Masalimo 120 - Buku LopatulikaApempha Mulungu amlanditse pa omnamiza Nyimbo yokwerera. 1 Ndinafuulira kwa Yehova mu msauko wanga, ndipo anandivomereza. 2 Yehova, landitsani moyo wanga kumilomo ya mabodza, ndi kulilime lonyenga. 3 Adzakuninkhanji, adzakuonjezeranji, lilime lonyenga iwe? 4 Mivi yakuthwa ya chiphona, ndi makala tsanya. 5 Tsoka ine, kuti ndili mlendo mu Meseki, kuti ndigonera m'mahema a Kedara! 6 Moyo wanga unakhalitsa nthawi pamodzi ndi iye wakudana nao mtendere. 7 Ine ndikuti, Mtendere; koma polankhula ine, iwowa akuti, Nkhondo. |
Bible Society of Malawi
Bible Society of Malawi