Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 120:5 - Buku Lopatulika

5 Tsoka ine, kuti ndili mlendo mu Meseki, kuti ndigonera m'mahema a Kedara!

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

5 Tsoka ine, kuti ndili mlendo m'Meseki, kuti ndigonera m'mahema a Kedara!

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

5 Ndili ndi tsoka lalikulu, chifukwa ndimakhala pakati pa anthu onga mbuli za ku Meseki ndi Kedara.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

5 Tsoka ine kuti ndimakhala ku Mesaki, kuti ndimakhala pakati pa matenti a ku Kedara!

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 120:5
16 Mawu Ofanana  

Ana aamuna a Yafeti: Gomeri, ndi Magogi, ndi Madai, ndi Yavani, ndi Tubala, ndi Meseki ndi Tirasi.


ndipo maina a ana a Ismaele, maina ao m'mibadwo yao ndi awa: woyamba wa Ismaele ndi Nebayoti; ndi Kedara, ndi Adibeele, ndi Mibisamu,


Wakuda ine, koma wokongola, ana aakazinu a ku Yerusalemu, ngati mahema a Kedara, ngati nsalu zotchinga za Solomoni.


Kalanga ine, amai, pakuti mwandibala ine munthu wandeu, munthu wakutetana nalo dziko lonse lapansi! Sindinakongoletsa paphindu, anthu sanandikongoletse paphindu; koma iwo onse anditemberera.


Ukhala pakati pa manyengo m'manyengo; akana kundidziwa, ati Yehova.


Yavani, Tubala, Meseki, anagulana nawe malonda; ndi anthu amoyo ndi zotengera zamkuwa anagulana nawe malonda.


Arabiya ndi akalonga onse a ku Kedara anazolowerana nao malonda ako; anaankhosa, nkhosa zamphongo, ndi mbuzi, izi anagulana nawe.


Ndipo iwe, wobadwa ndi munthu, nenera motsutsana naye Gogi, uziti, Atero Ambuye Yehova, Taona, nditsutsana nawe Gogi, iwe mfumu yaikulu ya Meseki ndi Tubala;


Ndidziwa kumene ukhalako kuja kuli mpando wachifumu wa Satana; ndipo ugwira dzina langa, osakaniza chikhulupiriro changa, angakhale m'masiku a Antipa, mboni yanga, wokhulupirika wanga, amene anaphedwa pali inu, kuja akhalako Satana.


Ndipo Samuele anamwalira; ndi Aisraele onse anaunjikana pamodzi nalira maliro ake, namuika m'nyumba yake ku Rama. Davide ananyamuka, natsikira ku chipululu cha Parani.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa