirira monga mofunika ndiyo, kuti ipatse chisomo kwa iwo akumva.
Pakuti m'kati mwake mwa mitima ya anthu, mutuluka maganizo oipa, zachiwerewere,
zakuba, zakupha, zachigololo, masiriro, zoipa, chinyengo, chinyanso, diso loipa, mwano, kudzikuza, kupusa:
zoipa izi zonse zituluka m'kati, nkudetsa munthu.
Koma tsopano tayani inunso zonsezi: mkwiyo, kupsa mtima, dumbo, mwano, zonyansa zotuluka m'kamwa mwanu:
Momwemonso akazi okalamba akhale nao makhalidwe oyenera anthu oyera, osadierekeza, osakodwa nacho chikondi cha pavinyo, akuphunzitsa zokoma;
Chiwawo chonse, ndi kupsa mtima, ndi mkwiyo, ndi chiwawa, ndi mwano zichotsedwe kwa inu, ndiponso choipa chonse.
Momwemo pakutaya choipa chonse, ndi chinyengo chonse, ndi maonekedwe onyenga, ndi kaduka, ndi masinjiriro onse,
Yehova, ndani adzagonera m'chihema mwanu? Adzagonera ndani m'phiri lanu lopatulika?
Iye wakuyendayo mokwanira, nachita chilungamo, nanena zoonadi mumtima mwake.
Amene sasinjirira ndi lilime lake, nachitira mnzake choipa, ndipo satola miseche pa mnansi wake.
Usamayendayenda nusinjirira mwa anthu a mtundu wako; usamatsata mwazi wa mnansi wako; Ine ndine Yehova.
ndipo mayendedwe anu mwa amitundu akhale okoma, kuti, m'mene akamba za inu ngati ochita zoipa, akalemekeze Mulungu pakuona ntchito zanu zabwino, m'tsiku la kuyang'anira.
Ndipo ndinena kwa inu, kuti mau onse opanda pake, amene anthu adzalankhula, adzawawerengera mlandu wake tsiku la kuweruza.
Pakuti udzayesedwa wolungama ndi mau ako, ndipo ndi mau ako omwe udzatsutsidwa.
anadzala ndi zosalungama zonse, kuipa, kusirira, dumbo; odzala ndi kaduka, mbanda, ndeu, chinyengo, udani;
wakunena za Mwana wake, amene anabadwa, wa mbeu ya Davide, monga mwa thupi,
akazitape, osinjirira, akumuda Mulungu, achipongwe, odzitama, amatukutuku, oyamba zoipa, osamvera akulu ao,
Ndinafuulira kwa Yehova mu msauko wanga, ndipo anandivomereza.
Yehova, landitsani moyo wanga kumilomo ya mabodza, ndi kulilime lonyenga.
Muchenjere naye yense mnansi wake, musakhulupirire yense mbale wake; pakuti abale onse amanyenga, ndipo anansi onse adzayenda ndi maugogodi.
Ndipo yense adzanyenga mnansi wake, osanena choonadi; aphunzitsa lilime lao kunena zonama; nadzithodwetsa kuchita zoipa.
Ukhala pakati pa manyengo m'manyengo; akana kundidziwa, ati Yehova.
ponamizidwa, tipempha; takhala monga zonyansa za dziko lapansi, litsiro la zinthu zonse, kufikira tsopano.
asachitire mwano munthu aliyense, asakhale andeu, akhale aulere, naonetsere chifatso chonse pa anthu onse.
Usatola mbiri yopanda pake; usathandizana naye woipa ndi kukhala mboni yochititsa chiwawa.
Odala muli inu m'mene adzanyazitsa inu, nadzazunza inu, nadzakunenerani monama zoipa zilizonse chifukwa cha Ine.
Pakamwa pako mpochita zochimwa, ndipo lilime lako likonza chinyengo.
Mulungu awalira mu Ziyoni, mokongola mwangwiro.
Ukhala, nuneneza mbale wako; usinjirira mwana wa mai wako.
Ikhale yosalankhula milomo ya mabodza, imene imalankhula mwachipongwe pa olungama mtima, ndi kudzikuza ndi kunyoza.
Yehova, landitsani moyo wanga kumilomo ya mabodza, ndi kulilime lonyenga.
Adzakuninkhanji, adzakuonjezeranji, lilime lonyenga iwe?
Munthu wabwino atulutsa zabwino m'chuma chokoma cha mtima wake; ndi munthu woipa atulutsa zoipa m'choipa chake: pakuti m'kamwa mwake mungolankhula mwa kuchuluka kwa mtima wake.
Ndipo lilime ndilo moto; ngati dziko la chosalungama mwa ziwalo zathu laikika lilime, ndili lodetsa thupi lonse, niliyatsa mayendedwe a chibadwidwe, ndipo liyatsidwa ndi Gehena.
Lilime lako likupanga zoipa; likunga lumo lakuthwa, lakuchita monyenga.
Ukonda choipa koposa chokoma; ndi bodza koposa kunena chilungamo,
ukonda mau onse akuononga, lilime lachinyengo, iwe.
Munthu akati, kuti, Ndikonda Mulungu, nadana naye mbale wake, ali wabodza: pakuti iye wosakonda mbale wake amene wamuona, sangathe kukonda Mulungu amene sanamuone.
Musabwezere munthu aliyense choipa chosinthana ndi choipa. Ganiziranitu zinthu za ulemu pamaso pa anthu onse.
Ngati nkutheka, monga momwe mukhoza, khalani ndi mtendere ndi anthu onse.
Ndipo aphunziraponso kuchita ulesi, aderuderu; koma osati ulesi wokha, komatunso alankhula zopanda pake, nachita mwina ndi mwina, olankhula zosayenera.
Ndinati, Ndidzasunga njira zanga, kuti ndingachimwe ndi lilime langa. Ndidzasunga pakamwa panga ndi cham'kamwa, pokhala woipa ali pamaso panga.
Ngati wina adziyesera ali wopembedza Mulungu, ndiye wosamanga lilime lake, koma adzinyenga mtima wake, kupembedza kwake kwa munthuyu nkopanda pake.
pakuti pakamwa pa woipa ndi pakamwa pa chinyengo pananditsegukira; anandilankhulira ndi m'kamwa mwa bodza.
Ichi chikhale mphotho ya otsutsana nane yowapatsa Yehova, ndi ya iwo akunenera choipa moyo wanga.
Koma Inu, Yehova Ambuye, muchite nane chifukwa cha dzina lanu; ndilanditseni popeza chifundo chanu ndi chabwino.
Pakuti ine ndine wozunzika ndi waumphawi, ndi mtima wanga walaswa m'kati mwanga.
Ndamuka ngati mthunzi womka m'tali; ndiingidwa kwina ndi kwina ngati dzombe.
Mabondo anga agwedezeka chifukwa cha kusala; ndi mnofu wanga waonda posowa mafuta.
Ndiwakhaliranso chotonza; pakundiona apukusa mutu.
Ndithandizeni Yehova, Mulungu wanga: Ndipulumutseni monga mwa chifundo chanu;
kuti adziwe kuti ichi ndi dzanja lanu; kuti Inu Yehova munachichita.
Atemberere iwowa, koma mudalitse ndinu; pakuuka iwowa adzachita manyazi, koma mtumiki wanu adzakondwera.
Otsutsana nane avale manyazi, nadzikute nacho chisokonezo chao ngati ndi chofunda.
Ndipo anandizinga ndi mau a udani, nalimbana nane kopanda chifukwa.
Koma zakutuluka m'kamwa zichokera mumtima; ndizo ziipitsa munthu.
Pakuti mumtima muchokera maganizo oipa, zakupha, zachigololo, zachiwerewere, zakuba, za umboni wonama, zamwano;
Pakamwa pake mposalala ngati mafuta amkaka, koma mumtima mwake munali nkhondo, mau ake ngofewa ngati mafuta oyenga, koma anali malupanga osololasolola.
Mau anu akhale m'chisomo, okoleretsa, kuti mukadziwe inu mayankhidwe anu a kwa yense akatani.
kapena chinyanso, ndi kulankhula zopanda pake, kapena zopusa zimene siziyenera; koma makamaka chiyamiko.
Mbiri yabwino ifunika kopambana chuma chambiri; kukukomera mtima anzako kuposa siliva ndi golide.
Mochokera m'kamwa momwemo mutuluka chiyamiko ndi temberero. Abale anga, izi siziyenera kutero.
Uzikhala kutali ndi mlandu wonama; ndipo usapha munthu wosachimwa ndi wolungama; pakuti sindidzayesa wolungama munthu woipa.
Pakuti si mdani amene ananditonzayo; pakadatero ndikadachilola, amene anadzikuza pa ine sindiye munthu wondida; pakadatero ndikadambisalira:
Koma ameneyo ndiwe, munthu woyenerana nane, tsamwali wanga, wodziwana nane.
Tinapangirana upo wokoma, tinaperekeza khamu la anthu popita kunyumba ya Mulungu.
Mwa ichi, mutataya zonama, lankhulani zoona yense ndi mnzake; pakuti tili ziwalo wina ndi mnzake.
Chifukwa chake zonse zimene mwazinena mumdima zidzamveka poyera; ndipo chimene mwalankhula m'khutu, m'zipinda za m'kati chidzalalikidwa pa matsindwi a nyumba.
M'kamwa mwa wolungama mulankhula nzeru; koma lilime lokhota lidzadulidwa.
Milomo ya wolungama idziwa zokondweretsa; koma m'kamwa mwa oipa munena zokhota.
