Biblia Todo Logo
Baibulo la pa intaneti
- Zotsatsa -




Masalimo 120:4 - Buku Lopatulika

4 Mivi yakuthwa ya chiphona, ndi makala tsanya.

Onani mutuwo Koperani

Chichewa Buku Lopatulika Bible 2014

4 Mivi yakuthwa ya chiphona, ndi makala tsanya.

Onani mutuwo Koperani

Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

4 Adzakuzunzani ndi mivi yakuthwa ya munthu wankhondo, pamodzi ndi makala amoto a mtengo wa tsanya.

Onani mutuwo Koperani

Mawu a Mulungu mu Chichewa Chalero

4 Adzakulangani ndi mivi yakuthwa ya munthu wankhondo, ndi makala oyaka a mtengo wa tsanya.

Onani mutuwo Koperani




Masalimo 120:4
19 Mawu Ofanana  

Mivi yanu njakuthwa; mitundu ya anthu igwa pansi pa inu; iwalasa mumtima adani a mfumu.


Potero Mulungu adzakupasula kunthawi zonse, adzakuchotsa nadzakukwatula m'hema mwako, nadzakuzula, kukuchotsa m'dziko la amoyo.


Moyo wanga uli pakati pa mikango; ndigona pakati pa oyaka moto, ndiwo ana a anthu amene mano ao ali nthungo ndi mivi, ndipo lilime lao ndilo lupanga lakuthwa.


Onani abwetuka pakamwa pao; m'milomo mwao muli lupanga, pakuti amati, Amva ndani?


Ndipo anamkonzera zida za imfa; mivi yake aipanga ikhale yansakali.


Wopeputsa mnzake asowa nzeru; koma wozindikira amatonthola.


Woipa alandira malipiro onyenga; koma wofesa chilungamo aonadi mphotho.


Wonyoza Mulungu aononga mnzake ndi m'kamwa mwake; koma olungama adzapulumuka pakudziwa.


Milomo yonama inyansa Yehova; koma ochita ntheradi amsekeretsa.


Munthu wopanda pake akonzeratu zoipa; ndipo m'milomo mwake muli moto wopsereza.


Lilime lili ndi mphamvu pa imfa ndi moyo; wolikonda adzadya zipatso zake.


Mau akazitape akunga zakudya zolongosoka, zotsikira m'kati mwa mimba.


Mboni yonama sidzakhala yosalangidwa; wolankhula mabodza sadzapulumuka.


Mboni yonama sidzapulumuka chilango; wolankhula mabodza adzaonongeka.


Chifukwa chake atero Yehova wa makamu, Taonani, ndidzawasungunula, ndi kuwayesa, pakuti ndidzachitanji, chifukwa cha mwana wamkazi wa anthu anga?


Koma amantha, ndi osakhulupirira, ndi onyansa, ndi ambanda, ndi achigololo, ndi olambira mafano, ndi onse a mabodza, cholandira chao chidzakhala m'nyanja yotentha ndi moto ndi sulufure; ndiyo imfa yachiwiri.


Titsatireni:

Zotsatsa


Zotsatsa