Chidzudzulo chomveka chiposa chikondi chobisika.
Kulasa kwa bwenzi kuli kokhulupirika; koma mdani apsompsona kawirikawiri.
Wakuda mnzake amanyenga ndi milomo yake; koma akundika chinyengo m'kati mwake.
Pamene akometsa mau ake usamkhulupirire; pakuti m'mtima mwake muli zonyansa zisanu ndi ziwiri.
Angakhale abisa udani wake pochenjera, koma udyo wake udzavumbulutsidwa posonkhana anthu.
Inde, anakonda kutemberera, ndipo kudamdzera mwini; sanakondwere nako kudalitsa, ndipo kudamkhalira kutali.
Anavalanso temberero ngati malaya, ndipo lidamlowa m'kati mwake ngati madzi, ndi ngati mafuta m'mafupa ake.
Koma manenedwe anu akhale, Inde, inde; Iai, iai; ndipo choonjezedwa pa izo chichokera kwa woipayo.
Ndipo ndikudandaulirani, abale, yang'anirani iwo akuchita zopatutsana ndi zophunthwitsa, kosalingana ndi chiphunzitsocho munachiphunzira inu; ndipo potolokani pa iwo.
Pakuti otere satumikira Ambuye wathu Khristu, koma mimba yao; ndipo ndi mau osalaza ndi osyasyalika asocheretsa mitima ya osalakwa.
Yehova adzadula milomo yonse yothyasika, lilime lakudzitamandira;
amene amati, Ndi lilime lathu tidzaposa; milomo yathu nja ife eni; mbuye wa pa ife ndani?
Munthu wopanda pake, mwamuna wamphulupulu; amayenda ndi m'kamwa mokhota.
Amatsinzinira ndi maso ake, napalasira ndi mapazi ake, amalankhula ndi zala zake;
zopotoka zili m'mtima mwake, amaganizira zoipa osaleka; amapikisanitsa anthu.
Chifukwa chake tsoka lake lidzadza modzidzimuka; adzasweka msangamsanga, palibe chompulumutsa.
Pakuti asamve zowawa wina wa inu ngati wambanda, kapena mbala, kapena wochita zoipa, kapena ngati wodudukira;
M'kamwa mwake mwadzala kutemberera ndi manyengo ndi kuchenjerera; pansi pa lilime lake pali chivutitso chopanda pake.
Mtima wa wolungama uganizira za mayankhidwe; koma m'kamwa mwa ochimwa mutsanulira zoipa.
Musandikoke kundichotsa pamodzi ndi oipa, ndi ochita zopanda pake; amene alankhula zamtendere ndi anansi ao, koma mumtima mwao muli choipa.
Chifukwa chake zinthu zilizonse mukafuna kuti anthu achitire inu, inunso muwachitire iwo zotero; pakuti icho ndicho chilamulo ndi aneneri.
Akubadwa inu a njoka, mungathe bwanji kulankhula zabwino, inu akukhala oipa? Pakuti m'kamwa mungolankhula mwa kusefuka kwake kwa mtima.
Chifukwa chake uli wopanda mau owiringula, munthu iwe, amene uli yense wakuweruza; pakuti m'mene uweruza wina, momwemo udzitsutsa iwe wekha, pakuti iwe wakuweruza, umachita zomwezo.
Koma nzeru yochokera kumwamba iyamba kukhala yoyera, nikhalanso yamtendere, yaulere, yomvera bwino, yodzala chifundo ndi zipatso zabwino, yopanda tsankho, yosadzikometsera pamaso.
Ndipo chipatso cha chilungamo chifesedwa mumtendere kwa iwo akuchita mtendere.
Taonani, ali m'chikuta cha zopanda pake; anaima ndi chovuta, nabala bodza.
Anachita dzenje, nalikumba, nagwa m'mbuna yomwe anaikumba.
Chovuta chake chidzambwerera mwini, ndi chiwawa chake chidzamgwera pakati pamutu pake.
Usalole m'kamwa mwako muchimwitse thupi lako; usanene pamaso pa mthenga kuti, Ndinaphophonya; Mulungu akwiyire mau ako chifukwa ninji, naononge ntchito ya manja ako?
Potero Mulungu adzakupasula kunthawi zonse, adzakuchotsa nadzakukwatula m'hema mwako, nadzakuzula, kukuchotsa m'dziko la amoyo.
Monga woyaluka woponya nsakali, mivi, ndi imfa,
momwemo wonyenga mnzake ndi kuti, ndi kusewera kumeneku.
Ndipo aliyense amene adzanenera Mwana wa Munthu zoipa adzakhululukidwa; koma amene anenera Mzimu Woyera zamwano sadzakhululukidwa.
M'maso mwake munthu woonongeka anyozeka; koma awachitira ulemu akuopa Yehova. Atalumbira kwa tsoka lake, sasintha ai.